Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Seŵenzetsani Nkhani Zongocitika Kumene mu Ulaliki

Seŵenzetsani Nkhani Zongocitika Kumene mu Ulaliki

Pa utumiki wake, Yesu anaseŵenzetsa nkhani zongocitika kumene pophunzitsa anthu. (Luka 13:1-5) Inunso mungaseŵenzetse nkhani zongocitika kumene pothandiza anthu kucita cidwi na uthenga wa Ufumu. Pambuyo pofotokoza za kukwela mtengo kwa zinthu, tsoka la zacilengedwe, zacipolowe, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo, kapena nkhani zina zotelo, funsani funso lopangitsa munthu kuganiza. Mungafunse kuti: “Kodi muganiza kuti mavuto monga . . . adzatha?” kapena “Kodi muona kuti n’ciyani cingathetse vuto la . . . ?” Kenako muŵelengeleni vesi ya m’Baibo yogwilizana na nkhaniyo. Ngati munthuyo waonetsa cidwi, muonetseni vidiyo kapena mugaŵileni cofalitsa ca mu Thuboksi yathu. Pamene tikuyesetsa kuwafika pamtima anthu m’gawo lathu, ‘tizicita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino.’—1 Akor. 9:22, 23.

Ni nkhani ziti zimene zingakope cidwi ca anthu m’gawo lanu?