November 1-7
YOSWA 18-19
Nyimbo 12 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Analigaŵa Mwanzelu Dziko la Kanani”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Yos. 18:1-3—Kodi n’ciani mwina cimene cinapangitsa kuti Aisiraeli acedwe kukakhala m’dela la kumadzulo kwa Yorodano? (it-1 359 ¶5)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Yos. 18:1-14 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Kukambilana.Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Uthenga Wabwino—Sal. 37:10, 11. Nthawi iliyonse vidiyo ikaima, na imwe iimitseni na kufunsa omvetsela mafunso amene aonekela mu vidiyo.
Ulendo Woyamba: (Mph. 4) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako gaŵilani Nsanja ya Mlonda ya Na. 2 2021. (th phunzilo 1)
Ulendo Woyamba: (Mph. 4) Mukayamba na makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki, koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 11)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Timayamika Yehova Cifukwa ca Cikondi Canu”: (Mph. 15) Nkhani yokambilana, yokambidwa na mkulu. Onetsani vidiyo yakuti “Timayamika Mulungu Nthawi Zonse Cifukwa ca Inu”. Fotokozankoni mfundo imodzi kapena ziŵili zocititsa cidwi zocokela m’nkhani za pa jw.org, za mutu wakuti “Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito.”
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 62
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 23 na Pemphelo