Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muzidalila Yehova Pamene Mukuvutitsidwa

Muzidalila Yehova Pamene Mukuvutitsidwa

Anthu ovutitsa anzawo angacite zinthu zimene zingativulaze, komanso kutipweteka mtima. Angacititsenso kuti ubwenzi wathu na Yehova uwonongeke ngati ticita mantha pamene akutsutsa kulambila kwathu. Kodi mungadziteteze bwanji kwa anthu ovutitsa anzawo?

Alambili a Yehova ambili, akwanitsa kuthana na ovutitsa anzawo mwa kudalila Yehova. (Sal. 18:17) Mwacitsanzo, Esitere molimba mtima anaulula ciwembu ca munthu wankhanza dzina lake Hamani. (Esitere 7:​1-6) Asanacite zimenezo, iye anaonetsa kudalila Yehova mwa kusala kudya. (Esitere 4:​14-16) Yehova anam’dalitsa Esitere pa zimene anacita mwa kumuteteza pamodzi na anthu ake.

Inu acicepele, ngati mumavutitsidwa, pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Komanso uzan’koni munthu wina wacikulile monga makolo anu za vuto lanulo. Khalani wotsimikiza kuti nanunso Yehova adzakuthandizani mmene anathandizila Esitere. N’ciyani cina cingakuthandizeni ngati mumavutitsidwa?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI UMOYO WANGA NILI WACICEPELE—KODI KUVUTITSIDWA MUNGATHANE NAKO BWANJI? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi acinyamata angaphunzilepo ciyani pa citsanzo ca Charlie na Ferin?

  • Kodi makolo angaphunzilepo ciyani pa zimene Charlie na Ferin anakamba pankhani yothandiza ana kuthana na munthu wowavutitsa?