Nkhani 49
Dzuŵa Liimilila
“WAMUONA Yoswa? Uganiza acita ciani?” Afuula kuti: ‘Dzuŵa, imilila!’ Ndipo dzuŵa liimilila. Liimilila conco pakati pa mutu tsiku lonse. Yehova ndiye wacititsa zimenezi. Tiye tione cifukwa cimene Yoswa afunila kuti dzuŵa lisaloŵe.
Pamene mafumu oipa aja 5 aku Kanani ayamba kumenyana ndi Agibeoni, Agibeoni atuma munthu kwa Yoswa kuti awathandize. Iwo apempha kuti: ‘Bwelani kuno mwamsanga! Mutipulumutse! Mafumu onse amene akhala kudela la kumapili abwela kudzacita nkhondo ndi akapolo anu.’
Msanga-msanga Yoswa ndi amuna ake ankhondo anyamuka. Ndipo ayenda usiku wonse. Pamene afika ku Gibeoni, asilikali a mafumu 5 acita mantha ndi kuyamba kuthaŵa. Pamenepo Yehova agwetsa vimatalala vikulu-vikulu kucokela kumwamba, ndipo vikupha asilikali ambili kuposa amene aphedwa ndi asilikali a Yoswa.
Yoswa aona kuti dzuŵa likaloŵa kudzakhala mdima, ndipo asilikali a mafumu oipa aja adzathaŵa. Ndiye cifukwa cake apemphela kwa Yehova kuti: ‘Dzuŵa, liimilile!’ Pamene dzuŵa liloŵa, Aisiraeli akwanitsa kupha asilikali onse ndi kuwina nkhondo.
Mu dziko la Kanani mukali mafumu oipa ambili amene amazonda anthu a Mulungu. Yoswa ndi asilikali ake atenga zaka 6 kuti agonjetse mafumu 31 amenewa. Pambuyo pa zimenezi, Yoswa agaŵa dziko la Kanani kuti mafuko amene alibe malo akhale ndi malo ao-ao.
Zaka zambili zapitapo tsopano, ndipo Yoswa akufa ali ndi zaka 110. Pamene iye ndi anzake ali moyo, anthu akhala akumvela Yehova. Koma pambuyo pakuti anthu abwino amenewa afa, anthu ayamba kucita zinthu zoipa, cakuti agwela m’mavuto akulu. Apa m’pamene io afunikila kwambili thandizo la Mulungu.
Yoswa 10:6-15; 12:7-24; 14:1-5; Oweruza 2:8-13.