Gao 7
Kucokela Pamene Yesu Anaukitsidwa, Kukafika Pamene Paulo Anamangidwa
Yesu anaukitsidwa patsiku lacitatu kucokela pamene anamwalila. Pa tsiku limeneli anaonekela kasanu kwa otsatila ake. Yesu anapitiliza kuonekela kwa io kwa masiku 40. Tsiku lina, pamene ophunzila ake anali kuona, Yesu ananyamuka ndi kukwela kumwamba. Pambuyo pamasiku 10, Mulungu anatumiza mzimu woyela kwa otsatila a Yesu amene anali kuyembekezela ku Yerusalemu.
Panthawi ina, adani a Mulungu anapoyna atumwi m’ndende, koma mngelo anawamasula. Wophunzila Stefano anaphedwa mwa kuponyedwa miyala ndi anthu otsutsa Cikristu. Koma tidzaphunzila mmene Yesu anasankhila mmodzi wa otsutsa amenewa kukhala wophunzila wake wapadela, ndipo anadzakhala mtumwi Paulo. Ndiyeno patapita zaka zitatu ndi hafu kucokela pa imfa ya Yesu, Mulungu anatuma mtumwi Petulo kuti akalalikile kwa Koneliyo ndi banja lake, amene sanali Ayuda.
Patapita zaka pafupi-fupi 13, Paulo ananyamuka paulendo wake woyamba wokalalikila. Paulendo wake waciŵili, Paulo anayenda ndi Timoteyo. Tidzaphunzila mmene Paulo ndi anzake amene anali kuyenda nao anakhalila, ndi nthawi yosangalatsa potumikila Mulungu. Pamapeto pake, Paulo anaponyedwa m’ndende ku Roma. Patapita zaka ziŵili anam’masula, koma anam’ponyanso m’ndende ndi kumupha. Zocitika za mu GAO 7 zinacitika panyengo yazaka pafupi-fupi 32.