Nkhani 112
Boti Iwonongeka Pacisumbu
ONA boti pacithunzi-thunzi apa yacita ngozi ndipo yaonongeka! Kodi waaona anthu amene alumphila m’madzi? Ena afika kale kumtunda. Kodi uyu amene aoneka apa ni Paulo? Tiye tione zimene zamucitikila.
Kumbukila kuti Paulo anaikidwa m’ndende ku Kaisareya kwa zaka ziŵili. Ndiyeno Paulo ndi akaidi ena aikidwa mu boti ndi kuyamba ulendo woyenda ku Roma. Pamene apita pafupi ndi cisumbu ca Kerete, cimphepo camphamvu ciyamba kuomba boti yao. Cimphepo ciomba ndi mphamvu kwambili cakuti oyendetsa botiyo alephela kuiyendetsa bwino. Ndipo io sakhoza kuona dzuŵa usana kapena nyenyezi usiku. Pambuyo pa masiku ambili, onse amene ali mu boti alibenso ciyembekezo cakuti adzapulumuka.
Ndiyeno Paulo anyamuka ndi kukamba kuti: ‘Palibe ngakhale mmodzi wa ife amene adzafa; boti cabe ni imene idzaonongeka. Usiku wapita mngelo wa Mulungu anabwela kwa ine ndipo anandiuza kuti, “Usaope Paulo! Uyenela kuima pamaso pa Kaisara, wolamulila waciroma. Ndipo Mulungu adzapulumutsa onse amene uli nao paulendowu.”’
Patapita masiku 14 kucokela pamene cimphepo cinayamba kuomba, pakati pausiku oyendetsa boti aona kuti madzi acepela-cepela! Poopa kuti angagunde miyala mu mdima, aponya m’madzi zoimitsila boti zochedwa anangula. Ndipo m’mawa mwake aona doko. Conco aganiza zakuti apeleke boti yao kumtunda kumeneko.
Komabe, pamene afika pafupi ndi mtunda, boti igunda pamcenga ndipo iima pamenepo. Ndiyeno mafunde ayamba kugunda boti mwamphamvu cakuti iyamba kuphwanyika. Msilikali amene awayang’anila akuti: ‘Coyamba, inu nonse amene munganyaye lumphilani m’madzi, ndipo munyaye kupita kumtunda. Ndiyeno inu nonse otsala muwatsatile, ndipo mutenge zidutswa zocoka ku boti kuti muyandamepo.’ Iwo acita zimenezo, ndipo mwa njila imeneyi anthu onse 276 anali mu boti apulumuka monga mmene mngelo analonjezela.
Cisumbu cimeneci cichedwa kuti Melita. Anthu a pacisumbuci ni okoma mtima kwambili, ndipo asamalila onse amene anali mu boti. Pamene cimphepo cileka kuomba, Paulo aikidwa mu boti ina, ndipo ayenda naye ku Roma.
Machitidwe 27:1-44; 28:1-14.