Gao 2
Kucokela pa Cigumula Kukafika Pamene Aisiraeli Anamasulidwa ku Iguputo
Anthu 8 cabe ni amene anapulumuka Cigumula camadzi, koma m’kupita kwa nthawi, anthu amenewo anaculuka kufika m’masauzande ambili. Ndiyeno, patapita zaka 352 kucokela pa Cigumula, Abulahamu anabadwa. Timaphunzila za mmene Mulungu anasungila lonjezo lake kwa Abulahamu mwa kum’patsa mwana mwamuna, dzina lake Isaki. Pamene Isaki anakula anabala ana amuna aŵili, koma Mulungu anasankhapo mmodzi, Yakobo.
Yakobo anakhala ndi banja lalikulu. Anali ndi ana amuna okwana 12, ndi ana ena akazi. Ana amuna a Yakobo okwana 10 anali kuzonda mng’ono wao Yosefe, cakuti anamugulitsa muukapolo ku Iguputo. Pambuyo pake, Yosefe anakhala wolamulila wamphamvu ku Iguputo. Pamene kunakhala njala yaikulu, Yosefe anawayesa abale ake kuti aone ngati anasintha mitima yao. Potsilizila pake, banja lonse la Yakobo, kutanthauza Aisiraeli onse, anasamukila ku Iguputo. Zimenezi zinacitika patapita zaka 290 kucokela pamene Abulahamu anabadwa.
Aisiraeli anakhala ku Iguputo kuja kwa zaka 215. Koma Yosefe atafa, ana a Isiraeli anakhala akapolo kumeneko. M’kupita kwa nthawi, Mose anabadwa, ndipo Mulungu anam’gwilitsila nchito kulanditsa ana a Isiraeli mu ukapolo ku Iguputo. Mbili yonse ya zocitika za mu Gao 2 inatenga zaka zokwanila 857.