Nkhani 18
Yakobo Ayenda Ku Harana
KODI amuna amene Yakobo akamba nao pacithunzi-thunzi apa, waŵadziŵa? Pambuyo poyenda masiku ambili, Yakobo anakumana ndi amunawa pacitsime. Iwo anali kulisha mbelele zao. Yakobo anawafunsa kuti: ‘Kodi mwacokela kuti?’
Iwo anayankha kuti: ‘Tacokela ku Harana.’
Yakobo anawafunsanso kuti: ‘Kodi mumudziŵa Labani?’
Iwo anayankha kuti: ‘Inde. Si uyo mwana wake Rakele abwela apo ndi nkhosa.’ Kodi wamuona Rakele amene abwela apo?
Pamene Yakobo anaona Rakele ali ndi nkhosa za Labani amalume ake, anayenda kukacotsa mwala pacitsime kuti nkhosa zimwe madzi. Pamenepo Yakobo anapsompsona Rakele ndipo anadzidziŵikitsa kwa iye. Rakele anakondwela kwambili, ndipo anayenda kunyumba kukauza atate ake a Labani.
Labani anakondwela kwambili kuti Yakobo adzakhala nao. Ndipo pamene Yakobo ananena zakuti afuna kukwatila Rakele, Labani anakondwela kwambili. Koma anapempha Yakobo kuti aseŵenze m’munda wake kwa zaka 7 kuti akwatile Rakele. Yakobo anacita zimenezi cifukwa anamukonda kwambili Rakele. Koma pamene nthawi ya cikwati inafika, kodi udziŵa cimene cinacitika?
Labani anapeleka Leya, mwana wake mkulu kwa Yakobo mu malo mwa Rakele. Pamene Yakobo anavomela kuseŵenzela Labani zaka zina 7, ni pamene anamupatsanso Rakele kukhala mkazi wake. Panthawi imeneyo, Mulungu anali kuvomeleza amuna kukhala ndi akazi ambili. Koma, malinga ndi mmene Baibo imakambila, mwamuna ayenela kukhala ndi mkazi mmodzi cabe.
Genesis 29:1-30.