Nkhani 10
Cigumula Cacikulu
ANTHU amene anali kunja kwa cingalawa, anapitiliza ndi moyo wao wa nthawi zonse. Iwo sanakhulupilile kuti Cigumula cidzabwela, ndipo anapitiliza kuseka. Koma posapita nthawi analeka kuseka.
Mwadzidzidzi mvula inayamba kugwa. Ndipo inali kuti poo ngati kuti munthu akhuthula madzi a m’dalamu. Nowa anakamba zoona! Koma tsopano nthawi inapita yakuti munthu wina aliyense aloŵe m’cingalawa. Yehova anakhoma citseko ca cingalawa.
Posapita nthawi, nthaka yonse kusiyapo mapili inambila m’madzi. Madzi anaculuka ndipo anasefukila ngati mitsinje ikulu-ikulu. Anakokolola mitengo ndi kugubuduza miyala ikulu-ikulu. Mkokomo wa madzi unali kumveka kuti woo kulikonse! Anthu anacita mantha ndipo anakwela m’mapili. Anayamba kuganiza kuti sembe anamvela Nowa ndi kuloŵa m’cingalawa pamene citseko cinali cotseguka! Koma anacedwa kale.
Madzi anapitilizabe kuculuka. Mvula inali kugwa usana ndi usiku kwa masiku 40. Pang’ono-pang’ono, madzi anakwela m’mbali mwa mapili, ndipo posapita nthawi ngakhale mapili atali kwambili anambila. Conco, monga mmene Mulungu anakambila, anthu onse ndi zinyama zonse zimene zinali kunja kwa cingalawa zinafa. Koma onse amene anali mkati mwa cingalawa anapulumuka.
Nowa ndi ana ake anacita nchito yabwino kupanga cingalawa. Madzi anacinyamula ndipo cinayandama pamwamba pa madzi. Ndiyeno tsiku lina pamene mvula inaleka kugwa, dzuŵa linayamba kuwala. Kunali kuoneka mocititsa cidwi! Dziko lonse linali nyanja cabe. Cingalawa cabe n’cimene cinali kuonekela pamwamba pa madzi.
Vimphona vonse tsopano kunalibe, ndipo sivikanavulazanso anthu. Vonse vinaonongedwa pamodzi ndi amai ao ndi anthu onse oipa. Nanga n’ciani cinacitika kwa atate a vimphona vimenevi?
Iwo sanali anthu monga ife. Anali angelo amene anacoka kumwamba kudzakhala padziko lapansi monga anthu. Conco, pamene cigumula cinacitika, angelo amenewa sanaonongedwe pamodzi ndi anthu onse. Iwo anavula matupi aumunthu amene anapanga, ndipo anabwelela kumwamba monga angelo. Koma sanaloledwe kukhala mbali ya banja la angelo a Mulungu. Conco anakhala angelo a Satana. Angelo amenewa m’Baibo amachedwa viŵanda.
Mulungu anapangitsa mphepo kuomba padziko lapansi, ndipo madzi a cigumula anayamba kucepa. Patapita miyezi 5, cingalawa cinakhala pamwamba pa phili. Masiku ambili anapita, ndipo anthu amene anali m’cingalawa anali kusonjola kunja, ndipo anayamba kuona nsonga za mapili. Madzi anapitiliza kucepela-cepela.
Potsilizila pake, Nowa anatulutsa m’cingalawa mbalame yakuda yochedwa khwangwala. Mbalame imeneyi inali kuuluka kwa kanthawi ndiyeno inali kubwelelanso, cifukwa siinali kupeza malo okhalapo. Inapitiliza kucita conco, ndipo nthawi iliyonse ikabwelela inali kukhala pa cingalawa.
Nowa anali kufuna kudziŵa ngati madzi asililatu panthaka, conco anatulutsa njiŵa. Koma njiŵa nayo inabwelela cifukwa sinapeze malo okhalapo. Nowa anaitumizanso kaciŵili. Apa tsopano inabwela ndi tsamba la mtengo wa maolivi kukamwa kwake. Conco Nowa anadziŵa kuti madzi acepa. Nowa anatumiza njiŵa kacitatu, ndipo njiŵayo potsilizila pake inapeza malo ouma okhala.
Mulungu tsopano anakamba ndi Nowa, ndipo anati: ‘Tuluka m’cingalawa. Tenga banja lako lonse ndi nyama zonse.’ Iwo anali atakhala m’cingalawa kupitilila caka cimodzi. Conco anasangalala kwambili kuti anatuluka m’cingalawa ndi kuti anali amoyo!
Genesis 7:10-24; 8:1-17; 1 Petulo 3:19, 20.