Nkhani 8
Vimphona Padziko Lapansi
NGATI waona munthu mutali wofika pamtenje wa nyumba abwela kwa iwe, kodi ungaganize ciani? Munthu ameneyo angakhale cimphona! Panthawi ina padziko lapansi panali vimphona. Baibo imakamba kuti Atate a vimphona vimenevi anali angelo amene anacokela kumwamba. Koma kodi zimenezi zinacitika bwanji?
Kumbukila kuti mngelo woipa, Satana, anali kupangitsa anthu kucita vinthu voipa. Anali kuyesa kunyengelela ngakhale angelo a Mulungu kuti nao azicita vinthu voipa. M’kupita kwa nthawi, ena mwa angelo amenewa anayamba kumvela Satana. Iwo anasiya nchito imene Mulungu anawapatsa kumwamba. Anabwela pano padziko lapansi ndi kuvala matupi aumunthu. Kodi udziŵa cimene anacitila zimenezi?
Baibo imakamba kuti, ana a Mulungu amenewa anakhumbila akazi okongola pano padziko lapansi, ndipo anafuna kuti azikhala nao. Conco anabwela padziko lapansi ndi kukwatila akazi amenewa. Baibo imakamba kuti cimene angelo awa anacita cinali cinthu coipa kwambili, cifukwa Mulungu anapanga angelo kuti azikhala kumwamba.
Pamene angelo ndi akazi ao anayamba kubala ana, ana ao anali kuoneka osiyana. Mwina poyamba sanali kuoneka osiyana kwambili ndi ana ena. Koma io anali kukulila-kulila ndi kukhala amphamvu kwambili, mpaka anakhala vimphona.
Vimphona vimenevi vinali voipa kwambili. Cifukwa cakuti vinali vikulu-vikulu ndiponso vamphamvu kwambili, vinali kuvutitsa ndi kuvulaza anthu. Vinali kukakamiza anthu kuti akhale oipa monga mmene vinalili.
Panthawi imeneyi Inoki anali anamwalila kale. Koma panali munthu wina wabwino padziko lapansi. Munthu ameneyu dzina lake anali Nowa. Nthawi zonse iye anali kucita zimene Mulungu anali kumuuza.
Tsiku lina Mulungu anauza Nowa kuti nthawi yakuti iye aononge anthu onse oipa yafika. Koma Mulungu anakamba kuti adzapulumutsa Nowa, banja lake, ndi nyama zambili zosiyana-siyana. Tiye tione mmene Mulungu anacitila zimenezi.
Genesis 6:1-8; Yuda 6.