Nkhani 95
Mmene Yesu Amaphunzitsila
TSIKU lina Yesu auza munthu wina kuti ayenela kukonda mnzake. Ndipo munthuyu afunsa Yesu kuti: ‘Kodi mnzanga ndani?’ Yesu adziŵa zimene munthuyu aganiza. Iye aganiza kuti anthu a fuko lake ndi acipembedzo cake cabe ndiye anzake. Tiye tione zimene Yesu auza munthu ameneyu.
Nthawi zina Yesu amaphunzitsa mwa kugwitsila nchito mafanizo. Ndipo izi n’zimene acita apa. Iye akamba fanizo lonena za Myuda ndi Msamariya. Tinaphunzila kale kuti Ayuda ambili sanali kukonda Asamariya. Tsopano, si ili fanizo la Yesu:
Tsiku lina munthu wina, Myuda, anali kuyenda mu mseu wa m’mapili kupita ku Yeriko. Iye anakumana ndi acifwamba amene anamutengela ndalama ndi kumumenya kwambili ndi kumusiya ali pafupi kufa.
Pambuyo pa zimenezi, wansembe waciyuda anali kuyenda mu mseu umenewu. Iye anamuona munthu womenyedwayu, koma kodi uganiza kuti anacita bwanji? Anangomulambalala ndi kupitiliza kuyenda. Ndiyeno munthu winanso wopembedza kwambili anabwela. Iye anali Mlevi. Koma kodi anaima? Iyai, nayenso sanaime kuti athandize munthu womenyedwa uja. Wamuona wansembe ndi Mlevi patali apo ayenda mu mseu.
Koma wamuona uyu amene ali ndi munthu womenyedwa pacithunzi-thunzi apa. Ameneyu ni Msamariya, koma athandiza Myuda. Iye aika mankhwala pa zilonda zake. Pambuyo pake amutenga Myuda uyu ndi kumupeleka kumalo kumene angagone kuti acile.
Pamene atsiliza kufotokoza fanizo lake, Yesu afunsa munthu amene anamufunsa funso uja kuti: ‘Ndani mwa atatuwa amene iwe uona kuti anaonetsa cikondi kwa munthu amene anamenyedwa ndi acifwamba? Kodi anali wansembe, Mlevi, kapena Msamariya?’
Iye ayankha kuti: ‘Msamariya, cifukwa ni amene anacitila cifundo munthu womenyedwa.’
Yesu akuti: ‘Wanena zoona, pita iwenso uzikacita zomwezo kwa anthu ena.’
Kodi umakonda mmene Yesu amaphunzitsila? Tingaphunzile zinthu zambili-mbili ngati timvetsela ku zimene Yesu amakamba mu Baibo, si conco?
Luka 10:25-37.