Nkhani 94
Yesu Amakonda Tuŵana
WAMUONA Yesu pacithunzi-thunzi apa wakumbatila kamwana. N’coonekelatu kuti Yesu amasamalila tuŵana. Amuna amene amuyang’ana ni atumwi ake. Kodi Yesu awauza ciani? Tiye tione zimene awauza.
Yesu ndi atumwi ake angobwela kumene kucoka paulendo wautali. Ali mu njila, atumwi anali kukangana okha-okha. Conco pamene Yesu afika, awafunsa kuti: ‘Munali kukangana ciani mu njila?’ Yesu adziŵa zimene anali kukangana. Koma awafunsa kuti aone ngati atumwi adzamuuza zimene anali kukangana.
Koma atumwi sayankha, cifukwa cakuti mu njila anali kukangana zakuti wamkulu ndani pakati pao. Atumwi ena afuna kukhala ochuka kuposa anzao. Koma kodi Yesu adzawauza bwanji kuti n’kosayenela kufuna kukhala wamkulu?
Iye aitana kamwana ndi kukaimika patsogolo pao. Ndiyeno auza ophunzila ake kuti: ‘Ndithu ndikuuzani, ngati simutembenuka ndi kukhala ngati ana ang’ono, simudzaloŵa mu ufumu wa Mulungu. Wamkulu kwambili mu ufumu wakumwamba ni amene akhala ngati mwana mng’ono.’ Kodi udziŵa cifukwa cake Yesu anakamba zimenezi?
N’cifukwa cakuti ana ang’ono samadela nkhawa za kukhala wamkulu kapena kukhala wochuka kuposa ena. Conco atumwi ayenela kuphunzila kukhala ngati ana ndi kupewa kukangana zakuti wamkulu kapena wochuka ndani.
Palinso nthawi zina pamene Yesu aonetsa mmene amasamalila tuŵana. Patapita miyezi yocepa anthu ena abweletsa ana ao kuti aonane ndi Yesu. Atumwi aletsa ana ao kubwela kwa Yesu. Koma Yesu auza atumwi ake kuti: ‘Alekeni ana abwele kwa ine, musawaletse iyai. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.’ Ndiyeno Yesu akumbatila anao ndi kuwadalitsa. Kodi si zokondweletsa kudziŵa kuti Yesu amakonda tuŵana?