Nkhani 61
Davide Aikidwa Kukhala Mfumu
SAULI afunanso kugwila Davide. Iye atenga asilikali ake aluso kwambili okwana 3,000 ndi kupita kukamufuna-funa. Pamene Davide adziŵa zimenezi, atumiza azondi kuti akaone kumene Sauli ndi anthu ake amangila msasa. Ndiyeno Davide afunsa anyamata ake aŵili kuti: ‘Ndani angapite nane kumsasa wa Sauli?’
Abisai ayankha kuti: ‘Ndipita nanu.’ Abisai ni mwana wa Zeruya, mlongosi wa Davide. Pamene Sauli ndi anyamata ake ali gone, Davide ndi Abisai aloŵa mu msasa wao mwakacete-cete. Atenga mkondo wa Sauli ndi mtsuko wake wa madzi, zimene zili pafupi ndi mutu wake. Palibe awaona kapena kuwamva cifukwa onse ali m’tulo tofa nato.
Kodi wamuona Davide ali ndi Abisai pacithunzi-thunzi apa? Iwo acokako bwino-bwino ku msasa wa Sauli, ndipo tsopano ali pamwamba pa phili. Davide afuula kwa mkulu wa gulu la nkhondo la Aisiraeli kuti: ‘Abineri, n’cifukwa ciani sunateteze mbuye wako mfumu? Taona! Kodi mkondo ndi mtsuko wa madzi za mfumu zili kuti?’
Sauli auka. Ndipo azindikila mau a Davide, conco afunsa kuti: ‘Kodi ndiwe Davide amene ulankhula?’ Kodi wamuona Sauli ndi Abineri pacithunzi-thunzi cili pansi apa?
Davide ayankha Sauli kuti: ‘Inde, mbuyanga mfumu.’ Ndipo Davide afunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani munithamangitsa? Ndacita ciani ine, ndipo ndalakwa ciani? Si uwu mkondo wanu, mbuyanga. Tumizani mmodzi mwa anyamata anu kuti abwele adzautenge.’
Ndiyeno Sauli akuti: ‘Ndacimwa ndipo ndacita zinthu mopusa.’ Pamenepo, Davide apita, ndipo Sauli abwelela kunyumba kwake. Koma Davide akuti mu mtima mwake: ‘Tsiku lina Sauli adzandipha ine. Conco n’thaŵile ku dziko la Afilisti.’ Ndipo acita zimenezo. Davide apusitsa Afilisti, powacititsa kukhulupilila kuti ali kumbali yao.
Panthawi ina yake, Afilisti anapita kukamenyana nkhondo ndi Aisiraeli. Pankhondo imeneyi, Sauli ndi Yonatani aphedwa. Zimenezi zipangitsa Davide kumva cisoni kwambili, ndipo apeleka nyimbo yogwila mtima kwambili. Iye aimba kuti: ‘Mtima wanga uŵaŵa cifukwa ca iwe m’bale wanga Yonatani. Ndiwe wokondweletsa kwa ine.’
Ndiyeno, Davide abwelela ku Isiraeli ku mzinda wa Heburoni. Pali nkhondo pakati pa anthu amene asankha Isi-boseti mwana wa Sauli kuti akhale mfumu, ndi anthu ena amene afuna Davide kuti akhale mfumu. Koma potsilizila pake, amuna amene ali kumbali ya Davide apambana. Davide ali ndi zaka 30 pamene aikidwa kukhala mfumu. Kwa zaka 7 ndi hafu alamulila ku Heburoni. Ana ake ena amene anabadwila kumeneko ni Aminoni, Abisalomu ndi Adoniya.
Nthawi yafika yakuti Davide ndi asilikali ake apite kukalanda mzinda wokongola wa Yerusalemu. Yoabu, mwana wina wa Zeruya mlongosi wa Davide, ndi amene atsogolela pankhondo imeneyi. Conco Davide ayamikila zimene Yoabu acita mwa kumuika kukhala mkulu wa asilikali ake. Tsopano, Davide ayamba kulamulila mzinda wa Yerusalemu.
1 Samueli 26:1-25; 27:1-7; 31:1-6; 2 Samueli 1:26; 3:1-21; 5:1-10; 1 Mbiri 11:1-9.