Nkhani 74
Mwamuna Wosaopa Munthu
ONA anthu aseka mwamuna wacinyamata uyu. Kodi umudziŵa dzina lake? Ni Yeremiya. Ni mneneli wofunika kwambili wa Mulungu.
Pamene Mfumu Yosiya angoyamba kuononga mafano mu dzikolo, Yehova auza Yeremiya kuti akhale mneneli Wake. Koma Yeremiya aona kuti ni wamng’ono kwambili kuti akhale mneneli. Komabe, Yehova akamba kuti adzamuthandiza.
Yeremiya auza Aisiraeli kuti aleke kucita zinthu zoipa. Iye akuti: ‘Milungu imene anthu amalambila ni yonama.’ Koma Aisiraeli ambili akonda kulambila mafano m’malo molambila Mulungu woona, Yehova. Pamene Yeremiya auza anthu kuti Mulungu adzawalanga cifukwa ca zoipa zao, io angomuseka.
Patapita zaka zambili, Yosiya amwalila, ndipo pambuyo pa miyezi itatu, mwana wake Yehoyakimu akhala mfumu. Yeremiya apitiliza kuuza anthu kuti: ‘Yerusalemu adzaonongedwa ngati simusintha makhalidwe anu oipa.’ Ansembe agwila Yeremiya, ndipo afuula kuti: ‘Uyenela kuphedwa cifukwa cokamba vinthu va conco.’ Ndiyeno ansembe auza akalonga a Isiraeli kuti: ‘Yeremiya ayenela kuphedwa cifukwa wakamba vinthu voipa ponena za mzinda wathu.’
Nanga Yeremiya adzacita ciani pamene zinthu zakhala conco? Iye sacita mantha! Auza anthu onse kuti: ‘Yehova ndiye ananituma kuti nikuuzeni zinthu izi. Ngati simudzasintha makhalidwe anu oipa, Yehova adzaononga Yerusalemu. Koma dziŵani kuti: Mukandipha, ndiye kuti mudzapha munthu wosalakwa.’
Akalonga sanamuphe Yeremiya, komabe Aisiraeli sasintha makhalidwe ao oipa. Pambuyo pake, Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, ibwela ndi kucita nkhondo ndi Yerusalemu. Potsilizila pake, Nebukadinezara apanga Aisiraeli kukhala atumiki ake. Iye atenga Aisiraeli masauzande ambili kupita nao ku Babulo. Ganizila cabe mmene zingakhalile ngati anthu amene sudziŵa akutenga kucoka kwanu ndi kupita nawe kumalo amene sudziŵa.
Yeremiya 1:1-8; 10:1-5; 26:1-16; 2 Mafumu 24:1-17.