Anzake a Mulungu Amacita Vinthu Vabwino
Phunzilo 15
Anzake a Mulungu Amacita Vinthu Vabwino
Ngati muli na mnzanu amene mumakonda na kumulemekeza, mumayesa kukhala monga iye. Baibo imakamba kuti: “Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima.” (Salmo 25:8) Kuti tikhale mnzake wa Mulungu, tifunikila kukhala anthu abwino ndi a mtima wolungama. Baibo imakambanso kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu; monga ana okondedwa ndipo yendani m’cikondi.” (Aefeso 5:1, 2) Onani mmene mungacitile zimenezi:
Muzithandiza ena. “Ticitile onse cokoma.”—Agalatiya 6:10.
Khalani wolimbikila panchito. “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwilitse nchito, nagwile nchito yokoma ndi manja ake.”—Aefeso 4:28.
Khalani munthu waukhondo ndi wamakhalidwe abwino. ‘Tizikonzele tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsiliza ciyelo m’kuopa Mulungu.’—2 Akorinto 7:1.
Aefeso 5:33–6:1.
Muzikondana na kupatsana ulemu na onse a m’banja mwanu. “Yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; . . . ndipo mkaziyo akumbukile kuti aziopa mwamuna. Ananu, mvelani akukubalani.”—Kondani anthu ena. “Tikondane wina ndi mnzake: cifukwa kuti cikondi cicokela kwa Mulungu.”—1 Yohane 4:7.
Muzimvela malamulo a dziko. ‘Anthu onse amvele maulamulilo aakulu [boma]; . . . Pelekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho.’—Aroma 13:1, 7.