Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa

Peza malangizo amene angakuthandize kukhala na umoyo wabwino.

FUNSO 1

Kodi Nifuna Kukhala Munthu Wabwanji?

Kudziŵa makhalidwe ako abwino, zimene umacita bwino, zimene sucita bwino, na zolinga zako, kudzakuthandiza kupanga zosankha zanzelu ukakumana na ciyeso.

FUNSO 2

Nimadelanji Nkhawa na Mmene Nimaonekela?

Kodi sumakondwela na mmene umadzionela pa gilasi? Nanga ungacite ciani kuti uzioneka bwino?

FUNSO 3

Ningakambilane Bwanji na Makolo Anga?

Malangizo aya angakuthandize kukambilana mosavuta na makolo ako.

FUNSO 4

Niyenela Kucita Ciani Nikacita Colakwa?

Nthawi iliyonse ukhoza kulakwitsa zinthu—kulakwa kulibe mwini. Ndiye tifunika kucita ciani?

FUNSO 5

Ningacite Bwanji Ngati Ena Anivutitsa ku Sukulu?

Si kuti palibiletu zimene ungacite. Ukhoza kugonjetsa munthu wokuvutitsa popanda kumenyana naye.

FUNSO 6

Ningakane Bwanji Kutunthiwa na Anzanga?

Cingakhale covuta kucita zimene udziŵa kuti n’zoyenela.

FUNSO 7

Ningacite Bwanji Ngati Wina Aninyengelela kuti Nigone Naye?

Ganizila zimene zinacitikilapo acicepele alionse amene anakondana mopitilila malile.

FUNSO 8

Niyenela Kudziŵa Ciani za Ogona Akazi Mwacikakamizo?

Acicepele ndiwo ali pa vuto kwambili. Kodi ungadziteteze bwanji ku vuto limeneli?

FUNSO 9

Kodi Niyenela Kukhulupilila za Cisanduliko—Evolution?

Ni kafotokozedwe kati komveka?

FUNSO 10

Kodi Baibo Ingan’thandize Bwanji?

Anthu ambili amakamba kuti nkhani zonse za mu Baibo ni nthano cabe, inasila nchito, kapena kuti ni yovuta kuimvetsetsa. Koma zonse izi si zoona.