GAWO 7
Mmene Mungaphunzitsile Mwana Wanu
“Mau awa amene ndikukulamula lelo azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomeleza mwa ana ako.”—Deuteronomo 6:6, 7
Pamene Yehova anapanga makonzedwe a banja, anapatsa makolo udindo wosamalila ana ao. (Akolose 3:20) Makolo, ndi udindo wanu kuphunzitsa mwana wanu kuti akule bwino ndi kuti azikonda Yehova. (2 Timoteyo 1:5; 3:15) Mufunikanso kudziŵa zimene zili mu mtima mwa mwana wanu. Koma mufunika kukhala citsanzo cabwino. Mungaphunzitse bwino mwana wanu Mau a Yehova, ngati coyamba inuyo muwaika pa mtima panu.—Salimo 40:8.
1 KHALANI OMASUKA NDI ANA ANU KUTI NAONSO AZILANKHULA NANU MOMASUKA
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Khalani wofulumila kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Mwacionekele, mumafuna kuti ana anu azilankhula nanu momasuka. Kuti zimenezi zitheke inuyo muyenela kukhala okonzeka kumvetsela ana akamafuna kulankhula. Khalani amtendele kuti athe kufotokoza zonse zimene zili mumtima mwao. (Yakobo 3:18) Ngati aganiza kuti mudzakhala ankhanza kapena muziwapeza zifukwa, sangamasuke nanu kwenikweni. M’malo mwake khalani oleza mtima ndi ana anu ndipo nthawi zonse muziwatsimikizila kuti mumawakonda.—Mateyu 3:17; 1 Akorinto 8:1.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Mvetselani pamene mwana wanu akulankhula
-
Muzilankhulana ndi ana anu nthawi zonse osati cabe pamene ali ndi vuto
2 YESETSANI KUMVETSETSA CIMENE KWENIKWENI AKUTANTHAUZA
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Munthu wosonyeza kuzindikila pa zinthu adzapeza zabwino.” (Miyambo 16:20) Nthawi zina mungafunike kumvetsetsa bwino mau a ana anu kuti mudziŵe mmene akumvela. Nthawi zambili, acicepele amakonda kuonjezela mau akamalankhula kapena kukamba zinthu zimene kwenikweni sanafune kukamba. Baibulo limati, “Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetse bwino n’ngopusa.” (Miyambo 18:13) Musakwiye msanga.—Miyambo 19:11.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Kaya mwana wanu akambe zotani, musamudule mau kapena kukwiya mopitilila malile
-
Kumbukilani mmene inu munali kumvela mukali pa msinkhu wake. Kumbukilaninso zinthu zimene munali kuona kuti n’zofunika panthawi imeneyo
3 ONETSANI KUTI NDINU OGWILIZANA
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Mwana, wanga tamvela malangizo a bambo ako, usasiye malamulo a mayi ako.” (Miyambo 1:8) Yehova wapatsa onse aŵili atate ndi amai udindo wolangiza ana ao. Muyenela kuphunzitsa ana anu kuti azikulemekezani ndi kukumvelani. (Aefeso 6:1-3) Ana angadziŵe ngati makolo ao sali “ogwilizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akorinto 1:10) Mukasiyana maganizo, pewani kukangana pamene ana akuona. Cifukwa anao angaleke kukulemekezani
ZIMENE MUNGACITE:
-
Kambilanani ndi kugwilizana mmene muzilangizila ana anu
-
Ngati inu ndi mnzanu wa m’cikwati muli ndi maganizo osiyana pankhani ya mmene mungaphunzitsile ana anu, yesani kuona mmene mnzanu akuonela zinthu
4 KHALANI NDI POLOGALAMU YABWINO
ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela.” (Miyambo 22:6) Kuphunzitsa bwino ana anu sikungacitike mwangozi. Mufunika kukhala ndi pulogalamu yabwino ya kaphunzitsidwe ndi kulangizidwe. (Salimo 127:4; Miyambo 29:17) Kulanga ana sikutanthauza kuwapatsa cabe cilango coŵaŵa, koma kumaphatikizapo kuwathandiza kumvetsa cifukwa cake mukuwapatsa malamulo. (Miyambo 28:7) Kuonjezela pamenepo, aphunzitseni kukonda mau a Yehova ndi kuzindikila mfundo zake. (Salimo 1:2) Kucita zimenezi kudzawathandiza kuti akhale ndi cikumbumtima cabwino.—Aheberi 5:14.
ZIMENE MUNGACITE:
-
Yesetsani kuthandiza ana anu kuti aziona Mulungu ngati Munthu weniweni amene angamudalile
-
Athandizeni kudziŵa ndi kupewa makhalidwe oononga monga amene amapezeka pa intaneti ndi pa malo ocezela pa intaneti. Auzeni mmene angapewele anthu ocitila ana zinthu zolaula