Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?
Mboni za Yehova zimapezeka padziko lonse, ndipo zimacokela m’mafuko ndi zikhalidwe zosiyana-siyana. Kodi zatheka bwanji kuti anthu osiyana-siyana conco agwilizane capamodzi?
Kodi Cifunilo ca Mulungu n’Ciani?
Mulungu afuna kuti anthu aphunzile za cifunilo cake padziko lonse lapansi. Kodi cifunilo ca Mulungu n’ciani? Nanga ndani masiku ano amene amaphunzitsa anthu zimenezi?
PHUNZILO 1
Kodi Mboni za Yehova Ni Anthu Otani?
Kodi ni Mboni za Yehova zingati zimene mumadziŵa? Kodi n’ciani maka-maka cimene mumadziŵa ponena za ife?
PHUNZILO 2
Ni Cifukwa Ciani Timachedwa Mboni za Yehova?
Onani zifukwa zitatu zimene tinasankhila dzina limeneli.
PHUNZILO 3
Coonadi ca m’Baibo Cipezekanso!
Kodi tingatsimikize bwanji kuti zimene timakhulupilila ndi zogwilizana ndi coonadi ca m’Baibo?
PHUNZILO 4
Ni Cifukwa Ciani Timafalitsa Baibulo la Dziko Latsopano?
Kodi n’ciani cimasiyanitsa Baibo ili ndi Mabaibo ena?
PHUNZILO 5
Kodi Mudzaona Ciani Mukabwela ku Misonkhano Yathu
Timasonkhana pamodzi kuti tiphunzile Malemba ndi kulimbikitsana. Tidzakulandilani ndi manja aŵili.
PHUNZILO 6
Kuyanjana ndi Akhristu Anzathu Kumatithandiza Pambali Ziti?
Mau a Mulungu amalimbikitsa Akhristu kuceza pamodzi. Onani mmene mungapindulile ndi maceza amenewa.
PHUNZILO 7
Kodi Misonkhano Yathu Imacitika Bwanji?
Kodi munaganizapo zimene zimacitika pamisokhano yathu? Mosakaikila mudzasangalala ndi maphunzilo ocokela m’Baibo amene mudzalandila.
PHUNZILO 8
Ni Cifukwa Ciani Timavala Bwino Pamisonkhano Yathu?
Kodi zimene timavala ndi nkhani yaikulu kwa Mulungu? Onani mfundo za m’Baibo zimene timatsatila pankhani ya kavalidwe ndi maonekedwe.
PHUNZILO 9
Mmene Tingakonzekelele Misonkhano
Kukonzekela misonkhano yathu pasadakhale kudzakuthandizani kupindula kwambili.
PHUNZILO 10
Kodi Kulambila kwa Pabanja n’Ciani?
Onani mmene makonzedwe amenewa angakuthandizileni kuyandikila Mulungu ndi kulimbitsa mgwilizano wa banja lanu
PHUNZILO 11
Ni Cifukwa Ciani Timacita Misonkhano Ikulu-ikulu?
Caka ciliconse timacita misonkhano itatu yofunika kwambili. Kodi mungapindule bwanji ndi misonkhano imeneyi?
PHUNZILO 12
Kodi Nchito Yathu Yolalikila Ufumu Imacitika Bwanji?
Timatsatila citsanzo cimene Yesu anatisiila pamene anali padziko lapansi. Kodi zina mwa njila zolalikilila ndi ziti?
PHUNZILO 13
Kodi Mpainiya Ndani?
Pa mwezi mboni zina zimathela maola 30, 50, kapena kuposapo pa nchito yolalikila. N’ciani cimawasonkhezela kucita zimenezi?
PHUNZILO 14
Kodi Apainiya Amalandila Maphunzilo Anji?
Kodi amene amadzipeleka kuti azilalikila za Ufumu nthawi zonse amalandila maphunzilo apadela ati?
PHUNZILO 15
Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?
Akulu ni amuna ofikapo mwa kuuzimu ndipo amatsogolela mpingo. Kodi amatithandiza m’njila ziti?
PHUNZILO 16
Kodi Atumiki Othandiza Ali ndi Udindo Wanji?
Atumiki othandiza amathandiza kuti mpingo uziyenda bwino. Onani mmene nchito yao imapindulitsila onse opezeka pamisonkhano
PHUNZILO 17
Kodi Oyang’anila Dela Amatithandiza m’Njila Ziti?
N’cifukwa ciani oyang’anila dela amacezela mipingo? Kodi amatithandiza pambali ziti akamacezela mpingo?
PHUNZILO 18
Kodi Timacita Ciani Pakagwa Tsoka Kuti Tithandize Abale Athu?
Pakagwa tsoka, mwamsanga timapeleka cithandizo cakuthupi ndi cakuuzimu kwa anthu amene akuvutika. Kodi timawathandiza m’njila ziti?
PHUNZILO 19
Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?
Yesu analonjeza kuti adzasankha kapolo kuti azigaŵila cakudya cakuuzimu ca panthawi yake. Kodi kapolo amacita bwanji zimenezi?
PHUNZILO 20
Mmene Bungwe Lolamulila Limagwilila Nchito Masiku Ano
IM’zaka za zana loyamba, kagulu ka akulu ndi atumwi kanatumikila monga bungwe lolamulila la mpingo wacikristu. Nanga bwanji masiku ano?
PHUNZILO 21
Kodi Beteli n’Ciani?
Beteli ndi malo apadela kumene kumacitika nchito yofunika kwambili. Dziŵani zambili zokhudza anthu amene amatumikila kumeneko.
PHUNZILO 22
Kodi ku Ofesi ya Nthambi Kumacitika Nchito Yanji?
Timalandila ndi manja aŵili alendo amene afuna kudzaona maofesi athu a nthambi. Tikupemphani kuti mukabwele.
PHUNZILO 23
Kodi Mabuku Athu Amalembedwa ndi Kumasulidwa Bwanji?
Timafalitsa mabuku m’zinenelo zopitilila 750. N’cifukwa ciani timacita khama conco?
PHUNZILO 24
Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?
Kodi cipembedzo cathu cimasiyana bwanji ndi zipembedzo zina pankhani ya ndalama?
PHUNZILO 25
Timamangilanji Nyumba za Ufumu? Nanga Timamanga Bwanji
N’cifukwa ciani malo athu olambilila amachedwa Nyumba za Ufumu? Dziŵani zambili za mmene Nyumba za Ufumu zimenezi zimathandizila mipingo.
PHUNZILO 26
Tingacite Ciani Kuti Tisamalile Nyumba Yathu ya Ufumu?
Nyumba ya Ufumu ya ukhondo ndi yokonzedwa bwino imacititsa kuti Mulungu wathu atamandike. Kodi pamakhala makonzedwe otani kuti Nyumba ya Ufumu izikhala yaukhondo?
PHUNZILO 27
Kodi Tingapindule Bwanji Ndi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu?
Kodi mukufuna kufufuza zinthu zina kuti mudziŵe zambili za m’Baibo? Pitani ku laibulale ya Kunyumba ya Ufumu
PHUNZILO 28
Kodi pa Webusaiti Yathu Pamapezeka Ciani?
Mungadziŵe zambili zokhudza ife ndi zikhulupililo zathu ndipo mungadziŵenso mayankha pa mafunso a m’Baibo.
Kodi Inu Mudzayamba Kucita Cifunilo ca Yehova?
Yehova Mulungu amakukondani kwambili. Kodi mungaonetse bwanji kuti mukufuna kumam’sangalatsa pamoyo wanu watsiku ndi tsiku?