Kubweleza Cigawo 3
Kambilanani mafunso aya na mphunzitsi wanu:
Ŵelengani Miyambo 27:11.
N’cifukwa ciyani mukufuna kukhala wokhulupilika kwa Yehova?
(Onani Phunzilo 34.)
Kodi mungapange bwanji zisankho zabwino pa nkhani imene Baibo siipelekapo lamulo lacindunji?
(Onani Phunzilo 35.)
Kodi muyenela kucita bwanji kuti muzikhala oona mtima pa zinthu zonse?
(Onani Phunzilo 36.)
Ŵelengani Mateyu 6:33.
Pa nkhani ya nchito, komanso ndalama, kodi mungafune-fune bwanji “ufumu coyamba”?
(Onani Phunzilo 37.)
Kodi ni njila ziti zimene mungaonetsele kuti mumalemekeza moyo mmene Yehova amacitila?
(Onani Phunzilo 38.)
Ŵelengani Machitidwe 15:29.
Kodi muyenela kucita bwanji poonetsa kuti mumamvela lamulo la Yehova pa nkhani ya magazi?
Kodi mukuona kuti zimene Mulungu akufuna pa nkhani imeneyi zili bwino?
(Onani Phunzilo 39.)
Ŵelengani 2 Akorinto 7:1.
Kodi kukhala woyela kuthupi komanso m’makhalidwe athu kumatanthauza ciyani?
(Onani Phunzilo 40.)
Ŵelengani 1 Akorinto 6:9, 10.
Kodi Baibo imati ciyani pa nkhani ya kugonana? Kodi inu mukugwilizana nazo?
Kodi Baibo imapeleka malangizo otani pa nkhani ya kumwa moŵa?
(Onani Phunzilo 41 na 43.)
Ŵelengani Mateyu 19:4-6, 9.
Kodi Mulungu amapeleka lamulo lanji pa nkhani ya ukwati?
N’cifukwa ciyani anthu akakwatilana, kapena akasudzulana, ayenela kulembetsa ku boma?
(Onani Phunzilo 42.)
Kodi ni zikondwelelo ziti kapena maholide amene Yehova sakondwela nawo? Ndipo cifukwa ciyani?
(Onani Phunzilo 44.)
Ŵelengani Yonane 17:16, komanso Machitidwe 5:29.
Kodi mungapewe bwanji kukhalila mbali m’nkhani za dziko?
Pakakhala kuwombana pakati pa lamulo la anthu komanso lamulo la Mulungu, kodi muyenela kucita bwanji?
(Onani Phunzilo 45.)
Ŵelengani Maliko 12:30.
Kodi mungaonetse bwanji kuti Yehova mumam’konda?
(Onani Phunzilo 46 na 47.)