Kodi Ndine Wokonzeka?
Kodi Ndine Wokonzeka Kulalikila Pamodzi na Mpingo
Mungakhale wofalitsa wosabatizika . . .
Ngati mumaphunzila Baibo nthawi zonse, ndipo mumapemphela, komanso mumapezeka ku misonkhano ya mpingo.
Ngati mumayamikila na kukhulupilila zimene mumaphunzila, ndiponso mumauzako ena zimene mumaphunzilazo.
Ngati mumakonda Yehova na kusankha anzanu amenenso amamukonda.
Ngati munafutitsa dzina lanu ku cipani candale kapena cipembedzo conyenga.
Ngati mumatsatila malamulo a Yehova pa umoyo wanu, ndipo mukufunadi kukhala Mboni ya Yehova.
Ngati mukuona kuti ndinu wokonzeka kuyamba kulalikila pamodzi na mpingo, dziŵitsani wokuphunzitsani Baibo. Iye adzadziŵitsa akulu, ndipo iwo adzakumana nanu na kukuuzani zofunikila.
Kodi Ndine Wokonzeka Kubatizika?
Mungakhale wokonzeka kubatizika . . .
Ngati ndinu wofalitsa wosabatizika.
Ngati nthawi zonse mumatengako mbali pa nchito yolalikila.
Ngati mumalemekeza na kutsatila citsogozo ca “kapolo wokhulupilika ndi wa nzelu.”—Mateyu 24:45-47.
Ngati munadzipatulila kwa Yehova m’pemphelo, ndipo mukufuna kumutumikila mpaka muyaya.
Ngati muona kuti ndinu wokonzeka kubatizika, dziŵitsani wokuphunzitsani Baibo. Iye adzakuthandizani kuti mukakumane na akulu, ndipo iwo adzakuuzani zofunikila.