Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
Kabuku kano kanakonzedwa kuti kakuthandizeni kunola maluso anu a kuŵelenga, kulankhula, komanso kuphunzitsa.
Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila
Timalalikila uthenga wofunika kwambili kwa anthu kuposa wina uliwonse.
PHUNZILO 2
Kukambilana Mwacibadwa
Kukambilana mwacibadwa kumamasula omvela anu, komanso kumawathandiza kulabadila uthenga wanu.
PHUNZILO 3
Gwilitsilani Nchito Mafunso
Mafunso aluso angakuthandizeni kuwakopa cidwi omvela anu, na kugogomeza mfundo zofunika.
PHUNZILO 4
Kachulidwe ka Malemba Koyenela
Onani mmene mungakonzekeletsele maganizo a omvela anu musanaŵelenge lemba.
PHUNZILO 5
Kuŵelenga Bwino
Kuŵelenga bwino ni mbali yofunika kwambili pothandiza ena kudziŵa za Yehova.
PHUNZILO 6
Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba
Thandizani omvela anu kuona bwino-bwino kugwilizana kwa lemba imene mwaŵelenga na mfundo imene mukufotokoza.
PHUNZILO 7
Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa
Kukamba maumboni a zoona komanso okhulutilitsa, kumathandiza omvela anu kukhutila na zimene mukukamba.
PHUNZILO 8
Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu
Phunzitsani mwaluso pogwilitsila nchito mafanizo osavuta kumva kwa omvela anu, komanso kumveketsa mfundo zofunika.
PHUNZILO 9
Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka
Seŵenzetsani zitsanzo zooneka kuti mukhomeleze kwambili mfundo m’maganizo mwa omvela anu.
PHUNZILO 10
Kusintha-sinthako Mawu
Muzisiyanitsa liŵilo la mau anu, kamvekedwe kake, komanso mphamvu yake, kuti mukhudze mtima omvela anu, na kuwalimbikitsa kucitapo kanthu.
PHUNZILO 11
Kukamba Mwaumoyo
Kukamba mwaumoyo kumaonetsa mmene mukumvelela, komanso kumakuthandizani kukopa cidwi ca omvela anu.
PHUNZILO 12
Mzimu Waubwenzi na Cifundo
Ngati mulankhula na mzimu woyenelela, mumaonetsa kuti mumawaganizila omvela anu.
PHUNZILO 13
Kumveketsa Phindu ya Nkhani
Thandizani omvela anu kumvetsa mmene nkhani yanu ikukhudzila umoyo wawo. Komanso afotokozeleni mocitila nazo zimene aphunzila.
PHUNZILO 14
Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu
Thandizani omvela anu kukutsatilani m’nkhani yanu. Onetsani bwino mmene mfundo yaikulu iliyonse ikugwilizanila na colinga canu, komanso na mutu wa nkhani.
PHUNZILO 15
Kukamba Motsimikiza
Kambani motsimikiza. Onetsani kuti mumakhulupilila kuti zimene mukamba n’zofunika ngako.
PHUNZILO 16
Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula
Kambani molimbikitsa osati mosuliza. Lunjikitsani nkhani yanu ku mfundo zotsitsimula za m’Mawu a Mulungu.
PHUNZILO 17
Muzikamba Zosavuta Kumvetsa
Thandizani omvela anu kumvetsa zimene mukukamba. Mveketsani mfundo zofunika momveka bwino.
PHUNZILO 18
Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela
Kambani mwa njila yopangitsa omvela anu kuganizilapo pa nkhaniyo, na kuwathandiza kuphunzilapodi kanthu.
PHUNZILO 19
Yesetsani Kuwafika pa Mtima Omvela
Limbikitsani omvela anu kukonda Mulungu, na Mawu ake Baibo.
PHUNZILO 20
Mawu Otsiliza Ogwila Mtima
Mawu otsiliza ogwila mtima, adzathandiza omvela anu kuona ubwino wa zimene aphunzila kuti akazigwilitsile nchito.
Lembani Mmene Mwapitila Patsogolo
Lembani mmene mwapitila patsogolo kuti munole maluso anu a kuŵelenga na kuphunzitsa.
Mungakondenso Izi
MPAMBO WA MAVIDIYO