Mawu Oyamba a Cigawo 1
Baibo imayamba nkhani zake mwa kufotokoza zinthu zokongola zimene Yehova analenga kumwamba na pa dziko lapansi. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kudziŵa zinthu zodabwitsa za cilengedwe. M’fotokozeleni za mmene Mulungu analengela ise anthu mwapadela kwambili, kupambana nyama. Ife anthu timakamba, kuganiza, kupanga zinthu, kuimba, na kupemphela. M’thandizeni kuyamikila mphamvu za Yehova na nzelu zake, maka-maka cikondi cake pa zinthu zonse zimene analenga—kuphatikizapo aliyense wa ise.
M'CIGAWO CINO
PHUNZILO 1
Mulungu Anapanga Kumwamba na Dziko Lapansi
Baibo imati Mulungu anapanga kumwamba na dziko lapansi. N’cifukwa ciani Mulungu analenga mngelo mmodzi coyamba akalibe kulenga cina ciliconse kapena wina aliyense?
PHUNZILO 2
Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
Mulungu anapanga mwamuna na mkazi woyamba na kuŵaika m’munda wa Edeni. Anali kufuna kuti iwo akhale ndi ana na kupanga dziko lonse kukhala paradaiso.