PHUNZILO 75
Mdyelekezi Ayesa Yesu
Pambuyo pakuti Yesu wabatizika, mzimu woyela unamutsogolela ku cipululu. Iye sanadye ciliconse kwa masiku 40, ndipo anamvela njala kwambili. Pamenepo Mdyelekezi anabwela kudzamuyesa. Iye anauza Yesu kuti: ‘Ngati ndimwe Mwana wa Mulungu zoona, uzani miyala iyi kuti isanduke cakudya.’ Yesu anagwila Malemba poyankha. Iye anati: ‘Malemba amakamba kuti munthu sangakhale na moyo cifukwa ca cakudya cabe, koma afunikanso kumvela mawu onse a Yehova.’
Mdyelekezi anabwelanso kaciŵili kudzayesa Yesu. Iye anati: ‘Ngati ndimwe Mwana wa Mulungu zoona, lumphani kucokela pamwamba pa kacisi. Malemba amati Mulungu adzatumiza angelo ake kuti adzakunyamuleni kuti musavulale.’ Koma Yesu anagwilanso Malemba. Anati: ‘Malemba amakambanso kuti usamuyese Yehova.’
Kacitatu, Satana anaonetsa Yesu maufumu onse a pa dziko lapansi, pamodzi na ulemelelo wawo komanso cuma cawo. Kenako Satana anati: ‘Nidzakupatsani maufumu onse aya ngati munganilambileko kamodzi cabe.’ Koma Yesu poyankha anati: ‘Coka Satana! Malemba amati muzilambila Yehova yekha cabe.’
Pamenepo Mdyelekezi anacokapo. Ndipo angelo anabwela na kum’patsa cakudya Yesu. Kucokela apa, Yesu anayamba kugwila nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Ndiye nchito imene Mulungu anatumila Yesu pa dziko lapansi. Anthu anali kukondwela na zimene Yesu anali kuwaphunzitsa, cakuti anali kumulondola kulikonse kumene anali kuyenda.
“Pamene [Mdyelekezi] akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, cifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yohane 8:44