PHUNZILO 76
Yesu Ayeletsa Kacisi
M’caka ca 30 C.E. Yesu anayenda ku Yerusalemu. Anthu ambili anapita ku Yerusalemu kukacita cikondwelelo ca Pasika. Pa nthawi ya cikondwelelo cimeneci, anthu anali kupeleka nsembe za nyama pakacisi. Nyama zimenezo, ena anali kubwela nazo, koma ena anali kukazigula ku Yerusalemu kumeneko.
Pamene Yesu anapita kukacisi, anapeza kuti anthu akugulitsa nyama kumeneko. Ganizila cabe! Iwo anali kupangila ndalama m’nyumba yolambililamo Yehova. Kodi Yesu anacita bwanji? Anapanga cikwapu ca nthambo, na kuthamangitsa nkhosa na ng’ombe kuzicotsa m’kacisi. Anagubuduza mathebulo a osintha ndalama,
na kutayila pansi ndalama zawo. Ndiyeno anauza ogulitsa nkhunda kuti: ‘Zicotseni muno izi! Musasandutse nyumba ya Atate wanga kukhala mocitila malonda!’Anthu pakacisi anadabwa kwambili na zimene Yesu anacita. Koma ophunzila ake anakumbukila ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Nidzadzipeleka na mtima wonse pa nyumba ya Yehova.’
Mu 33 C.E., Yesu anayeletsanso kacisi kaciŵili. Sanalole munthu aliyense kucita zinthu zonyoza nyumba ya Atate wake.
“Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” —Luka 16:13