Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 27

Anapandukila Yehova

Anapandukila Yehova

Pa nthawi ina Aisiraeli akali m’cipululu, Kora, Datani, Abiramu, ndi anthu ena 250 anaukila Mose. Anamuuza kuti: ‘Talema nawe lomba! Iwe ungakhale bwanji mtsogoleli wathu? Naye Aroni angakhale bwanji mkulu wa ansembe? Sikuti Yehova ali na iwe na Aroni cabe, alinso na ise tonse.’ Yehova sanakondwele nazo zimenezi. Anaona kuti kuukila Mose, kunali kum’pandukila Yehova!

Mose anauza Kora na anzake kuti: ‘Maŵa mukabwele ku cihema na zofukizila zanu zodzala nsembe zofukiza. Yehova adzationetsa amene iye adzasankha.’

M’maŵa mwake, Kora na amuna 250 anayenda kukakumana na Mose ku cihema. Kumeneko iwo anayamba kufukiza nsembe olo kuti sanali ansembe. Ndiyeno Yehova anauza Mose na Aroni kuti: ‘Cokani pakati pa Kora na anzake.’

Kora ndiye anapita kukaonana na Mose ku cihema. Koma Datani, Abiramu, na mabanja awo anakana kuyendako. Yehova anauza Aisiraeli kuti acoke ku misasa ya Kora, Datani, na Abiramu. Nthawi yomweyo Aisiraeli anacokako. Datani, Abiramu, na mabanja awo anaimilila panja pa matenti awo. Basi mwadzidzidzi, nthaka inang’ambika n’kuwameza onse! Ku cihema kuja, Kora na anzake 250 ananyeka na moto wocokela kumwamba.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Tenga ndodo ya mtsogoleli wa fuko lililonse na kulembapo dzina la mtsogoleliyo. Koma pa ndodo ya fuko la Levi, ulembepo dzina la Aroni. Uike ndodo zimenezo mkati mwa cihema colambililako. Ndodo ya munthu amene nasankha idzamela maluŵa.’

Tsiku lokonkhapo, Mose anatenga ndodo zonse na kuzibweletsa kwa atsogoleli a mafuko. Ndodo ya Aroni ndiye inamela maluŵa, ndipo inali na zipatso za maamondi zakupsa. Izi zinatsimikizila kuti Yehova anali atasankha Aroni kukhala mkulu wa ansembe.

“Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela.”—Aheberi 13:17