Mawu Oyamba a Cigawo 9
M’cigawo cino tidzaphunzila za acicepele, aneneli, komanso mafumu amene anaonetsa cikhulupililo camphamvu mwa Yehova. Ku Siriya, kunali kamtsikana kena kaciisiraeli komwe kanali kukhulupilila kuti mneneli wa Yehova angacilitse Namani. Mneneli Elisa anali na cidalilo conse mwa Yehova kuti adzam’teteza ku gulu la adani ake. Mkulu wa Ansembe Yehoyada anaika moyo wake paciswe, kuti ateteze wacicepele Yehoasi kwa ambuye ake aakazi oipa kwambili, Ataliya. Mfumu Hezekiya inali na cidalilo cakuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu, ndipo iye sanagonje kwa Asuri pomuwopseza. Mfumu Yosiya inafafaniza kulambila mafano m’dziko lawo, inamanganso kacisi, na kuthandiza anthu kuyambanso kulambila koona.
M'CIGAWO CINO
PHUNZILO 51
Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali
Kamtsikana kaciisiraeli kauza adona ake za mphamvu zazikulu za Yehova za kucilitsa mozizwitsa.
PHUNZILO 52
Asilikali a Yehova Amoto
Mmene mtumiki wa Elisa anaonela kuti ‘tili na ambili kumbali yathu kuposa amene ali kumbali yawo.’
PHUNZILO 53
Yehoyada Anali Wolimba Mtima
Mosasamala kanthu za mfumukazi yoipa, wansembe wokhulupilika aonetsa kulimba mtima.
PHUNZILO 54
Yehova Anamulezela Mtima Yona
Kodi cinacitika n’ciani kuti mmodzi wa aneneli a Mulungu amezedwe na cinsomba cacikulu? Nanga anacokamo bwanji? Kodi Yehova anam’phunzitsa ciani?
PHUNZILO 55
Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya
Adani a Ayuda akuti Yehova sadzateteza anthu ake, koma zimenezi si zoona!
PHUNZILO 56
Yosiya Anali Kukonda Cilamulo ca Mulungu
Yosiya akhala mfumu ali na zaka 8 cabe, ndipo athandiza anthu kuyamba kulambila Yehova.