MUTU 2
Khalani na Cikumbumtima Cabwino kwa Mulungu
‘Khalani na cikumbumtima cabwino.’ —1 PETULO 3:16.
1, 2. N’cifukwa ciani kupeza munthu wokulangizani njila, kapena cipangizo, n’kofunika ngako? Kodi Yehova anatipatsa ciani kuti cizititsogolela?
YELEKEZANI kuti mukuyenda m’cipululu cacikulu. Maonekedwe a malo akungosintha-sintha cifukwa cimphepo cikukankhila mcenga kumalo osiyana-siyana uku na uku, cakuti mukhoza kusoŵa mosavuta. Kodi mungadziŵe bwanji kumene muyenda? Mungafunikile munthu wokulangizani njila, kapena cipangizo
cokuthandizani. Ingakhale kampasi, dzuŵa, nyenyezi, mapu, kapena munthu wocidziŵa bwino cipululuco. Zimenezi n’zofunikila ngako, cifukwa kudziŵa kumene muyenda kungapulumutse moyo wanu.2 Tonse timakumana na mavuto osiyana-siyana mu umoyo, cakuti tikhoza kukhala otayika m’maganizo. Koma Yehova anapatsa munthu aliyense cikumbumtima kuti cizim’tsogolela. (Yakobo 1:17) Kodi cikumbumtima n’ciani maka-maka? Nanga cimaseŵenza bwanji? Tikadziŵa zimenezi, tidzadziŵanso mmene tingaphunzitsile cikumbumtima cathu, komanso cifukwa cake tifunika kudela nkhawa zikumbumtima za anthu ena, na mmene cikumbumtima coyela cimatipatsila umoyo wabwino.
KODI CIKUMBUMTIMA N’CIANI? NANGA CIMASEŴENZA BWANJI?
3. Kodi cikumbumtima n’ciani?
3 Cikumbumtima ni mphatso yapadela imene Yehova anatipatsa. Ni mtima uja umene umatiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. Liwu lacigiriki la m’Baibo limene analimasulila kuti “cikumbumtima” limatanthauza “kudzidziŵa bwino iwe wekha.” Ngati cikumbumtima cathu ciseŵenza bwino, cimatithandiza kudzifufuza kuti tidziŵe kuti ndine munthu wabwanji. Cingatithandize kuvomeleza maganizo obisika a mkati-kati mwa mtima wathu. Cingatitsogolele ku zinthu zabwino, komanso kutipatutsa ku zinthu zoipa. Cimatimvetsa bwino tikapanga cosankha canzelu, koma cimativutitsa mumtima tikacita cinthu coipa.—Onani Mfundo ya Kumapeto 5.
4, 5. (a) N’ciani cinacitika pamene Adamu na Hava ananyalanyaza cikumbumtima cawo? (b) N’zitsanzo ziti za m’Baibo zoonetsa mmene cikumbumtima cimaseŵenzela?
Genesis 3:7, 8) Olo kuti onse anali na cikumbumtima, ndipo anadziŵa kuti kusamvelela Mulungu n’kulakwa, aliyense anasankhabe kunyalanyaza cikumbumtima cake.
4 Munthu aliyense angasankhe kumvelela cikumbumtima cake kapena kucinyalanyaza. Adamu na Hava anasankha kucinyalanyaza, ndiye cifukwa cake anacimwa. Pambuyo pake anadziimba mlandu, koma sizinaphule kanthu. Anali atam’cimwila kale Mulungu. (5 Koma alipo anthu ambili opanda ungwilo amene amamvelela cikumbumtima cawo. Citsanzo cabwino ni Yobu. Cifukwa copanga zosankha zanzelu, iye anati: “Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.” (Yobu 27:6) Yobu pokamba kuti “mtima wanga,” anatanthauza cikumbumtima cake, inde mtima wouza munthu cabwino kapena coipa. Koma Davide nthawi zina ananyalanyaza cikumbumtima cake na kucimwila Yehova. Pambuyo pake, “anavutika mumtima mwake,” monga kuti cikumbumtima cake cinali kum’kwapula. (1 Samueli 24:5) Cinali kumuuza kuti ‘izi zimene wacita wacimwa.’ Iye anafunikila kumvelela cikumbumtima cake kuti asakacitenso chimo limenelo.
6. N’cifukwa ciani m’pake kukamba kuti cikumbumtima ni mphatso yocokela kwa Mulungu?
6 Ngakhale anthu amene sadziŵa Yehova amadziŵa kuti pali zinthu zoyenela na zosayenela. Baibo imakamba kuti: “Maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomeleza.” (Aroma 2:14, 15) Mwacitsanzo, anthu ambili amadziŵa kuti kupha munthu kapena kuba n’kulakwa. Cimene cimawauza mumtima mwawo kuti ici n’coipa, ndiye cikumbumtima cimene Yehova anaikamo, olo kuti iwo sangadziŵe. Amacitanso mogwilizana na mfundo zimene Mulungu anatipatsa, kuti zitithandize kumapanga zosankha zabwino mu umoyo wathu.
7. N’cifukwa ciani nthawi zina cikumbumtima cathu cingatinamize?
7 Koma nthawi zina cikumbumtima cingatinamize. Mwacitsanzo, cifukwa ca maganizo athu olakwika, cikumbumtima cathu cingatipeleke ku njila yosayenela. Cikumbumtima cabwino sicimangobwela cokha iyayi. (Genesis 39:1, 2, 7-12) Timacita kuciphunzitsa. Ndipo Yehova amatipatsa mzimu woyela na mfundo za m’Baibo kuti zitithandize. (Aroma 9:1) Koma kodi tingaciphunzitse bwanji cikumbumtima cathu? Tiyeni tione.
KODI CIKUMBUMTIMA CATHU TINGACIPHUNZITSE BWANJI?
8. (a) Kodi maganizo athu angakhudze bwanji cikumbumtima cathu? (b) Tikalibe kupanga cosankha, kodi tiyenela kudzifunsa ciani?
8 Anthu ena amaganiza kuti kumvelela cikumbumtima cawo, kumatanthauza kucita zimene zili m’maganizo mwawo. Amaona kuti akhoza kucita ciliconse, malinga ngati mtima wawo wacikonda. Koma mtima wathu ni wopanda ungwilo. Ndipo maganizo athu akhoza kukhala amphamvu cakuti angapondeleze cikumbumtima cathu. Baibo imati: “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa. Ndani angaudziŵe?” (Yeremiya 17:9) Inde, tingayambe kuona cinthu cina kuti n’cabwino pamene n’coipa. Mwacitsanzo, Paulo akalibe kukhala Mkhristu, anavutitsa anthu a Mulungu mwankhanza kwambili. M’maganizo mwake, anali kuona kuti zimenezo zinali zoyenela, cakuti anazicita na cikumbumtima coyela. Koma pambuyo pake anakamba kuti: “Yehova ndiye amandifufuza.” (1 Akorinto 4:4; Machitidwe 23:1; 2 Timoteyo 1:3) Pamene Paulo anadziŵa kuti anali kulakwila Yehova, anazindikila kuti afunika kusintha. Conco, tikalibe kucita ciliconse, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova afuna kuti nicite bwanji?’
9. Kodi kuyopa Mulungu kumatanthauza ciani?
9 Ngati mumakonda munthu wina, simungafune kum’khumudwitsa. Cifukwa timam’konda Yehova, sitifuna kucita ciliconse cimene cingam’kwiyitse. Tifunika kuyopa kwambili kukwiitsa Yehova. Citsanzo cabwino ni Nehemiya. Iye anakana kulemelelapo pa udindo wake wa ubwanamkubwa. Cifukwa ciani? Iye anati “cifukwa coopa Mulungu.” (Nehemiya 5:15) Nehemiya sanafune kucita ciliconse cimene cikanakwiyitsa Yehova. Monga Nehemiya, na ise tiyenela kuyopa kucita ciliconse cimene cingakwiyitse Yehova. Kuti tidziŵe zimene zimam’kondweletsa, tifunika kumaŵelenga Baibo.—Onani Mfundo ya Kumapeto 6.
10, 11. Ni mfundo za m’Baibo ziti zingatithandize kupanga zosankha zabwino pa nkhani ya moŵa?
10 Mwacitsanzo, Mkhristu angafunike kusankha kuti amwe moŵa kapena iyai. Kodi ni mfundo ziti zimene zingam’thandize kupanga cosankha canzelu? Zina ni izi: Baibo siiletsa kumwa moŵa. Ndipo imakamba kuti vinyo, kapena kuti waini, ni mphatso yocokela kwa Mulungu. (Salimo 104:14, 15) Ngakhale n’conco, Yesu anauza otsatila ake kuti sayenela “kumwa kwambili.” (Luka 21:34) Paulo naye anauza Akhristu kuti azipewa “maphwando aphokoso ndi kumwa mwaucidakwa.” (Aroma 13:13) Anakamba kuti acakolwa “sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.
* Kodi nimakwanitsa kuceza mosangalala na anzanga palibe moŵa?’ Tingapemphe Yehova kuti atithandize kupanga zosankha zanzelu. (Ŵelengani Salimo 139:23, 24.) Tikacita zimenezi, tidzaphunzitsa cikumbumtima cathu kulabadila mfundo za m’Baibo. Koma si izi cabe, palinso zina zofunikila.
11 Mkhristu angadzifunse kuti: ‘Kodi moŵa ni cinthu cofunika bwanji kwa ine? Kodi nimadalila moŵa kuti nisangulukeko, kapena kuti nicotse mantha? Kodi nimakwanitsa kungomwako mwa saizi cabe, komanso mwa apa na apo?TIYENELA KUGANIZILANSO ZIKUMBUMTIMA ZA ENA
12, 13. N’cifukwa ciani zikumbumtima za anthu n’zosiyana-siyana? Tiyenela kucita bwanji tikaona kusiyana kumeneku?
12 Ise anthu timakhala na zikumbumtima zosiyana-siyana. Cikumbumtima canu cingakuloleni kucita cinthu cimene wina cikumbumtima cake sicingamulole. Mwacitsanzo, imwe mungasankhe kumwako moŵa, pamene wina angasankhe kusamwa. N’cifukwa ciani anthu angakhale na maganizo osiyana pa nkhaniyi?
13 Mmene munthu amaonela cinthu cingadalile na kumene anakulila, mmene a m’banja lakwawo amacionela cinthuco, zimene wakumana nazo mu umoyo, na zinthu zina. Pa nkhani ya moŵa, munthu amene kumbuyoku anali na vuto la ucakolwa, angasankhe kungolekelatu moŵa. (1 Mafumu 8:38, 39) Ndiye mungamvele bwanji ngati mupatsa munthu moŵa koma iye n’kukana? Kodi muyenela kukhumudwa? Kapena mudzamuumiliza kuti amwe? Kodi mufunika kumufunsa kuti akuuzeni cimene wakanila? Iyai, cifukwa mufunika kulemekeza cikumbumtima cake.
14, 15. Kodi panali cocitika canji m’nthawi ya Paulo? Nanga Paulo anapeleka malangizo abwino akuti ciani?
14 M’nthawi ya mtumwi Paulo, panali cocitika cimene cinaonetsa mmene zikumbumtima zingakhalile zosiyana. Nyama ina imene anali kugulitsa m’misika, inali ija imene anaiseŵenzetsa pa kulambila konama na kuipeleka nsembe ku mafano. (1 Akorinto 10:25) Kwa Paulo panalibe vuto kugula nyama imeneyo na kudya. Kwa iye zakudya zonse ni Yehova anazipeleka. Koma abale ena amene poyamba anali kulambila mafano, anaona zinthu mosiyana. Anaona kuti n’kulakwa kudya nyama imeneyo. Kodi Paulo anaganiza kuti: ‘Ngati cikumbumtima canga cinilola vuto palibe. Nili na ufulu wakudya zimene nifuna’?
15 Paulo sanaganize conco. Iye sanafune olo pang’ono kukhumudwitsa abale ake, cakuti anali wokonzeka kudzimana ufulu wake. Iye anakamba kuti sitiyenela ‘kudzikondweletsa tekha.’ Anati: “Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweletse yekha.” (Aroma 15:1, 3) Molingana na Yesu, Paulo anali kuganizila kwambili anthu ena kupambana iye mwini.—Ŵelengani 1 Akorinto 8:13; 10:23, 24, 31-33.
16. N’cifukwa ciani sitiyenela kuweluza m’bale wathu pa zimene cikumbumtima cake camulola kucita?
16 Koma bwanji ngati wina cikumbumtima cake cimulola kucita zinthu zimene ise tiona kuti n’zoipa? Tifunika kusamala kwambili kuti tisamaweluze ena mwa kuumilila pa maganizo akuti ise tili bwino, koma iwo ni olakwa. (Ŵelengani Aroma 14:10.) Yehova anatipatsa cikumbumtima kuti ciziweluza ise, osati kuweluzila anthu ena. (Mateyu 7:1) Sitifuna kuti zokonda zathu zizibweletsa magaŵano mu mpingo. M’malo mwake, tizifuna-funa njila zolimbikitsila cikondi na mgwilizano.—Aroma 14:19.
TIMAPINDULA NA CIKUMBUMTIMA CABWINO
17. N’ciani cacitika ku cikumbumtima ca anthu ena?
17 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.” (1 Petulo 3:16) Koma ngati anthu apitiliza kunyalanyaza mfundo za Yehova, m’kupita kwa nthawi cikumbumtima cawo cimaleka kuwacenjeza ciliconse. Paulo anakamba kuti cikumbumtima cimeneco cimakhala monga ‘copseleza na citsulo camoto.’ (1 Timoteyo 4:2) Kodi munapyapo kwambili na moto? Mukapya kwambili, pamatsala cipsela moti sipamveka mukakhudzapo. N’cimodzi-modzi na cikumbumtima. Ngati munthu apitiliza kucita voipa, cikumbumtima cake cimakhala “copseleza.” Potsilizila pake, cimalekelatu kuseŵenza.
18, 19. (a) Kodi tikamavutika mumtima mwathu, zingatanthauze ciani? (b) Nanga tingacite ciani ngati tikali kudzimva a mlandu pa macimo amene tinalapa kale?
18 Ngati tivutika mumtima, mwina cikumbumtima cathu cikutiuza kuti tinacita cinthu cosayenela. Izi zikacitika, tiyeni tiyese kupeza cimene tinacita kuti tileke. Tifunika kuphunzilila pa zimene tinalakwitsa kuti tisakabwelezenso. Mwacitsanzo, pamene Mfumu Davide anacimwa, cikumbumtima cake cinam’limbikitsa kulapa. Salimo 51:1-19; 86:5; onani Mfundo ya Kumapeto 7.
Iye anaipidwa na zimene anacita, ndipo anatsimikiza mtima kuti adzayambanso kumvela Yehova. Ndiye cifukwa cake anakamba kuti Yehova ni ‘wabwino ndi wokonzeka kukhululuka.’ —19 Koma anthu ena angamavutikebe mumtima na colakwa cimene anacita kale-kale ndipo analapa. Maganizo amenewa amasautsa kwambili, ndipo angapangitse munthu kudziona kuti ni wopanda pake. Ngati nthawi zina mumamvela conco, kumbukilani kuti madzi akatayika sayoleka, simungasinthe zimene zinacitika kale. Kaya munali kuzindikila bwino-bwino coipa kapena ayi, dziŵani kuti Yehova anakhululuka na mtima wonse, ndipo macimowo anawafafaniza kothelatu. Ndimwe woyela pamaso pa Yehova, ndipo pali pano mumacita zabwino. Mungamadziimbebe mlandu, koma 1 Yohane 3:19, 20.) Izi zitanthauza kuti cikondi ca Mulungu na cikhululuko cake, n’zampamvu cakuti zimatha kuticotsela maganizo odziimba mlandu, kapena manyazi amene tingakhale nawo. Musakaikile olo pang’ono, Yehova anakukhululukilani. Munthu akalandila cikhululuko ca Yehova, cikumbumtima cake cimakhala pamtendele, ndipo amatumikila Mulungu mwacimwemwe.—1 Akorinto 6:11; Aheberi 10:22.
Baibo imati: “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (Ŵelengani20, 21. (a) Kodi buku ino inalembedwa kuti itithandize kucita ciani? (b) Kodi Yehova anatipatsa ufulu wocita ciani? Nanga tiyenela kuuseŵenzetsa bwanji?
20 Buku ino inalembedwa kuti ikuthandizeni kuphunzitsa cikumbumtima canu, kuti cizikucenjezani komanso kukutetezani m’masiku otsiliza ovuta ano. Idzakuthandizaninso kudziŵa moseŵenzetsela mfundo za m’Baibo pa nkhani zosiyana-siyana mu umoyo wanu. Koma si ndiye kuti buku ino idzapeleka malangizo pa nkhani ina iliyonse iyai. Ise timatsatila “cilamulo ca Khristu,” cimene n’cozikidwa pa mfundo za Mulungu. (Agalatiya 6:2) Pa nkhani zimene palibe lamulo lacindunji, sititengelapo mwayi wocita coipa ayi. (2 Akorinto 4:1, 2; Aheberi 4:13; 1 Petulo 2:16) M’malo mwake, timaseŵenzetsa ufulu wathu na kusankha mwanzelu, poonetsa cikondi cathu kwa Yehova.
21 Pamene tisinkha-sinkha pa mfundo za m’Baibo na kuziseŵenzetsa, timaphunzila kugwilitsila nchito ‘mphamvu zathu za kuzindikila.’ (Aheberi 5:14) Tikacita zimenezi, timakhala na cikumbumtima cophunzitsidwa bwino, cimene cidzatitsogolela mu umoyo wathu, na kutithandiza kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.
^ ndime 11 Madokota ambili amati anthu amene ali na vuto la ucakolwa, cimawavuta ngako kuti amwe moŵa mwa saizi. Amati anthu amenewo ni bwino kungolekelatu moŵa.