Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 11

Pambuyo pa Tsiku la Cikwati

Pambuyo pa Tsiku la Cikwati

“Cikondi sicitha.” —1 AKORINTO 13:8.

1, 2. Kodi mavuto m’banja atanthauza kuti cikwati calephela? Fotokozani.

CIKWATI ni mphatso yocokela kwa Yehova. Cimapangitsa munthu kukhala na umoyo wacimwemwe. Ngakhale n’conco, cikwati ciliconse cimakhala na mavuto ake. Ndipo nthawi zina, zingaoneke monga mavutowo sadzasila. Zikakhala conco, mwamuna na mkazi wake sangamvelenso cikondi cija ca poyamba.

2 Koma tisadabwe ngati nthawi zina timakhala na mavuto m’cikwati cathu. Kukhala na mavuto m’banja sikutanthauza kuti cikwati calephela. Ngakhale anthu amene anakhalapo na mavuto aakulu m’cikwati cawo, anapeza njila zobwezeletsa cikondi cawo, na kulimbitsanso cikwati cawo. Motani?

YANDIKILANI MULUNGU, KOMANSO WINA NA MNZAKE

3, 4. Kodi nthawi zina cingacitike n’ciani m’cikwati?

3 Cikwati cimabweletsa pamodzi anthu aŵili osiyana. Aliyense ali na zokonda zake, zimene sakonda, maganizo ake, na kacitidwe kake ka zinthu. Komanso, mwamuna na mkazi wake angakhale ocokela ku mabanja osiyana, mitundu, na zikhalidwe. Zimatenga nthawi kuti aŵiliwo afike podziŵana bwino, na kumvetsetsana bwino-bwino.

4 Koma m’kupita kwa nthawi, aliyense angayambe kusamala kwambili zofuna zake, cakuti angayambe kukanganukana. Zingafike pooneka monga akukhala umoyo wayekha-wayekha. Kodi cingathandize n’ciani kuti alumikizanenso?

Uphungu wa m’Baibo ni wothandiza m’cikwati

5. (a) N’ciani cingathandize Akhristu okwatilana kukhala okondana? (b) Malinga na Aheberi 13:4, tiyenela kuciona bwanji cikwati?

5 Yehova amapeleka mauphungu abwino kwambili amene angakuthandize imwe aŵili kumuyandikila, komanso kuyandikilana wina na mnzake. (Salimo 25:4; Yesaya 48:17, 18) Iye amatiuza kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.” (Aheberi 13:4) Cinthu cimene mumaciona kukhala colemekezeka, cimakhala ca mtengo wapatali. Mumaciteteza na kucisunga bwino. Yehova afuna kuti tiziona cikwati mwa njila imeneyi.

KUKONDA YEHOVA KUNGATHANDIZE CIKWATI CANU

6. Kodi Mateyu 19:4-6 itiuza ciani za mmene Yehova amaonela cikwati?

6 Yehova ndiye anamangitsa cikwati coyamba. Mwana wake, Yesu, anati: “Kodi simunawelenge kuti amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa cifukwa cimeneci mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi’? Cotelo salinso aŵili, koma thupi limodzi. Conco cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” (Mateyu 19:4-6) Kucokela pa ciyambi peni-peni, colinga ca Yehova n’cakuti cikwati cizikhala mgwilizano wa moyo wonse. Amafuna kuti mabanja azikhala ogwilizana, komanso acimwemwe.

7. Kodi mwamuna na mkazi wake angalimbitse bwanji cikwati cawo?

7 Koma masiku ano, mu vikwati mumakhala mavuto ambili kuposa kale lonse. Ndipo mavuto akakula kwambili, ena amaona kuti ni bwino angolekana. Koma kudziŵa mmene Yehova amaonela cikwati kungatithandize.—1 Yohane 5:3.

8, 9. (a) Kodi malangizo a Yehova pa cikwati tiyenela kuyatsatila panthawi ziti? (b) Nanga tingaonetse bwanji kuti cikwati n’cinthu colemekezeka kwa ife?

8 Malangizo a Yehova ni othandiza nthawi zonse. Monga taonela kale, iye amatilangiza kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka.” (Aheberi 13:4; Mlaliki 5:4) Tikatsatila malangizo a Yehova ngakhale pamene n’zovuta, tidzapindula.—1 Atesalonika 1:3; Aheberi 6:10.

9 Popeza cikwati ni cinthu colemekezeka kwa ise, tiyenela kupewa kukamba kapena kucita ciliconse cimene cingauwononge. M’malo mwake, tifuna kuti mgwilizano wathu na mnzathu uzilimbila-limbilako nthawi zonse. Koma tingacite bwanji zimenezi?

LEMEKEZANI CIKWATI CANU MWA ZOCITA ZANU

10, 11. (a) Kodi mu vikwati vina muli mavuto otani? (b) N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi wake afunika kusamala na makambidwe awo?

10 Pali njila zambili zimene munthu angakhumudwitsile mnzake wa m’cikwati. Tidziŵanso kuti si kololeka kwa Mkhristu kumenya mnzake wa m’cikwati, kaya na manja kapena na mawu. Inde, mawu nawo akhoza kukhala cida comenyela munthu. Mkazi wina anati: “Mwamuna wanga amanimenya na mawu. N’zoona kuti nilibe zilonda, koma manyozo ake, monga akuti ‘Nalema nawe!’ kapena ‘Ndiwe wacabe-cabe!’ amasiya zilonda mu mtima mwanga.” Mwamuna wina nayenso anati mkazi wake amam’khumudwitsa nthawi zambili cifukwa ca mitafu yake. Anati: “Siningabweleze pa anthu zimene amanikambila. N’cifukwa cake sinikamba naye, na kufika mocedwa kucokela ku nchito. Ku nchito kumacita kumveka bwino kusiyana n’kunyumba.” Masiku ano, manyozo, mitafu, na kukamba nkhadzulila n’zofala kwambili.

11 Ngati mwamuna na mkazi wake amakonda kutafulilana, zimasiya zilonda mu mtima zimene sizipola msanga. Kunena zoona, Yehova safuna kuti mwamuna na mkazi wake azicitilana zimenezi. Komanso, n’zotheka kukhumudwitsa mnzako wa m’cikwati iwe osadziŵa. Ungaone monga umucitila zabwino, koma kodi iye amamvela bwanji? Mukadziŵa kuti zimene mwakamba zam’khumudwitsa, kodi ndimwe okonzeka kupepesa?—Agalatiya 5:15; ŵelengani Aefeso 4:31.

12. N’ciani cingawononge ubale wa munthu na Yehova?

12 Mmene mumakambila kwa mnzanu wa m’cikwati, kaya ni pamaso pa anthu kapena kuseli, Yehova zimam’khudza. (Ŵelengani 1 Petulo 3:7.) Yakobo 1:26 imatikumbutsa kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.”

13. Kodi wina angakhumudwitse bwanji mnzake wa m’cikwati?

13 Palinso mbali zina zimene okwatilana afunika kusamala. Mwacitsanzo, kodi mnzanu wa m’cikwati angamvele bwanji ngati mumakonda kukambilana kwambili na wina wosiyana naye ziwalo? N’zoona kuti pangakhale cifukwa comveka, monga kum’thandiza mu utumiki, kapena pa vuto lina lake. Koma funso n’lakuti mnzanu amvela bwanji? Mlongo wina anati: “Cimaniŵaŵa kuona kuti mwamuna wanga amapeleka nthawi yambili na cisamalilo kwa mlongo wina. Zimanipangitsa kumvela monga ndine wosafunika kweni-kweni.”

14. (a) Kodi tiphunzilapo ciani pa Genesis 2:24? (b) Kodi tiyenela kudzifunsa ciani?

14 Monga Akhristu, tili na udindo kwa makolo komanso abale na alongo mu mpingo wathu. Koma tikaloŵa m’banja, udindo wathu waukulu umakhala pa mnzathu wa m’cikwati. Yehova anati mwamuna ‘adzadziphatika kwa mkazi wake.’ (Genesis 2:24) Tiyenela kudela nkhawa mmene mnzathu amakhudzidwila. Dzifunseni kuti: ‘Kodi mwamuna wanga, kapena mkazi wanga, nimam’patsa nthawi yokwanila, cisamalilo conse, na cikondi cokwana?’

15. N’cifukwa ciani Akhristu ayenela kupewa kuyandikana kwambili na munthu amene si mnzawo wa m’cikwati?

15 Kukonda kuceza kwambili na wina amene si mnzathu wa m’cikwati, n’kubweletsa vuto m’banja. Tingayambe kukopeka na munthuyo. (Mateyu 5:28) M’kupita kwa nthawi, mungacite cinthu conyozetsa cikwati canu.

‘POGONA PA OKWATILANA PAKHALE POSAIPITSIDWA’

16. Kodi Baibo imalamula ciani za cikwati?

16 Pambuyo pokamba kuti “Ukwati ukhale wolemekezeka,’ Baibo imati: “Pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.” (Aheberi 13:4) Mawu akuti “pogona pa okwatilana” amatanthauza kukhalila malo amodzi kwa mwamuna na mkazi wake. (Miyambo 5:18) Kodi tingapewe bwanji kuipitsa mbali imeneyi ya cikwati?

17. (a) Kodi anthu masiku ano cigololo amaciona bwanji? (b) Nanga Akhristu ayenela kuciona bwanji?

17 Anthu ena saona kuti pali vuto kugona na munthu wina amene sali naye pabanja. Koma ise timakanilatu kutengela maganizo amenewo. Yehova amakambilatu poyela kuti za ciwelewele na cigololo amadana nazo kwambili. (Ŵelengani Aroma 12:9; Aheberi 10:31; 12:29) Kugona na munthu amene sitinakwatilane naye, ndiko kudetsa cikwati cathu. Kumeneko n’kunyozela miyezo ya Yehova, na kuwononga ubale wathu na iye. Conco, tiyenela kupewelatu ciliconse cimene cingatitengele ku cigololo. Inde, kuphatikizaponso maganizo olakwika okhumbila munthu wina—Yobu 31:1.

18. (a) N’cifukwa ciani cigololo cinali colingana na kulambila milungu yonyenga? (b) Nanga Yehova amaciona bwanji cigololo?

18 Mu nthawi ya Aisiraeli pansi pa Cilamulo, cigololo cinali chimo lalikulu kwambili, molingana na kulambila milungu yonyenga. Ndipo zonse ziŵili cilango cake cinali imfa. (Levitiko 20:2, 10) Kodi cigololo cinali colingana bwanji na kulambila mafano? Ngati Mwisiraeli wapezeka kuti walambila mulungu wonyenga, ndiye kuti anaphwanya lonjezo lokhala wokhulupilika kwa Yehova. N’cimodzi-modzinso cigololo. Kunali kuphwanya lonjezo lokhala wokhulupilika kwa mnzake wa m’cikwati. (Ekisodo 19:5, 6; Deuteronomo 5:9; ŵelengani Malaki 2:14.) Inde, cigololo cinali ucimo waukulu kwa Yehova.

19. N’ciani cingatithandize kupewelatu cigololo?

19 Nanga zili bwanji masiku ano? Olo kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose, maganizo a Yehova pa cigololo sanasinthe. Monga mmene sitingalambilile mulungu wonyenga, tisayese kuphwanya lonjezo lokhala wokhulupilika kwa mnzathu wa m’cikwati. (Salimo 51:1, 4; Akolose 3:5) Koma tikaliphwanya, ndiye kuti tanyoza cikwati cathu, komanso Yehova Mulungu.—Onani Mfundo ya Kumapeto 26.

MMENE MUNGALIMBITSILE CIKWATI CANU

20. Kodi nzelu zimapindulitsa bwanji a m’cikwati?

20 Kodi mungacilimbitse bwanji cikwati canu? Mawu a Mulungu amati: “Nzelu zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikila kumacititsa kuti lilimbe kwambili.” (Miyambo 24:3) Nyumba ingakhale yozizila, yothuma, yopanda cinthu, yabwino, komanso yotetezeka. Cikwatinso n’cimodzi-modzi. Munthu wanzelu amacita zotheka kuti cikwati cake cikhale cotetezeka, cokongola, komanso cokondweletsa.

21. Kodi cidziŵitso cingalimbitse bwanji cikwati?

21 Ponena za nyumba ya cikwati, Baibo imatinso: “Kudziŵa zinthu kumacititsa kuti zipinda zamkati mwa nyumba zidzaze ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.” (Miyambo 24:4) Zimene mumaphunzila m’Mawu a Mulungu zingawongolele zinthu m’cikwati canu. (Aroma 12:2; Afilipi 1:9) Mukaŵelenga capamodzi Baibo na zofalitsa zathu, kambilanani za mmene mungagwilitsile nchito zimene mwaphunzila. Pezani njila zoonetselana cikondi na ulemu, komanso kukomelana mtima na kuganizilana. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukulitsa makhalidwe olimbitsa cikwati canu, kuti muzikhala wokondeka kwambili kwa mnzanuyo.—Miyambo 15:16, 17; 1 Petulo 1:7.

Pemphani citsogozo ca Yehova pa kulambila kwa pabanja

22. N’cifukwa ciani tiyenela kuonetsa cikondi na ulemu kwa mnzathu wa m’cikwati?

22 Tiyenela kuyesetsa kuonetsa mwamuna wathu, kapena mkazi, wathu cikondi na ulemu. Pamenepo cikwati cathu cidzakhala cothuma bwino, komanso colimba. Koma coposa zonse, tidzakondweletsa Yehova.—Salimo 147:11; Aroma 12:10.