GAO 13
Kodi Tiyenela Kucita Ciani Kuti Tikondweletse Mulungu?
Pewani zoipa. 1 Akorinto 6:9, 10
Ngati timakonda Yehova, sitidzacita zinthu zimene iye safuna.
Yehova safuna kuti tiziba, tizikolewa, kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo.
Mulungu amadana ndi kupha, kucotsa mimba, kugonana amuna kapena akazi okha-okha. Safuna kuti tikhale adyela kapena andeu.
Sitiyenela kulambila mafano kapena kucita zamizimu.
M’Paladaiso imene idzakhalako padziko lapansi, simudzakhala anthu ocita zoipa.
Mateyu 7:12
Citani zabwino.Kuti tikondweletse Mulungu, tiyenela kuyesa-yesa kukhala ngati iye.
Onetsani cikondi kwa ena mwa kukhala okoma mtima ndi opatsa.
Khalani oona mtima.
Uzani ena za Yehova ndi njila zake.—Yesaya 43:10.
Khalani acifundo ndi okhululuka.