Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 1

Kodi Zipembedzo Zonse Zimaphunzitsa Zoona?

Kodi Zipembedzo Zonse Zimaphunzitsa Zoona?

1. Kodi zina mwa zipembedzo zimene zimapezeka mu Africa n’ziti?

PAFUPI-FUPI aliyense mu Africa amavomeleza kuti kulambila Mulungu ni kofunika. Koma io samagwilizana pankhani ya mmene angalambilile Mulungu. Ena amapita kukalambila kumoski, ena kukacisi wa makolo. Ndipo ena amapita kuchechi. Koma kungakhale kulakwa kuganiza kuti mu Africa muli zipembedzo zitatu cabe. Asilamu amasiyana-siyana malamulo ndi zikhulupililo zao. Zipembedzo za makolo zimasiyana-siyana malinga ndi malo. Machechi amene amati ndi acikristu ni ogaŵikana kwambili. Kuonjezela pa machechi akulu-akulu, mu Africa muli machechi ena ang’ono-ang’ono masauzande amene anacoka m’machechi akulu-akulu.

Timakhala m’Cipembedzo Cifukwa Cakuti Ndi Coona

2. (a) Kodi anthu amasankha kukhala m’zipembedzo zimene alimo pa zifukwa ziti? (b) Kodi ni zifukwa ziti zimene si umboni wakuti Mulungu amakondwela ndi cipembedzo cathu?

2 N’cifukwa ciani anthu ali m’zipembedzo zimene alimo? Anthu ambili amasankha kukhala m’cipembedzo cifukwa cakuti ndi ca makolo ao. Cinanso anthu amakhala m’zipembedzo zimene alimo cifukwa ca zimene zinacitika kale. Buku lakuti The Africans—A Triple Heritage imakamba kuti: “Cisilamu cinafala kumpoto kwa Sahara mwa kugonjetsa adani ake, . . . naco Cikristu cinafala kumwela kwa Sahara m’njila imodzi-modzi. Cisilamu cinafala kumpoto kwa Sahara mwa kugwilitsila nchito lupanga, Cikristu naco cinafala kumwela kwa Sahara mwa kugwilitsila nchito mfuti.” Ngakhale zili conco, ambili a ife timakhulupilila kuti Mulungu amakondwela ndi cipembedzo cathu. Koma cipembedzo sicimakhala coona cabe cifukwa cakuti ndi cimene makolo athu alimo kapena cifukwa cakuti atsamunda anakakamiza makolo athu akale kuloŵamo.

3-5. Kodi ni citsanzo citi cimene cikutithandiza kudziŵa kuti si zipembedzo zonse zimene zimaphunzitsa zoona?

3 Ngakhale kuti zipembedzo zonse zimanena kuti zili ndi malangizo odalilika olambilila Mulungu, zikhulupililo zao zimasiyana. Zipembedzo zimenezi zimaphunzitsa zinthu zosiyana-siyana ponena za Mulungu ndi zimene iye amafuna kwa ife. Ganizilani izi: Tinene kuti mwaloŵa nchito pakampani ina yaikulu. Tsiku loyamba kugwila nchito, mwamva kuti abwana anu ali pachuti. Ndiyeno mufunsa anthu atatu ogwila nchito pamenepo zimene muyenela kucita. Woyamba akuuzani kuti abwana afuna kuti mupyange. Waciŵili akuuzani kuti mupente nyumba ili pakampanipo. Ndipo wacitatu akuuzani kuti mupeleke makalata.

4 Pambuyo pake, mufuna kudziŵa kuti abwana anu ni munthu wabwanji. Woyamba akuuzani kuti abwana ndi atali, acicepele ndi oipa mtima. Waciŵili akuuzani kuti ndi afupi, acikulile ndi abwino mtima. Wacitatu akuuzani kuti iyai abwana si amuna koma ndi akazi. Inu mudzadziŵa kuti anthu atatu ameneo sakukamba zoona. Ngati mufuna kupitiliza nchito, mudzafunsa-funsa kuti muŵadziŵe abwana anu ndi zimene afuna kuti inu mucite.

5 N’cimodzi-modzi pankhani ya cipembedzo. Cifukwa cakuti pali zikhulupililo zosiya-siyana ponena za Mulungu ndi zimene iye amafuna kwa ife, tiyenela kutsimikiza kuti njila imene timalambilila ndi yoona. Koma kodi tingadziŵe bwanji zoona ponena za Mulungu?