MBALI 7
Kodi Amene Ali m’Cipembedzo Coona Ndani?
1. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikondweletse Mulungu?
KUTI Mulungu akhale mnzathu wa pamtima, tiyenela kupewelatu cipembedzo conama. Tiyenela kukhala m’cipembedzo coona. Masiku ano padziko lonse lapansi pali anthu mamiliyoni amene ali m’cipembedzo coona.
2. Kodi anthu amene amapanga gulu la Mboni za Yehova amacokela kuti, nanga nchito yao ni yabwanji?
2 Monga mmene Baibo inakambilatu, olambila oona ndi “khamu lalikulu” limene lacokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu ulionse, ndi cinenelo ciliconse.” (Chivumbulutso 7:9) M’maiko 236, Mboni za Yehova mamiliyoni zikuthandiza anthu kuphunzila za njila zacikondi za Yehova ndi zofuna zake.
Kudziŵa Olambila Oona
3. Kodi Mboni zimalambila ndani, ndipo ni mitundu ya kulambila iti imene zimapewa?
3 Mboni zimadziŵa kuti Yehova yekha ndiye ayenela kulambilidwa. Iwo sagwadila mafano kapena zithunzi-thunzi. (1 Yohane 5:21) Salemekeza akufa mwa kucezela pa malilo kapena kucita miyambo imene imalimbikitsa zikhulupililo zonama ndi “ziphunzitso za ziŵanda.” (1Timothy 4:1) Koma amatonthoza ofedwa mwa kuwafotokozela zimene Mulungu alonjeza kuti adzaukitsa akufa m’paladaiso padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
4. Kodi anthu a Mulungu amaona bwanji za matsenga?
4 Mboni sizimacita za matsenga ngakhale pang’ono, kapena ufiti, cifukwa zimadziŵa kuti zinthu zimenezi zicokela kwa Mdyelekezi. Sizimakhulupilila kuti matsenga angawachinjilize koma amakhulupilila Yehova.—Miyambo 18:10.
5. Kodi a Mboni za Yehova “sali mbali ya dziko” m’njila yabwanji?
5 Yesu anakamba kuti ophunzila ake “sali mbali ya dziko.” (Yohane 17:16) Yesu anakana kuloŵa m’ndale. (Yohane 6:15 ) N’cimodzi-modzi ndi Mboni. Izo sizimaloŵa m’ndale, kukweza dziko limene zimakhala, ndipo zimapewa tsankho limene lili m’dziko. Ngakhale zili conco, zimapeleka misonkho ndipo zimamvela malamulo a m’dziko limene zimakhala.—Yohane 15:19; Aroma 13:1, 7.
6. Kodi atumiki a Mulungu amatsatila mfundo zanji pankhani ya cikwati ndi kulekana?
6 Popeza kuti zimamvela malamulo a boma, Mboni zimaonetsetsa kuti zalembetsa cikwati cao kuboma. (Tito 3:1) Zimamvela malamulo a Mulungu, ndipo sizikwatila mphali. (1 Timoteyo 3:2) Ndiponso, popeza kuti atumiki a Mulungu amatsatila mfundo za m’Baibo pa umoyo wao, zikwati zao sizimatha kaŵili-kaŵili.
7. Kodi Mboni zimakondana bwanji?
7 Mboni zimakondana. Cikondi cimeneci, kuphatikizapo cikondi cao pa Mulungu, ndi cimene cimazigwilizanitsa capamodzi kupanga gulu la abale eni-eni. Cikondi cimeneci cimazigwilizanitsa ngakhale kuti izo zimacokela m’mitundu ndi m’maiko osiyana-siyana. Ngati kwacitika tsoka kapena ngati ena akumana ndi mavuto, Mboni sizimacedwa kuthandizana. Mboni zimaonetsa cikondi pa umoyo wao wonse.—Yohane 13:35.
8. Kodi anthu a Mulungu samacita zoipa ziti?
8 Anthu a Yehova amayesa-yesa kukhala anthu oona mtima ndi abwino. Samaba, sanama, sacita zaciwelewele, saledzela, ndipo sacita cinyengo pamalonda. Amuna samenya akazi ao. Akalibe kukhala Mboni, ena anali kucita zinthu zimenezi, koma Yehova anawathandiza kuleka kucita zimenezi. Iwo ‘anasambitsidwa kukhala oyela’ m’maso mwa Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11.
Amene Amacita Cifunilo ca Mulungu
9. Kodi buku lina linakamba ciani za machechi amizimu mu Africa?
9 Ni zoona kuti zipembedzo zambili zimakamba
kuti zili ndi coonadi. Izo zimanena kuti nchito zodabwitsa zimene zimacita ndi umboni wa zimenezi. Mwacitsanzo, pofotokoza za machechi amizimu mu Africa, buku lina limakamba kuti: “Amene maka-maka amacita nchito ya wamatsenga kapena sing’anga lelo ni [magulu atsopano a Cikristu]. . . . Iwo amati amalosela ndi kucita zozizwitsa. Aneneli ao amaona masomphenya ndi kumasulila maloto. Amagwilitsila nchito madzi oyela, mafuta opatulika, phulusa, makandulo ndi lubani pocilitsa ndi pochinjiliza anthu ku matenda.”10, 11. N’cifukwa ciani zimene anthu amaganiza kuti n’zozizwitsa si umboni wakuti cipembedzo cao cimacokela kwa Mulungu?
10 Anthu a m’zipembedzo zimenezi amakamba kuti zozizwitsa zimene amacita ni umboni wakuti cipembedzo cao ni codalitsidwa ndi Mulungu. Koma zimene amaganiza kuti ni zozizwitsa si umboni wakuti Yehova amavomeleza cipembedzo cao. Satana amapatsa anthu ena, amene kulambila kwao ni konama, mphamvu yocita ‘nchito zamphamvu.’ (2 Atesalonika 2:9) Ndiponso, Baibo inakambilatu kuti mphatso yocokela kwa Mulungu yocita zozizwitsa monga kunenela, kulankhula malilime, ndi kukhala ndi cidziŵitso capadela, “idzatha.”—1 Akorinto 13:8.
11 Yesu anacenjeza kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzaloŵa ufumu wakumwamba iyai, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba. Ambili adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosele m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziŵanda m’dzina lanu, ndiponso kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziŵani ngakhale pang’ono! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu.”—Mateyu 7:21-23.
12. Ndani amene adzaloŵa Ufumu wakumwamba?
12 Nanga ndani amene adzaloŵa Ufumu wakumwamba? Ndi anthu okha amene amacita cifunilo ca Yehova.
Alaliki a Ufumu wa Mulungu
13. Kodi ndi nchito iti imene Mulungu walamula anthu ake kucita masiku ano, nanga amene akuicita ndani?
13 Kodi cifunilo ca Mulungu kamba ka anthu ake masiku ano n’ciani? Yesu anakamba kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Imenei ndi nchito imene Mboni za Yehova zikucita mwacangu.
14. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani, nanga ni ndani amene adzalamulila mu Ufumu umeneo?
14 “Padziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” Mboni za Yehova zimalalikila kuti Ufumu wa Mulungu ni boma lakumwamba limene lidzalamulila dziko lonse lapansi mwacilungamo. Zimaphunzitsa kuti Yehova waika Kristu Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu umeneo, pamodzi ndi olamulila anzake a 144,000 amene anasankhidwa pakati pa anthu.—Danieli 7:14, 18; Chivumbulutso 14:1, 4.
15. Kodi Ufumu wa Mulungu udzaononga ciani?
15 Mboni zimaseŵenzetsa Baibo kuonetsa anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzaononga dziko lonse la Satana. Naco cipembedzo conama pamodzi ndi ziphunzitso zake zimene sizimalemekeza Mulungu koma zimalemekeza Mdyelekezi, cidzaonongedwa. (Chivumbulutso 18:8) Nao maboma onse a anthu amene amatsutsa Mulungu adzaonongedwa.—Danieli 2:44.
16. Kodi Kristu Yesu adzalamulila ndani, nanga anthu amenewa adzakhala kuti?
16 Ndiponso, Mboni za Yehova zimaphunzitsa anthu kuti Kristu Yesu adzadalitsa anthu onse amene amacita zimene Mulungu afuna. Iye adzalamulila anthu amenewa pano padziko lapansi. Baibo imalonjeza kuti: “Adzalanditsa wosauka wofuulila thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.”—Salimo 72:12, 13.
17. Kodi ni andani cabe amene amalalikila za Ufumu wa Mulungu?
17 Kulibe gulu lina, kusiyapo Mboni za Yehova, limene limacita cifunilo ca Mulungu mwa kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Ni Mboni za Yehova cabe zimene zimaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi.