NKHANI 1
Kodi Mulungu N’ndani?
1, 2. Kodi anthu amakonda kufunsa mafunso abwanji?
ANA amakonda kufunsa mafunso ambili. Angafunse kuti, ‘ici n’ciani?’ Ungotsiliza kuyankha udzamva, nanga ici, uyu n’ndani, cifukwa ciani? Mulimonse mmene ungayankhile bwino, adzafunsabe kuti, ‘Cifukwa ciani?’
2 Ife tonse timakonda kufunsa mafunso. Tingafunse zakuti tidzadya ciani, tidzavala ciani kapena tidzagula ciani. Timakhalanso ndi mafunso pa nkhani zikulu, monga za umoyo ndi tsogolo lathu. Koma ngati sitipeza mayankho okhutilitsa, tingagwe ulesi ndi kuleka kufuna-funa mayankho.
3. N’cifukwa ciani anthu ambili amaganiza kuti sangapeze mayankho pa mafunso ofunika kwambili?
3 Kodi Baibulo ili ndi mayankho pa mafunso ofunika amene tingakhale nawo? Anthu ena angaganize conco, koma amaona kuti Baibulo ni buku yovuta kuimvetsetsa. Amaganiza kuti amene amadziŵa mayankho amenewo ni alaliki kapena abusa. Ndipo pali ena amene amacita manyazi kuvomeleza kuti sadziŵa mayankho pa mafunso amenewo. Nanga inu muganiza bwanji?
4, 5. Ni mafunso ofunika ati amene muli nawo? N’cifukwa ciani simuyenela kuleka kufuna-funa mayankho?
4 Mwina inu mumafuna mayankho pa mafunso monga aya: Kodi colinga ca moyo wanga n’ciani? Nanga nikafa n’dzayenda kuti? Kodi Mulungu n’ndani maka-maka? Yesu, mphunzitsi wochuka anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani.” (Mateyu 7:7) Musaleme kufuna-funa mpaka mukapeze mayankho okhutilitsa.
5 Inde, ‘mukapitiliza kufunafuna,’ mudzapeza mayankho Miyambo 2:1-5) Ndipo mayankho ake ni osavuta kuwamvetsetsa. Cifukwa ca zimene mudzaphunzila, mudzakhala okondwela pali pano, ndipo mudzakhala ndi ciyembekezo ca tsogolo labwino. Lomba tiyeni tikambilane funso limene anthu ambili amavutika nalo maganizo.
m’Baibulo. (KODI MULUNGU AMATIDELA NKHAWA KAPENA NI WANKHANZA?
6. N’cifukwa ciani anthu ena amaganiza kuti Mulungu sawadela nkhawa?
6 Anthu ambili amaona kuti Mulungu satidela nkhawa. Amati sembe Mulungu amatidela nkhawa, dziko siikanakhala mmene ilili conco. Kulikonse timangoona nkhondo, anthu kuzondana, ndi mavuto ambili-mbili. Tikanena za matenda, kuvutika, ndi imfa, ndiye zosacita kukamba. Conco, anthu pothedwa nzelu amafunsa kuti, ‘Ngati n’zoona kuti Mulungu amatidela nkhawa, n’cifukwa ciani sacotsapo mavuto onsewa?’
7. (a) Kodi abusa apangitsa bwanji anthu kuganiza kuti Mulungu ni wankhanza? (b) Tidziŵa bwanji kuti Mulungu sindiye amacititsa zinthu zoipa?
7 Nthawi zina, abusa azipembedzo ni amene amapangitsa anthu kuganiza kuti Mulungu ni wankhanza. Pakacitika cinthu coipa kwambili, iwo amati ni cifunilo ca Mulungu. Pamene akamba conco, m’ceni-ceni amaimba Mulungu mlandu. Koma Baibulo imaphunzitsa kuti si Mulungu amene amacititsa mavuto. Pa Yakobo 1:13 timaŵelenga kuti Mulungu sayesa munthu ndi zinthu zoipa. Ndipo: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Izi zitanthauza kuti, ngakhale kuti Mulungu saletsa zinthu zoipa kucitika, sindiye amazicititsa. (Ŵelengani Yobu 34:10-12.) Tiyeni tikambe mwa citsanzo.
8, 9. N’cifukwa ciani n’kulakwa kupatsa Mulungu mlandu wa mavuto amene timakumana nawo? Pelekani citsanzo.
Luka 15:11-13) N’cimodzi-modzi ndi Mulungu. Iye sanawaletse anthu pamene anasankha kum’pandukila ndi kucita zoipa. Conco, pakacitika zinthu zoipa, tizikumbukila kuti si Mulungu amene wapangitsa. Kupatsa Mulungu mlandu n’kumulakwila kwambili.
8 Tiyelekezele kuti mwana wacinyamata akhala pakhomo pa makolo ake. Atate wake amamukonda kwambili, cakuti anam’phunzitsa mmene angapangile zosankha mwanzelu. Koma tsiku lina mwana uyu apandukila makolo ndi kucoka panyumba. Kumene wayenda uko, ayamba kucita zinthu zoipa, mpaka kugwela m’mavuto akulu. Kodi mungaimbe mlandu atate wake, cifukwa sanamuletse kucoka pa nyumba? Iyai. (9 Pali cifukwa cabwino kwambili cimene Mulungu saletsela zoipa kucitika. Mu Nkhani 11, mudzaphunzila zimene Baibulo imakamba pa nkhani imeneyi. Koma cimene muyenela kudziŵa n’cakuti Mulungu amatikonda, ndipo sindiye amabweletsa mavuto amene amatigwela. Ndiponso, ni Mulungu cabe amene angacotsepo mavuto onse.—Yesaya 33:2.
10. N’ciani cimatipatsa citsimikizo cakuti Mulungu adzakonza zonse zimene anthu oipa awononga?
10 Mulungu ni woyela. (Yesaya 6:3) Ndipo zonse zimene amacita n’zacilungamo, n’zoyela, ndipo n’zabwino. Conco tiyenela kumudalila. Anthu sitingawadalile kweni-kweni cifukwa nthawi zina amacita zoipa. N’zoona kuti pali olamulila ena amene amayesa kukhala oona mtima. Koma ngakhale iwo alibe mphamvu zocotsela mavuto onse amene anthu amacititsa. Palibe aliyense ali ndi mphamvu monga za Mulungu. Iye adzakonza zonse zimene anthu oipa awononga. Inde, adzacotsapo zoipa zonse kwamuyaya.—Ŵelengani Salimo 37:9-11.
KODI MULUNGU AMAMVELA BWANJI NGATI ANTHU AVUTIKA?
11. Kodi Mulungu amamvela bwanji ngati inu muvutika?
11 Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona zimene zicitika m’dziko, ndi mavuto amene inu mumakumana nawo? Baibulo imatiphunzitsa kuti Mulungu “amakonda cilungamo.” (Salimo 37:28) Iye amakondwela ndi zabwino, koma amakhumudwa ndi zoipa. Conco, cimamuŵaŵa kwambili akaona anthu avutika. Mwacitsanzo, Baibulo imakamba kuti pamene Mulungu anaona kuti zoipa zinaculuka m’dziko m’nthawi yakale, “zinam’pweteka kwambili mumtima.” (Genesis 6:5, 6) Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Ndipo Baibulo imatiuza kuti Mulungu amasamala kwambili za ife.—Ŵelengani 1 Petulo 5:7.
12, 13. (a) Kodi cikondi tinakhala naco bwanji? Nanga timamvela bwanji tikaona mavuto m’dziko? (b) N’cifukwa ciani tili otsimikiza kuti Mulungu adzacotsapo mavuto onse ndi zoipa zonse?
12 Baibulo imatiuzanso kuti Mulungu anatilenga m’cifanizilo cake. (Genesis 1:26) Ici citanthauza kuti Mulungu anatilenga ndi makhalidwe abwino amene iye ali nawo. Conco, ngati cimakuŵaŵani mukaona kuti munthu amene alibe cifukwa avutikilamo, kumbukilani kuti Mulungu ni amene cimamuŵaŵa kwambili. Nanga timadziŵa bwanji zimenezi?
13 Baibulo imatiphunzitsa kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Mwa ici, ciliconse cimene amacita, amacicita cifukwa ca cikondi. Conco, timakwanitsa kukonda anthu ena cifukwa Mulungu anaika cikondi mwa ife potilenga. Ganizilani ici: Sembe kuti inu munali ndi mphamvu zokwanitsa kucotsapo mavuto onse pa dziko lapansi, ndi zoipa zonse, kodi simukanazicotsapo? N’zosacita kufunsa, cifukwa mumakonda anthu. Ndiye kuli bwanji Mulungu? Iye ni wamphamvu zonse, ndipo amatikonda kwambili. Sitikaikila olo pang’ono, kuti iye adzacotselatu mavuto onse ndi zoipa zonse. Dziŵani kuti malonjezo onse amene achulidwa kuciyambi kwa buku ino adzakwanilitsidwa. Koma kuti mukhulupilile malonjezo amenewa, pali zambili zimene mufunika kudziŵa za Mulungu.
MULUNGU AMAFUNA KUTI MUM’DZIŴE BWINO
14. Dzina la Mulungu n’ndani? Ndipo timadziŵa bwanji kuti tifunika kumachula dzina limeneli?
14 Ngati mufuna kuti munthu wina akhale mnzanu, kodi mumayamba kumuuza ciani? Dzina lanu, si conco? Kodi Mulungu ali ndi dzina? Machalichi ambili amakamba kuti dzina lake ni Mulungu kapena Ambuye. Koma amenewa si maina ake eni-eni iyai. Ni maina a udindo cabe kapena aulemu, monga maina akuti “mfumu” ndi “pulezidenti.” Mulungu mwini-wake amatiuza kuti dzina lake ni Yehova. Pa Salimo 83:18 timaŵelenga kuti: ‘Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, pa dziko lonse lapansi.’ Olemba Baibulo analemba dzina la Mulungu masauzande angapo. Ici cionetselatu kuti Yehova amafuna kuti inu mudziŵe dzina lake ndi kumalichula. Wakuuzani dzina lake cifukwa amafuna kuti mukhale bwenzi lake.
15. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza ciani?
15 Dzina la Mulungu lakuti Yehova lili ndi tanthauzo lofunika kwambili. Limatanthauza kuti Mulungu amakwanilitsa lonjezo lililonse limene amapanga, ndi kuti amakwanilitsa colinga cake. Palibe aliyense ayenela kuchulidwa ndi dzina limeneli, ni la Yehova yekha cabe. *
16, 17. Fotokozani tanthauzo la maina audindo aya: (a) “Wamphamvuyonse,”(b) “Mfumu yamuyaya,”(c) “Mlengi.”
Salimo 83:18 imakamba kuti: “Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba.” Pa Chivumbulutso 15:3 timaŵelenganso kuti: “Nchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njila zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya.” Kodi dzina laudindo lakuti “Wamphamvuyonse” limatanthauza ciani? Limatanthauza kuti Yehova ni wamphamvu kwambili kuposa aliyense m’cilengedwe conse. Ndipo dzina laudindo lakuti “Mfumu yamuyaya” limatanthauza kuti iye wakhala alipo kucokela muyaya. Salimo 90:2 imakamba kuti iye ni Mulungu kucokela muyaya mpaka muyaya. Kodi si zocititsa cidwi zimenezi?
16 Ponena za Yehova,17 Yehova yekha ndiye Mlengi. Pa Chivumbulutso 4:11 pamati: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Zoona, Yehova ndiye analenga zinthu zonse zimene mungaganizile monga angelo, nyenyezi, zipatso, nsomba, ndi zina zonse.
KODI INU MUNGAKHALE BWENZI LA YEHOVA?
18. N’ciani cimapangitsa anthu ena kuona kuti sizingatheke kuti akhale bwenzi la Mulungu? Koma Baibulo imakamba ciani pa nkhaniyi?
18 Anthu ena akaŵelenga za makhalidwe apamwamba a Yehova, amacita mantha ndi kuganiza kuti: ‘Ngati Mulungu ni wamphamvu conco, wolemekezeka kwambili, ndipo amakhala kutali-tali kumwamba, ndine ndani ine kuti aniganizile!’ Koma kodi Mulungu afuna kuti tizimuona conco? Kutali-tali! Yehova afuna kukhala pafupi ndi ife. Baibulo imakamba kuti “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Mulungu afuna kuti mumuyandikile, ndipo analonjeza kuti “iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.
19. (a) Mungacite ciani kuti mukhale bwenzi la Mulungu? (b) Pa makhalidwe a Yehova, ni ati amene mukondapo kwambili?
19 Mungacite ciani kuti mukhale bwenzi la Mulungu? Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khiristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Mukapitiliza kuphunzila Baibulo, mudzamudziŵa bwino Yehova ndi Yesu. Pambuyo pake mudzalandila moyo wosatha. Taphunzila kale kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:16) Koma iye alinso ndi makhalidwe ena okondweletsa kwambili. Baibulo imatiuza kuti Yehova ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Ekisodo 34:6) Yehova ni ‘wabwino ndipo ni wokonzeka kukhululuka.’ (Salimo 86:5) Mulungu ni woleza mtima ndi wokhulupilika. (2 Petulo 3:9; Chivumbulutso 15:4) Mudzadziŵa zambili za makhalidwe ake abwino mwa kuŵelenga za iye m’Baibulo.
20-22. (a) Kodi zingatheke bwanji kukonda Mulungu amene sitimuona? (b) Mudzacita ciani ngati anthu ena ayesa kukuletsani kuphunzila Baibulo?
Yohane 1:18; 4:24; 1 Timoteyo 1:17) Pamene muŵelenga za Yehova m’Baibulo, mudzafika pom’dziŵa bwino ngati kuti mumuona. (Salimo 27:4; Aroma 1:20) Pamene mudziŵa zambili za Yehova, cikondi canu pa iye cidzakulilako-kulilako, mpaka mudzakhala naye pafupi kwambili.
20 Koma mungakhale bwanji pa ubwenzi ndi Mulungu amene simuona? (21 Yehova alidi Atate wathu. (Mateyu 6:9) Ndiye anatipatsa moyo, ndipo amatifunila umoyo wabwino. N’zimene tate aliyense wacikondi amafunila ana ake. (Salimo 36:9) Inde, Baibulo imatiphunzitsa kuti ngakhale inu mungakhale bwenzi la Yehova. (Yakobo 2:23) Ganizabe cabe zimenez! Yehova, Mlengi wacilengedwe conse, afuna mukhale bwenzi lake!
22 Koma pali anthu ena amene angayese kukuletsani kuphunzila Baibulo. Amaopa kuti mungacoke ku cipembedzo canu. Musalole kuti munthu wina akulepheletseni kukhala bwenzi la Yehova. Mulungu ndiye Bwenzi labwino kupambana wina aliyense.
23, 24. (a) N’cifukwa ciani tikuti musaleke kufunsa mafunso? (b) Tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila??
23 Pamene muphunzila Baibulo, mudzapeza zinthu zina zimene simudzamvetsetsa. Osacita manyazi kufunsa kapena kupempha ena kuti akuthandizeni. Yesu anakamba kuti tizikhala odzicepetsa monga ana ang’ono. (Mateyu 18:2-4) Paja ana amafunsa mafunso ambili-mbili. Mulungu amafuna kuti mupeze mayankho pa mafunso anu. Conco, phunzilani Baibulo mwakhama, pofuna kutsimikiza kuti zimene muphunzila ni coonadi.—Ŵelengani Machitidwe 17:11.
24 Kuphunzila Baibulo ndiye njila yabwino kwambili yodziŵila Yehova. M’nkhani yotsatila, tidzaona cifukwa cake Baibulo ni yosiyana kwambili ndi mabuku ena onse.
^ ndime 15 Ngati m’Baibulo yanu mulibe dzina lakuti Yehova, kapena ngati mufuna kudziŵa zambili pa tanthauzo la dzina la Mulungu ndi kachulidwe kake, onani Zakumapeto 1.