NKHANI 22
Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi
1, 2. (a) N’cifukwa ciani nthawi zina tingayambe kuganiza kuti ciyembekezo ca Paladaiso ndi loto cabe? (b) N’ciani cingatithandize kukhulupilila kwambili malonjezo a Mulungu?
TAYELEKEZELANI kuti mwaona m’bale wokhulupilika amene wafika pa misonkhano, ndipo ndi wotopa kwambili. Iye akuvutika maganizo cifukwa ca zinthu zoipa zimene bwana wake wamucitila ku nchito. Komanso ali ndi nkhawa cifukwa ca mavuto amene akukumana nao posamalila banja lake ndiponso cifukwa ca kudwala kwa mkazi wake. Pamene nyimbo yotsegulila misonkhano iyamba, m’baleyo akulimbikitsidwa, ndipo akusangalala cifukwa cokhala ndi abale ndi alongo ake pa Nyumba ya Ufumu. Nyimboyo ndi yokhudza ciyembekezo ca Paladaiso. Mau a m’nyimboyo akumulimbikitsa kuganizila mmene umoyo udzakhalila m’Paladaiso ndi kudziyelekezela kuti walowamo kale. M’baleyu amaikonda kwambili nyimboyi moti pamene akuimba pamodzi ndi banja lake, mtima wake ukukhala m’malo cifukwa ca ciyembekezo ca moyo wa m’Paladaiso.
2 Kodi inunso munamvapo conco nthawi ina? Ambili a ife tinamvapo conco. Komabe, cifukwa ca mavuto amene timakumana nao m’dziko loipali, nthawi zina tingayambe kuganiza kuti ciyembekezo ca Paladaiso ndi loto cabe. Tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta,’ ndipo dzikoli lafika poipa kwambili. (2 Tim. 3:1) N’ciani cingatithandize kuona ciyembekezo ca Paladaiso kukhala ceniceni? Nanga timadziŵa bwanji kuti posacedwapa Ufumu wa Mulungu udzalamulila anthu onse? Tiyeni tikambilane maulosi a Yehova ocepa cabe amene anthu ake anaona akukwanilitsidwa m’nthawi zakale. Ndiyeno tikambilananso mmene maulosi amenewo ndiponso maulosi ena akukwanilitsidwila masiku ano. Pambuyo pake tionanso mmene maulosi amenewo adzakwanilitsidwila mtsogolo.
Mmene Yehova Anakwanilitsila Malonjezo Ake m’Nthawi Zakale
3. Ndi lonjezo liti limene linalimbikitsa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo?
3 Taganizilani za umoyo wa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo m’zaka za m’ma 500 B.C.E. Ambili a io anakulila ku ukapolo pamodzi ndi makolo ao, ndipo umoyo unali wovuta kwambili kumeneko. Ababulo anali kuwanyoza cifukwa cakuti anali kukhulupilila Yehova. (Sal. 137:1-3) Pamene anali ku ukapolo, Ayuda okhulupilika anali ndi cikhulupililo colimba cakuti Yehova adzawabweza ku dziko lao. Yehova anali atawalonjeza kuti zinthu zidzakhala bwino akadzabwelela ku dziko lao. Iye anawauza kuti zinthu ku Yuda zidzakhala bwino monga mmene zinalili m’munda wa Edeni kapena kuti m’Paladaiso. (Ŵelengani Yesaya 51:3) Powauza malonjezo amenewo, Mulungu anafuna kulimbitsa cikhulupililo ca anthu ake. Kodi malonjezowo anawalimbikitsa bwanji? Tiyeni tikambilane ena a malonjezo amenewo.
4. Kodi Yehova anawatsimikizila bwanji Ayuda kuti adzakhala otetezeka m’dziko la kwao?
4 Citetezo. Ayuda anayenela kubwelela ku dziko lao lakutali limene linali la bwinja kwa zaka 70. Ndipo ndi ocepa cabe amene anali kulidziŵa dzikolo. M’nthawi zakale, mikango, zimbalongondo, akambuku ndi zinyama zina zoopsa zinali zofala kwambili. Mwacionekele, amuna okwatila anali kudela nkhawa kuti adzateteza bwanji akazi ndi ana ao. Analinso kudela nkhawa kuti adzateteza bwanji ziweto zao monga nkhosa ndi ng’ombe. Nkhawa imeneyo inali yomveka. Komabe, ganizilani za lonjezo la Mulungu lopezeka pa Yesaya 11:6-9. (Ŵelengani.) Kenako ganizilani mmene lonjezolo linatonthozela anthu a Mulungu. Mwa mau olembedwa mwandakatulo amenewo, Yehova anatsimikizila anthu ake amene anali ku ukapolowo kuti adzakhala otetezeka pamodzi ndi ziŵeto zao. Mkango unali kudzadya udzu mlingalilo lakuti sukanadya ng’ombe za Ayuda. Anthu okhulupilika amenewo sanafunikile kuopa nyama iliyonse yolusa. Yehova analonjeza kuti anthu ake adzakhala otetezeka akadzabwelela ku Yuda, kaya poyenda m’cipululu kapena m’thengo.—Ezek. 34:25.
5. Ndi maulosi ati amene anathandiza Ayuda amene anali ku ukapolo kukhulupilila kuti Yehova adzawapatsa zinthu zambili zofunikila?
5 Zinthu zoculuka. Koma Ayuda ayenela kuti analinso ndi nkhawa zina, ndipo anali kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndidzadyetsa bwanji banja langa ndikabwelela kwathu? Nanga tizikakhala kuti? Kodi tizikagwila nchito yanji? Kodi idzakhala nchito yabwino kuposa nchito yotopetsa imene tikugwila kuno ku ukapolo?’ Yehova anayankha mafunso onsewa kudzela m’maulosi ake ouzilidwa. Iye analonjeza kuti mvula izidzagwa bwino kwambili m’dzikolo, ndipo “zokolola za munthakayo zidzakhala cakudya copatsa thanzi” ndiponso coculuka. (Yes. 30:23) Ponena za malo okhala ndi nchito, Yehova anapelekanso lonjezo lina lokhudza anthu ake. Iye anati: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabyala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabyala wina n’kudya.” (Yes. 65:21, 22) Ndithudi, io anali kudzakhala ndi umoyo wabwino ku Yuda mosiyana ndi mmene anali kukhalila ku ukapolo ku Babulo. Nanga bwanji za mavuto ao aakulu amene anawapangitsa kuti apite ku ukapolo?
6. Ndi matenda otani amene anthu a Mulungu anali kudwala kwa nthawi yaitali? N’ciani cimene Yehova anatsimikizila Ayuda amene anali kubwelela kwao kucoka ku ukapolo?
6 Umoyo wabwino wa kuuzimu. Anthu a Mulungu anali atafooka mwakuuzimu zaka zambili asanapite ku ukapolo. Kudzela mwa mneneli wake Yesaya, Yehova anati: “Mutu wanu uli ndi zilonda zokhazokha, ndipo mtima wanu wafooka.” (Yes. 1:5) Iwo anali akhungu ndi ogontha mwakuuzimu cifukwa anali atasiya kumvela malangizo a Yehova, komanso sanali kufuna kuona kuwala kwa kuuzimu. (Yes. 6:10; Yer. 5:21; Ezek. 12:2) Ngati anthu omwe anabwelako ku ukapoloko akanakhalanso akhungu ndi ogontha mwakuuzimu, kodi tsogolo lao likanakhala lotani? Kodi Yehova akanawayanja? Mau a Yehova ayenela kuti anawakhazika mtima pansi. Iye anati: “M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mau a m’buku. Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.” (Yes. 29:18) Ndithudi, Yehova anali kudzacilitsa anthu ake omwe analapa pambuyo pozindikila kulakwa kwao. Iye anali kudzawapatsa malangizo opatsa moyo ndi othandiza malinga ngati io anali kudzapitilizabe kukhala omvela.
7. Kodi zimene Mulungu analonjeza anthu ake amene anali ku ukapolo zinakwanilitsidwa bwanji? N’cifukwa ciani zimenezi ziyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu?
7 Kodi Yehova anakwanilitsa malonjezo ake? Yankho tingalipeze tikaona zimene zinacitika. Pamene Ayuda anabwelela kwao, Mulungu anali kuwateteza, kuwapatsa zinthu zoculuka, ndipo anali ndi umoyo wabwino wa kuuzimu. Mwacitsanzo, Yehova anawateteza kwa anthu a mitundu ina amene anali amphamvu ndi oculuka kuposa io. Nyama za kuchile sizinaononge ziweto za Ayuda. N’zoona kuti Ayudawo anaona kukwanilitsidwa kocepa cabe kwa maulosi okhudza paladaiso amene anenedwelatu ndi anthu monga Yesaya, Yeremiya, ndi Ezekieli. Koma zinthu zocepa zimene Ayudawo anaona panthawiyo, zinawalimbikitsa kwambili. Tikamaganizila zimene Yehova anacitila anthu ake m’nthawi zakale, cikhulupililo cathu cimalimba kwambili. Maulosi amene anakwanilitsidwa poyamba anali olimbikitsa kwambili ngakhale kuti anacitika pamlingo wocepa. Motelo, maulosiwa akadzakwanilitsidwa pa mlingo waukulu tidzalimbikitsidwa koposa. Taonani zimene Yehova akuticitila masiku ano.
Mmene Yehova Akukwanilitsila Malonjezo Ake Masiku Ano
8. Kodi anthu a Mulungu akusangalala kukhala ‘m’dziko’ lotani?
8 Anthu a Yehova sapanga mtundu umodzi masiku ano, ndipo sakhala m’dziko limodzi. Koma Akristu odzozedwa ndi amene amapanga mtundu umodzi wakuuzimu, umene umachedwa “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Ndipo anzao a “nkhosa zina” amagwilizana ndi odzozedwa amenewa ‘m’dziko’ lao limene ndi malo ao ogwilila nchito padziko lapansi kuti alambile Yehova Mulungu mogwilizana. Kulambila Mulungu ndiye cinthu cacikulu pa umoyo wao. (Yoh. 10:16; Yes. 66:8) Nanga ndi “dziko” lotani limene Yehova watipatsa? Watipatsa paladaiso wakuuzimu. M’paladaiso ameneyu, takhala tikuona kukwanilitsidwa kwa kuuzimu kwa malonjezo a Mulungu akuti zinthu zidzakhala monga mmene zinalili mu Edeni. Tiyeni tikambilane zitsanzo zina zokhudza kukwanilitsidwa kwa malonjezo amenewo.
9, 10. (a) Kodi ulosi wa pa Yesaya 11:6-9 ukukwanilitsidwa bwanji masiku ano? (b) N’ciani cimaonetsa kuti pakati pa anthu a Mulungu pali mtendele?
9 Citetezo. Mu ulosi wa pa Yesaya 11:6-9, timaŵelenga za mgwilizano ndi mtendele umene udzakhalapo pakati pa nyama za kuchile ndiponso pakati pa anthu ndi ziweto. Kodi ulosi umenewo ukukwanilitsidwa mwakuuzimu masiku ano? Inde ukwanilitsidwa. Pa vesi 9 pakufotokoza cimene cidzapangitsa kuti zolengedwezo zisakavulazane. Vesilo limati: “Cifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.” Kodi ‘kudziŵa Yehova’ kumasintha nyama? Ayi. Koma anthu ndi amene amasintha akadziŵa Mulungu Wam’mwambamwamba ndi kuphunzila kutsatila njila zake za mtendele. M’pake kuti timaona kukwanilitsidwa kocititsa cidwi kwa ulosi umenewo m’paladaiso wa kuuzimu masiku ano. Ulamulilo wa Ufumu wapangitsa kuti otsatila a Kristu asakhale aukali, ndiponso kuti athetse khalidwe lililonse lolingana ndi nyama. Iwo aphunzila kukhala mwamtendele ndiponso mogwilizana ndi abale ndi alongo ao akuuzimu.
10 Mwacitsanzo, m’buku lino tinaphunzila zifukwa za m’Malemba zimene zimapangitsa Akristu kusatenga mbali m’zandale. Tinaphunzilanso za zinzunzo zimene abale athu ambili akumana nazo cifukwa cosatenga nao mbali m’zandale. Kodi sizocititsa cidwi kuti m’dziko lino laciwawa muli “mtundu” wocepa wa anthu amene amakana kucita ciwawa mwa njila iliyonse ngakhale ataopsezedwa kuti adzaphedwa? Umenewu ndi umboni wamphamvu wakuti nzika za Ufumu wa Mesiya zili pa mtendele wofanana ndi umene Yesaya anafotokoza. Yesu anakamba kuti anthu adzadziŵa ophunzila ake cifukwa ca cikondi cimene adzakhala naco pakati pao. (Yoh. 13:34, 35) Kristu kupyolela mwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu akuphunzitsa moleza mtima Akristu oona mumpingo kuti azikhala mwamtendele, azikondana ndi kuti azikomelana mtima.—Mat. 24:45-47.
11, 12. Ndi njala yotani imene ili m’dziko masiku ano? Nanga Yehova akupatsa anthu ake zinthu zambili m’njila yotani?
Amosi 8:11) Kodi nzika za Ufumu wa Mulungu zilinso ndi njala ya kuuzimu? Yehova anafotokoza kusiyana kumene kudzakhalapo pakati pa anthu ake ndi adani ake. Iye anati: “Atumiki anga adzadya, koma inuyo mudzakhala ndi njala. Atumiki anga adzamwa, koma inuyo mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzacita manyazi.” (Yes. 65:13) Kodi mwaona kukwanilitsidwa kwa mau amenewa?
11 Zinthu zoculuka. M’dzikoli muli njala ya kuuzimu. Baibulo linanenelatu kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani, masiku akubwela pamene ndidzatumiza njala m’dziko. Njala imeneyo siidzakhala ya cakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mau a Yehova.” (12 Timalandila cakudya cakuuzimu coculuka monga madzi a mumtsinje umene ukukulilakulila. Mabuku othandiza kuphunzila Baibulo kuphatikizapo zinthu zina zomvetsela monga mavidiyo, misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu, komanso zinthu zina zopezeka pa Webu saiti yathu, zonsezi ndi cakudya cakuuzimu cimene timalandila m’dziko lino limene likuvutika ndi njala ya kuuzimu. (Ezek. 47:1-12; Yow. 3:18) Kodi simukusangalala kuona kuti Yehova akukwanilitsa malonjezo ake mwa kutipatsa zinthu zoculuka masiku ano? Kodi mumayesetsa kudya pathebulo la Yehova nthawi zonse?
13. Kodi akhungu ayamba kuona ndiponso ogontha ayamba kumva m’njila yotani?
13 Umoyo wabwino wa kuuzimu. Masiku ano, anthu ambili ndi akhungu ndiponso ogontha mwakuuzimu. (2 Akor. 4:4) Koma Kristu akucilitsa mwakuuzimu anthu olemala ndi odwala padziko lonse. Kodi munaonapo anthu akhungu amene anayamba kuona ndiponso ogontha amene anayamba kumva? Ngati munaonapo anthu amene anadziŵa coonadi ca Mau a Mulungu molondola ndi kusiya zikhulupililo zabodza zimene zinali kuwapangitsa kuti asaone kapena kumva coonadi, ndiye kuti munaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo lakuti: “M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mau a m’buku. Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.” (Yes. 29:18) Padziko lonse lapansi, anthu masauzande ambilimbili akucilitsidwa mwakuuzimu caka ciliconse. Ndipo umboni wakuti malonjezo a Mulungu akukwanilitsidwa, umaonekela pamene munthu watuluka m’Babulo Wamkulu ndi kuyamba kulambila nafe m’paladaiso wakuuzimu.
14. Ndi umboni uti umene tiyenela kusinkhasinkha kuti tilimbitse cikhulupililo cathu?
14 M’nkhani iliyonse ya m’buku lino muli umboni wamphamvu woonetsa kuti Kristu waloŵetsa otsatila ake m’paladaiso weniweni wakuuzimu m’masiku otsiliza ano. Tiyeni tipitilizebe kuganizila za madalitso ambili amene tikulandila m’paladaiso wa kuuzimu ameneyu. Tikamatelo, cikhulupililo cathu pa zimene Yehova analonjeza kudzacita mtsogolo cidzalimba kwambili.
“Ufumu Wanu Ubwele”
15. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti dzikoli lidzakhala paladaiso?
15 Kuyambila paciyambi, colinga ca Yehova n’cakuti dziko lapansi likhale paladaiso. Iye anaika Adamu ndi Hava m’paladaiso Gen. 1:28) Koma Adamu ndi Hava anagwilizana ndi Satana ndipo anapandukila Mulungu. Zimenezo zinapangitsa kuti ana ao onse akhale opanda ungwilo, ocimwa ndi kuti azifa. Ngakhale n’conco, Mulungu sanasinthe colinga cake. Nthawi zonse mau ake amakwanilitsidwa. (Ŵelengani Yesaya 55:10, 11.) Motelo sitingakaikile kuti mbadwa za Adamu ndi Hava zidzadzaza dziko lapansi ndi kuligonjetsa ndiponso kuti zidzasamalila bwino cilengedwe ca Yehova m’paladaiso padziko lapansi. Panthawiyo, zimene Mulungu analonjeza Ayuda amene anali ku ukapolo zakuti adzakhala ndi umoyo wabwino wofanana ndi wa m’paladaiso zidzakwanilitsidwa kothelatu. Onani zitsanzo izi.
ndi kuwalamula kuti adzaze dziko lapansi ndi ana awo. Anawalamulanso kuti azisamalila zolengedwa zina zonse padzikoli. (16. Kodi Baibulo limafotokoza kuti m’Paladaiso tidzakhala ndi citetezo cotani?
16 Citetezo. Mtsogolomu, mau a pa Yesaya 11:6-9 adzakwanilitsidwa mwakuthupi. Amuna, akazi, ndi ana adzakhala otetezeka kulikonse kumene adzapita padziko lapansi. Sitidzaopa ciliconse kaya ndi munthu kapena nyama. Ganizilani mmene zinthu zidzakhalila pamene kulikonse m’dzikoli kudzakhala monga kunyumba kwanu. Simudzacita mantha kusambila m’mitsinje kapena m’nyanja, simudzaopa kuyenda m’mapili kapena m’chile. Ndipo simudzaopa ciliconse usiku. Mau a pa Ezekieli 34:25 adzakwanilitsidwa moti anthu a Mulungu ‘adzakhala m’cipululu popanda cowaopsa ndipo adzagona m’nkhalango.”
17. Tingatsimikize bwanji kuti Yehova adzatipatsa zinthu zambili zimene tikufunikila pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lonse lapansi?
17 Zinthu zoculuka. Ganizilani za nthawi yomwe sikudzakhala umphawi, matenda obwela cifukwa copelewela zakudya m’thupi, njala, kapena mabungwe othandiza anthu osauka. Cakudya coculuka ca kuuzimu cimene anthu a Mulungu ali naco masiku ano ndi umboni wamphamvu wakuti Mfumu Mesiya idzapeleka cakudya cokwanila kwa nzika zake. Pamene Yesu anali padziko lapansi anapeleka citsanzo cosonyeza kuti adzakwanilitsa malonjezo amenewa. Iye anadyetsa anthu masauzande ambili anjala mwa kugwilitsila nchito mitanda yocepa ya mkate ndi nsomba zoŵelengeka. (Mat. 14:17, 18; 15:34-36; Maliko 8:19, 20) Pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lonse lapansi, maulosi enanso adzakwanilitsidwa monga ulosi wakuti: “Adzabweletsa mvula pambeu zanu zimene munabyala munthaka, ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala cakudya copatsa thanzi. M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetselapo ziweto.”—Yes. 30:23.
18, 19. (a) Kodi ulosi wa pa Yesaya 65:20-22 umakukhudzani bwanji? (b) Kodi masiku athu adzakhala “ngati masiku a mtengo” m’njila yotani?
18 Lelolino, n’kovuta kuti anthu ambili akhale ndi nyumba zabwino, ndiponso kupeza nchito yabwino ndi yopindulitsa. M’dziko loipali, ambili amaona kuti amagwila nchito mwakhama ndiponso kwa nthawi yaitali popanda kulandila malipilo okwanila kuti asamalile mabanja ao. Koma anthu olemela ndiponso adyela ndi amene amapindula. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambili pamene ulosi wa Yesaya udzakwanilitsidwa padzikoli. Ulosiwo umati: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabyala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Yes. 65:20-22.
Sadzabyala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja ao.”—19 Kodi mau akuti masiku athu adzakhala “ngati masiku a mtengo” amatanthauzanji? Mukaima munsi mwa mtengo waukulu, kodi mumamva bwanji mukaganizila zaka zambili zimene mtengowo wakhalapo? N’kutheka kuti wakhalapo zaka zambilimbili agogo anu asanabadwe. N’zodziŵikilatu kuti ngati mukhalabe ndi moyo m’dziko loipali, mtengowo ungakhale zaka zambilimbili mpaka inu kufa ndi kuusiya. Koma n’zosangalatsa kuti mokoma mtima, Yehova walonjeza kuti m’Paladaiso amene akubwela, tidzakhala ndi moyo kwa masiku ambili ndiponso mwamtendele. (Sal. 37:11, 29) Nthawi imeneyo, tidzakhala ndi moyo wosatha ndipo ngakhale mitengo yokhalitsa kwambili tidzaiona monga udzu, umene umamela ndi kutha m’kanthawi kocepa.
20. N’ciani cimene cidzathandiza kuti nzika zokhulupilika za Ufumu zikhale ndi umoyo waungwilo?
20 Thanzi labwino. Masiku ano, aliyense amavutika ndi matenda ndi imfa. Ndipo tonsefe tikudwala matenda aakulu amene ndi uchimo. Mankhwala okha a matendawo ndi nsembe ya dipo ya Kristu. (Aroma 3:23; 6:23) Mu Ulamulilo wa Zaka 1,000, Yesu ndi olamulila anzake adzathandiza anthu kupindula mokwanila ndi nsembe imeneyi. Mwa pang’onopang’ono, io adzagwilitsila nchito nsembeyo kucotsa ucimo wonse mwa anthu okhulupilika. Panthawiyo ulosi wa Yesaya udzakwanilitsidwa kothelatu. Ulosiwo umati: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene macimo ao anakhululukidwa.” (Yes. 33:24) Tangolingalilani! Sikudzakhala munthu wakhungu, wogontha, kapena wolemala. (Ŵelengani Yesaya 35:5, 6.) Yesu adzacilitsa matenda a mtundu uliwonse, kuphatikizapo matenda a maganizo. Nzika zokhulupilika za Ufumu zidzasangalala ndi thanzi labwino.
21. N’ciani cidzacitikila imfa? N’cifukwa ciani mukuona kuti lonjezo limenelo ndi lotonthoza mtima?
21 Nanga bwanji ponena za imfa imene kaŵilikaŵili imabwela cifukwa ca ucimo umene umacitsa kuti tizidwala? Imfa ndi “mdani womalizila,” ndipo palibe munthu wopanda ungwilo amene angaipewe. (1 Akor. 15:26) Koma kodi imfa ndi mdani woopsa ngakhale kwa Yehova? Onani zimene Yesaya analosela ponena za Mulungu: “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Taganizilani mmene zinthu zidzakhalila panthawi imene kudzakhala kulibe malilo, manda, kapena misozi ya cisoni. M’malo mwake anthu adzakhala ndi misozi ya cikondwelelo poona kuti Yehova akukwanilitsa lonjezo lake la kuukitsa anthu akufa. (Ŵelengani Yesaya 26:19) Pomalizila pake, mavuto onse obwela cifukwa ca imfa adzatha.
22. N’ciani cidzacitika Ufumu wa Mesiya ukadzamaliza kucita cifunilo ca Mulungu padziko lapansi?
22 Podzafika kumapeto kwa zaka 1,000, Ufumu wa Mulungu udzakhala utamaliza kucita cifunilo ca Mulungu padziko lapansi. Ndiyeno Kristu adzabwezela ulamulilo kwa Atate wake. (1 Akor. 15:25-28) Panthawiyo, anthu onse adzakhala angwilo ndipo adzakhala okonzeka kukumana ndi ciyeso comaliza pambuyo pakuti Satana wamasulidwa kuphompho. Pomalizila pake, Kristu adzaphwanya njoka yoipayo ndi onse omucilikiza. (Gen. 3:15; Chiv. 20:3, 7-10) Koma anthu onse okonda Yehova ndi mtima wonse adzakhala ndi tsogolo labwino. Mau a m’Baibulo ndi amene amafotokoza bwino mmene zinthu zidzakhalila. Mauwo amakamba kuti anthu onse okhulupilika adzakhala ndi “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
23, 24. (a) N’cifukwa ciani tili ndi cidalilo cakuti malonjezo onse a Mulungu adzakwanilitsidwa? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kucita ciani?
23 Malonjezo amenewo si nkhambakamwa cabe kapena maloto. Zimene Yehova analonjeza zidzacitikadi. N’cifukwa ciani tikutelo? Kumbukilani mau a Yesu amene tinakambilana m’nkhani yoyamba m’buku lino. Iye anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kwa Yehova kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu ndi weniweni osati maganizo a munthu cabe. Panthawi ino ukulamulila kumwamba. Kwa zaka 100 tsopano, Ufumuwo wakhala ukukwanilitsa malonjezo a Yehova m’njila zoonekelatu mumpingo wacikristu. Tili ndi cidalilo cakuti malonjezo onse a Yehova adzakwanilitsidwa kothelatu pamene Ufumu wa Mulungu udzabwela kudzaonetsa mphamvu zake zonse padziko lapansi.
24 Tikudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela. Tikudziŵanso kuti mau onse amene Yehova analonjeza adzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciani tili ndi cidalilo cotele? Cifukwa cakuti UFUMU WA MULUNGU UKULAMULILA. Koma aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi Ufumuwo ukundilamulila ineyo?’ Tiyeni tiyesetse kukhala nzika zokhulupilika za Ufumuwo n’colinga cakuti tipindule kosatha ndi ulamulilo wa Ufumu umene ndi wangwilo ndi wolungama.