Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulamanzele: Wofalitsa wagwidwa ndi wapolisi cifukwa colalikila ku Eindhoven, m’dziko la Netherlands, 1945; Kulamanja: Kodi m’dziko lanu muli malamulo ovomeleza kulalikila?

CIGAWO 4

Zipambano za Ufumu—Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo Uthenga Wabwino

Zipambano za Ufumu—Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo Uthenga Wabwino

YELEKEZANI kuti pamene mukulalikila kunyumba ndi nyumba mukumva kulila kwa alamu ya galimoto ya apolisi. Kulilako kukupitilizabe, ndipo pamene mukuyamba kulankhula kwa mwininyumba, mnzanu amene mukulalikila naye akucita mantha pamene akuona galimoto yapolisi ikufika pafupi. Wapolisi akutsika m’galimotoyo ndi kukufunsani kuti: “Kodi aŵilinu ndinu mwakhala mukuyenda khomo ndi khomo kuuza anthu za Baibulo? Anthu akudandaula za inu.” Mwaulemu, mukumuuza kuti ndinu a Mboni za Yehova. Kodi cidzacitika n’ciani?

Cimene cingacitike cidzadalila pa zimene zakhala zikucitika m’dziko lanu. Kodi boma la m’dziko lanu lakhala likuona bwanji nchito ya Mboni za Yehova m’mbuyomu? Kodi m’dziko lanu muli ufulu wolambila? Ngati muli ufulu wolambila, ndiye kuti abale ndi alongo anu anagwila nchito zolimba pa “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Kaya mumakhala m’dziko liti, kuganizila za milandu imene Mboni za Yehova zapambana kungalimbitse kwambili cikhulupililo canu. M’cigawo cino, tidzaphunzila ina mwa milandu imeneyo. Milandu imene tapambanayo imapeleka umboni wosatsutsika wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni, cifukwa pa ife tokha sitikanapambana milanduyo.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 13

Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti

Masiku ano, oweluza ena ku makhoti akuluakulu amaweluza ngati Gamaliyeli, mphunzitsi wakale wa Cilamulo.

NKHANI 14

Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika

“Mtsinje” wa cizunzo umene Mboni za Yehova zakumana nao cifukwa cokana kutenga mbali m’zandale wamezedwa ndi anthu osayembekezeka.

NKHANI 15

Kumenyela Ufulu wa Kulambila

Anthu a Mulungu akhala akumenyela ufulu wao womvela malamulo a Ufumu wa Mulungu.