Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 14

N’cifukwa Ciani Mulungu Ali ndi Gulu?

N’cifukwa Ciani Mulungu Ali ndi Gulu?

1. N’cifukwa ciani Mulungu analinganiza mtundu wakale wa Isiraeli?

Mulungu analinganiza mbadwa za Abulahamu kukhala mtundu ndi kuwapatsa malamulo. Iye anacha mtunduwo “Isiraeli,” ndi kuupanga kukhala anthu ocilikiza kulambila koona ndi kusunga mau ake. (Salimo 147:19, 20) Mwa ici, anthu a mitundu yonse akanapindula cifukwa ca mtundu wa Isiraeli.​—Ŵelengani Genesis 22:18.

Mulungu anasankha Aisiraeli kukhala mboni zake. Mbili yao yakale imaonetsa mmene anthu anapindulila ndi malamulo a Mulungu. (Deuteronomo 4:6) Conco, kupitila mwa Aisiraeli, anthu ena anadziŵa Mulungu woona.​—Ŵelengani Yesaya 43:10, 12.

2. N’cifukwa ciani Akristu oona ali ndi gulu lolinganizika?

M’kupita kwa nthawi, Yehova sanapitilize kuyanja Aisiraeli, ndipo anasankha mpingo wacikristu m’malo mwa mtundu umenewu. (Mateyu 21:43; 23:37, 38) Masiku ano, Akristu oona ndi amene amatumikila monga Mboni za Yehova popeza Aisiraeli analephela.​—Ŵelengani Machitidwe 15:14, 17.

Yesu anakonzekeletsa otsatila ake kulalikila uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila m’mitundu yonse. (Mateyu 10:7, 11; 24:14; 28:19, 20) M’nthawi ya mapeto a dongosolo lino, nchito imeneyi ikufika pacimake. Kwa nthawi yoyamba m’mbili ya anthu, Yehova wagwilizanitsa anthu mamiliyoni ocokela m’mitundu yonse kupitila m’kulambila koona. (Chivumbulutso 7:9, 10) Akristu oona ali m’gulu logwilizana limene limalimbikitsana ndi kuthandizana. Padziko lonse lapansi, io amalandila malangizo ofanana a m’Baibo pamisonkhano yao.​—Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.

3. Kodi gulu lamakono la mboni za Yehova linayamba bwanji?

Gulu la masiku ano la Mboni za Yehova linayamba ca m’ma 1870. Kagulu kakang’ono ka ophunzila Baibo kanayamba kupezanso coonadi ca m’Baibo cimene cinali citasoŵa kwa nthawi yaitali. Iwo anali atadziŵa kuti Yesu anakonzekeletsa mpingo wacikristu kuti uzilalikila, conco anayamba nchito yolalikila Ufumu padziko lonse lapansi. Mu 1931 anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova.​—Ŵelengani Machitidwe 1:8; 2:1, 4; 5:42.

4. Kodi Mboni za Yehova zili ndi dongosolo lotani?

M’zaka za zana loyamba, mipingo yacikristu m’madela ambili inapindula kwambili ndi zocita za bungwe lolamulila limene linali kuzindikila Yesu monga Mutu wa mpingo. (Machitidwe 16:4, 5) Mofananamo, Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zimapindula ndi utsogoleli wa Bungwe Lolamulila la akulu ofikapo mwauzimu. Bungweli limayang’anila maofesi a nthambi a Mboni za Yehova amene amatembenuza, kusindikiza ndi kufalitsa mabuku ophunzilila Baibo m’zinenelo zopitilila 600. Cifukwa ca zimenezi, Bungwe Lolamulila limakwanitsa kupeleka malangizo a m’Malemba ndi cilimbikitso ku mipingo yoposa 100,000 padziko lonse lapansi. Mumpingo uliwonse, amuna oyenelela amatumikila monga akulu, kapena kuti oyang’anila. Amuna amenewa amasamalila nkhosa za Mulungu mwacikondi.​—Ŵelengani 1 Petulo 5:2, 3.

A mboni za Yehova ndi gulu limene limalalikila uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila. Mofanana ndi atumwi, amalalikila nyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Amadzipeleka pa kuphunzitsa Baibo anthu okonda coonadi. Koma a Mboni za Yehova si gulu cabe. Iwo ndi banja limene lili ndi Tate wao wacikondi. Ndipo io ndi abale ndi alongo amene amasamala za wina ndi mnzake. (2 Atesalonika 1:3) Popeza anthu a Yehova ndi gulu limene limakondweletsa Mulungu ndi kuthandiza anthu ena, io ali banja losangalala kwambili padziko lapansi.​—Ŵelengani Salimo 33:12; Machitidwe 20:35.