Kugwila Nchito ndi Mulungu Kumabweletsa Cimwemwe
“Pamene tikugwila naye nchito limodzi, tikukudandaulilaninso kuti musalandile kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya colinga ca kukoma mtimako.”—2 AKORINTO 6:1.
1. Ngakhale kuti Yehova ndi Mulungu Wamkulu Koposa, kodi wapatsa ena mwai wotani?
YEHOVA ndi wamkulu kuposa wina aliyense. Iye analenga zinthu zonse ndipo ali ndi nzelu ndi mphamvu zopanda malile. Mulungu atathandiza Yobu kumvetsetsa mfundo imeneyi, Yobu anati: “Ndadziŵa kuti inu mumatha kucita zinthu zonse, ndipo palibe zimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Yehova angakwanitse kucita ciliconse cimene wafuna popanda kuthandizidwa ndi wina aliyense. Koma amasonyeza cikondi cake kwa ena mwa kuwapatsa mwai wogwila naye nchito pokwanilitsa colinga cake.
2. Kodi Yehova anapatsa Yesu mwai wogwila naye nchito yotani?
2 Mulungu analenga Mwana wake, Yesu, asanalenge wina aliyense kapena cina ciliconse. Kenako, Yehova anapatsa Mwana wake mwai wogwila naye nchito yolenga zinthu zina zonse. (Yohane 1:1-3, 18) Ponena za Yesu, mtumwi Paulo anati: “Kudzela mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yacifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamulilo. Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzela mwa iye, ndiponso cifukwa ca iye.” (Akolose 1:15-17) Motelo, Yehova analemekeza kwambili Mwana wake mwa kumugwilitsila nchito polenga zinthu ndi kufotokozela ena za udindo wake waukulu.
3. Ndi nchito zotani zimene Yehova anapatsa Adamu? Nanga n’cifukwa ciani?
3 Yehova anapatsanso anthu mwai wogwila naye nchito. Mwacitsanzo, anapatsa Adamu nchito yakuti ache nyama maina. (Genesis 2:19, 20) Adamu ayenela kuti anasangalala kwambili ndi nchito imeneyi. Iye anali kuona mmene nyamazo zinali kuonekela ndi mmene zinali kucitila zinthu. Kenako, anali kupeza dzina loyenelela nyama iliyonse. Yehova ndiye analenga nyama zonse. Cotelo, akanatha kuzipatsa maina. Komabe, anaonetsa cikondi cake kwa Adamu mwa kum’patsa mwai woti ache nyamazo maina. Mulungu anapatsanso Adamu nchito yopanga dziko lonse lapansi kukhala paladaiso. (Genesis 1:27, 28) Koma pambuyo pake, Adamu analeka kugwila nchito ndi Mulungu, ndipo zotsatilapo zake n’zakuti anakumana ndi mavuto amene anakhudza mbadwa zake zonse.—Genesis 3:17-19, 23.
4. Kodi anthu ena anagwila nchito bwanji ndi Mulungu pokwanilitsa cifunilo cake?
4 M’kupita kwa nthawi, Mulungu anapatsanso anthu ena mwai wogwila naye nchito. Mwacitsanzo, Nowa anamanga cingalawa cimene cinam’pulumutsa pamodzi ndi banja lake panthawi ya Cigumula. Mose anamasula Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo. Yoswa anatsogolela Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Solomo anamanga kacisi ku Yerusalemu. Mariya anabeleka Yesu. Anthu okhulupilika amenewa ndiponso ena ambili anagwila nchito ndi Yehova pokwanilitsa cifunilo cake.
5. Kodi tili ndi mwai wogwila nao nchito iti? Kodi Yehova amafunikadi thandizo lathu kuti akwanitse kugwila nchitoyi? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
5 Masiku ano, Yehova watipatsa mwai wocita zonse zimene tingathe kuti ticilikize Ufumu wake. Tingatumikile Mulungu m’njila zosiyanasiyana. Ndipo ngakhale kuti siticita zinthu zofanana potumikila Mulungu, tonsefe tikhoza kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Yehova akanakwanitsa kugwila yekha nchitoyi. Iye akanalankhula ndi anthu mwacindunji kucokela kumwamba. Yesu anakamba kuti Yehova akhoza kupangitsa miyala kulengeza za Ufumu wa Mulungu ndi Mfumu yake. (Luka 19:37-40) Koma Yehova watipatsa mwai wokhala “anchito anzake.” (1 Akorinto 3:9) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene tikugwila naye nchito limodzi, tikukudandaulilaninso kuti musalandile kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya colinga ca kukoma mtimako.” (2 Akorinto 6:1) Ndi mwai wamtengo wapatali kukhala anchito anzake a Mulungu. Tsopano, tiyeni tikambilane mmene kugwila nchito ndi Mulungu kumatithandizila kukhala ndi cimwemwe coculuka.
KUGWILA NCHITO NDI MULUNGU KUMATIPATSA CIMWEMWE
6. Kodi Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu anali kumva bwanji pamene anali kugwila nchito ndi Atate wake?
6 Atumiki a Yehova akamagwila nchito ndi Mulungu amakhala ndi cimwemwe. Asanabwele padziko lapansi, Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu anati: Miyambo 8:22, 30) Pamene Yesu anali kugwila nchito ndi Atate wake, anali wosangalala cifukwa cakuti anacita zinthu zambili ndiponso anali kudziŵa kuti Yehova anali kumukonda. Nanga ifeyo timamva bwanji?
“Yehova anandipanga monga ciyambi ca njila yake . . . Ndinali pambali pake monga mmisili waluso. Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambili ndi ine. Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (7. N’cifukwa ciani nchito yolalikila imatipatsa cimwemwe?
7 Yesu anakamba kuti kupatsa ndiponso kulandila kumabweletsa cimwemwe. (Machitidwe 20:35) Tinasangalala pamene tinaphunzila coonadi, koma timakhalanso osangalala tikamaphunzitsa ena coonadi. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti timawaona akusangalala ndi zimene aphunzila m’Baibulo ndi kuyamba kupanga ubwenzi ndi Mulungu. Timasangalalanso tikaona kuti akusintha maganizo ao ndi umoyo wao. Palibe nchito ina yofunika kwambili ndiponso yosangalatsa imene tingacite kuposa yolalikila. Nchitoyi imathandiza anthu kukhala mabwenzi a Mulungu kuti adzapeze moyo wosatha.—2 Akorinto 5:20.
8. Kodi anthu ena anakamba ciani za cimwemwe cimene amapeza cifukwa cogwila nchito ndi Yehova?
8 Pamene tithandiza anthu kuphunzila za Mulungu, timadziŵa kuti Yehovaakusangalala ndi kuti amayamikila khama lathu pa nchito imene watipatsa. Kudziŵa zimenezi kumatisangalatsa. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Marco, amene amakhala ku Italy anati: “Ndili ndi cimwemwe cacikulu cifukwa codziŵa kuti ndikutumikila Yehova amene sangaiŵale zimene ndakhala ndikucita pomutumikila.” Nayenso Franco amene akutumikila ku Italy anati: “Kudzela m’Mau ake ndi zogaŵila zakuuzimu, nthawi zonse Yehova amatikumbutsa kuti amatikonda ndi kuti amayamikila zimene timacita pom’tumikila, ngakhale kuti nthawi zina tingaone ngati palibe zimene tikucita. N’cifukwa cake kugwila nchito ndi Mulungu kumandisangalatsa. Kumandipangitsanso kuona moyo wanga kukhala wofunika.”
KUGWILA NCHITO NDI MULUNGU KUMALIMBITSA UBWENZI WATHU NDI IYE NDIPONSO ANZATHU
9. Kodi Yehova ndi Yesu anali pa ubwenzi wotani? Nanga n’cifukwa ciani?
9 Tikamagwila nchito pamodzi ndi anthu amene timakonda, timayamba kuwakonda kwambili. Timafika podziŵa kwambili umunthu wao ndi makhalidwe ao. Timadziŵanso zolinga zao ndi zimene akucita kuti akwanilitse zolingazo. N’kutheka kuti Yesu anagwila nchito ndi Yehova kwa zaka mabiliyoni ambili. Iwo anayamba kukondana kwambili moti palibe cimene cikanasokoneza ubwenzi wao. Yesu anasonyeza kuti ubwenzi wake ndi Mulungu ndi wolimba kwambili pamene anati: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yohane 10:30) Iwo analidi ogwilizana, ndipo anagwila nchito mogwilizana kwambili.
Tikamalalikila timalimbitsa cikhulupililo cathu cifukwa cakuti timakumbukila malonjezo a Mulungu ndi mfundo zake zabwino
10. Kodi nchito yolalikila imalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi Mulungu ndiponso anzathu?
10 Panthawi ina, Yesu anapempha Yehova kuti ateteze ophunzila ake. N’cifukwa ciani anatelo? Iye anati: “Kuti akhale amodzi mmene ife tilili.” (Yohane 17:11) Tikamatsatila mfundo za m’Baibulo pa umoyo wathu ndi kugwila nchito yolalikila, timadziŵa bwino makhalidwe a Mulungu apamwamba. Timadziŵa cifukwa cake tiyenela kum’dalila ndi kumvela malangizo ake. Ndipo tikamayandikila Mulungu, nayenso amatiyandikila. (Ŵelengani Yakobo 4:8.) Timalimbitsanso ubwenzi wathu ndi abale ndi alongo athu cifukwa cakuti timapilila mavuto ofanana, timasangalala ndi zinthu zofanana, ndiponso timakhala ndi zolinga zofanana. Timagwila nchito pamodzi, kusangalala pamodzi, ndi kulimbikitsana tikakumana ndi mavuto. Octavia, amene amakhala ku Britain, anati: “Kugwila nchito ndi Yehova kumandithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi ena.” Ndipo anafotokoza kuti zili conco cifukwa cakuti iye ndi mabwenzi ake ali ndi “zolinga zofanana ndiponso tsogolo lofanana.” Inde, ndi mmene tonsefe timamvela. Tikaona abale athu akuyesetsa kucita zinthu zokondweletsa Yehova, timayamba kuwakonda kwambili.
11. N’ciani cidzalimbitsa kwambili ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso ndi anzathu m’dziko latsopano?
11 Masiku ano, tili pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu komanso ndi abale athu, koma ubwenzi umenewu udzakhala wolimba kwambili m’dziko latsopano. Ganizilani za nchito yosangalatsa imene tidzagwila mtsogolo. Tidzalandila anthu amene adzaukitsidwa ndi kuwaphunzitsa za Yehova. Ndiponso tidzagwila nchito yopanga dzikoli kukhala paladaiso. Zidzakhala zosangalatsa kwambili kugwilila nchito pamodzi mu ulamulilo wa Kristu, ndipo m’kupita kwa nthawi, tonse tidzakhala angwilo. Anthu onse adzayamba kukondana kwambili. Iwo adzakhala pa ubwenzi wolimba kwambili ndi Yehova amene ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.’—Salimo 145:16.
KUGWILA NCHITO NDI MULUNGU KUMATITETEZA
12. Kodi nchito yolalikila imatiteteza bwanji?
12 Timafunika kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikukhala m’dziko la Satana ndipo ndife opanda ungwilo. Conco, n’zosavuta kuyamba kutengela maganizo ndi zocita za anthu a m’dzikoli. Zili ngati tikusambila mumtsinje ndipo madzi akutikankhila kumbali imene sitikufuna. Zikakhala conco, timafunika kusambila ndi mphamvu zathu zonse kuti tipite kumene tikufuna. Mofanana ndi zimenezi, tiyenela kucita khama kuti tipewe kutengela mzimu wa dziko la Satana. Kodi nchito yolalikila imatiteteza bwanji? Tikamaphunzitsa ena za Yehova ndi Mau ake, timaika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambili ndiponso zabwino, osati pa zinthu zimene zingafooketse cikhulupililo cathu. (Afilipi 4:8) Tikamalalikila timalimbitsa cikhulupililo cathu cifukwa cakuti timakumbukila malonjezo a Mulungu ndi mfundo zake zabwino. Kulalikila kumatithandizanso kukhalabe ndi makhalidwe abwino amene amatiteteza kwa Satana ndi dziko lake.—Ŵelengani Aefeso 6:14-17.
Ngati timatangwanika ndi nchito ya Yehova, tidzapewa kudela nkhawa za mavuto athu nthawi zonse
13. Kodi m’bale wina wa ku Australia amaiona bwanji nchito yolalikila?
13 Ngati timatangwanika ndi nchito yolalikila, kuphunzila, ndi kuthandiza ena mumpingo, timakhalanso otetezeka cifukwa cakuti sitimangodela nkhawa za mavuto athu. Joel, amene amakhala ku Australia, anati: “Kulalikila kumandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenela. Kumandikumbutsa za mavuto amene anthu akukumana nao ndiponso mapindu amene ndapeza cifukwa cotsatila mfundo za m’Baibulo pa umoyo wanga. Nchito yolalikila imandithandiza kukhala wodzicepetsa. Imandipatsanso mwai wodalila Yehova ndi abale ndi alongo anga.”
14. Kodi kupilila kwathu pa nchito yolalikila kumaonetsa bwanji kuti mzimu wa Mulungu ukutitsogolela?
14 Kulalikila kumatithandiza kukhulupilila kuti mzimu wa Mulungu ukutitsogolela. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti mwapatsidwa nchito yogaŵila anthu buledi m’dela lanu. Simulipilidwa ndipo mumafunika kugwilitsila nchito ndalama zanu kugula zinthu zina zofunika. Kuonjezela apo, anthu ambili saifuna bulediyo, ndipo ena amadana nanu cifukwa cowabweletsela buledi. Kodi mungapitilize kugwila nchito yotelo? Mwacionekele, simungagwile nchitoyo kwa nthawi yaitali, mungafooke n’kuisiya. Mosiyana ndi zimenezi, ambili a ife timapitilizabe kugwila nchito yolalikila caka ciliconse, ngakhale kuti timathela nthawi yathu ndi ndalama zathu panchitoyi. Komanso, timagwilabe nchitoyi ngakhale kuti anthu amatiseka kapena kutikwiila. Zimenezi zimaonetsa kuti mzimu wa Mulungu umatithandiza.
KUGWILA NCHITO NDI MULUNGU KUMAONETSA KUTI TIMAM’KONDA NDIPONSO TIMAKONDA ANZATHU
15. Kodi nchito yolalikila uthenga wabwino imagwilizana bwanji ndi colinga ca Mulungu cokhudza anthu?
15 Kodi nchito yolalikila imagwilizana bwanji ndi colinga ca Yehova cokhudza anthu? Colinga ca Mulungu cinali cakuti Yesaya 55:11) Mulungu anakonza njila yotiombolela ku ucimo ndi imfa. Zimenezi zinatheka pamene Yesu anabwela padziko lapansi ndi kupeleka moyo wake monga nsembe. Koma kuti anthu apindule ndi nsembe imeneyi, afunika kumvela Mulungu. Cotelo, Yesu anaphunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna, ndipo analamula ophunzila ake kuti agwile nchito imeneyi. Masiku ano, tikamalalikila ndi kuthandiza ena kukhala mabwenzi a Mulungu, ndiye kuti tikugwila nchito ndi Mulungu pokwanilitsa colinga cake cakuti aombole anthu ku ucimo ndi imfa.
anthu akhale ndi moyo wosatha, ndipo colinga cimeneci sicinasinthe pamene Adamu anacimwa. (16. Kodi kulalikila kumagwilizana bwanji ndi malamulo aakulu a Mulungu?
16 Tikamathandiza ena kupeza njila ya ku moyo wosatha, timasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso anzathu. “Cifunilo [ca Mulungu] n’cakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Pamene Mfalisi anafunsa Yesu kuti amuuze lamulo lalikulu pa malamulo a Mulungu, Yesu anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba. Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’” (Mateyu 22:37-39) Tikamalalikila uthenga wa ufumu timaonetsa kuti tikumvela malamulo amenewa.—Ŵelengani Machitidwe 10:42.
17. Kodi mumamva bwanji cifukwa ca mwai wolalikila uthenga wabwino?
17 Ndife odala kwambili cifukwa Yehova watipatsa nchito imene imatibweletsela cimwemwe, imatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu ndiponso abale athu, komanso imateteza ubwenzi wathu ndi iye. Imatipatsanso mwai wosonyeza kuti timakonda Mulungu ndi anzathu. Yehova ali ndi atumiki mamiliyoni ambili padziko lapansi, ndipo onse ali ndi umoyo wosiyanasiyana. Komabe, kaya ndife ana, acikulile, olemela, osauka, amphamvu, kapena ofooka, tonse tingathe kuuzako ena zimene timakhulupilila. Timamva ngati Chantel wa ku France amene anati: “Mlengi wa zinthu zonse, Wamphamvuyonse m’cilengedwe, Mulungu wacimwemwe, wandiuza kuti: ‘Pita! Kalalikile! Kalalikile za ine ndi mtima wonse. Ndakupatsa mphamvu, Mau anga Baibulo, thandizo la angelo, anzako padziko, maphunzilo, ndi malangizo a panthawi yake.’ Ndithudi, ndi mwai waukulu kwambili kucita zimene Yehova watilamula ndi kugwila naye nchito.”