Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika

Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika

“Mukhale otsanzila anthu amene mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cao.”—AHEBERI 6:12.

NYIMBO: 86, 54

1, 2. Kodi Yefita ndi mwana wake anakumana ndi zocitika zotani?

MTSIKANA anathamanga kukalandila atate ake. Iye anasangalala kwambili kuwaona akubwela ali bwinobwino kucoka ku nkhondo. Mtsikanayo anayamba kuimba ndi kuvina mwacimwemwe cifukwa cakuti atate ake anapambana nkhondoyo. Koma zimene io anacita ndi kukamba ziyenela kuti zinam’dabwitsa kwambili. Iwo anang’amba zovala zao ndi kulila mofuula kuti: “Kalanga ine mwana wanga! Wandiwelamitsa ndi cisoni.” Ndiyeno, anamuuza kuti io analonjeza kwa Yehova zinthu zimene zidzasinthilatu umoyo wake. Cifukwa ca lonjezo limenelo, mtsikanayo sakanakhala ndi mwai wokwatiwa kapena kukhala ndi ana. Koma mofulumila mtsikanayo anayankha mwanzelu ndipo analimbikitsa atate ake kuti akwanilitse lonjezo lao kwa Yehova. Zimene anayankha zinaonetsa kuti iye anali kudziŵa kuti zilizonse zimene Yehova angam’pemphe kucita, ndi zabwino. (Oweruza 11:34-37) Atatewo anaona kuti mwana wao anali ndi cikhulupililo ndipo anasangalala kwambili cifukwa anadziŵa kuti kudzipeleka kwa mwana wao kudzakondweletsa Yehova.

2 Yefita ndi mwana wake anali kudalila kwambili Yehova ndipo anali kuona kuti kacitidwe kake ka zinthu ndiye koyenela. Iwo anakhalabe okhulupilika ngakhale pa nthawi imene sicinali copepuka kutelo. Anali kufuna kusangalatsa Yehova ndipo anaona kuti kucita zimenezo n’kofunika kwambili kuposa nsembe iliyonse.

3. Kodi citsanzo ca Yefita ndi mwana wake cingatithandize bwanji masiku ano?

3 Nthawi zina kukhala wokhulupilika kwa Yehova kumakhala kovuta. Timafunika “kumenya mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo.” (Yuda 3) Kuti tidziŵe mmene tingacitile zimenezi, tiyeni tiphunzile mmene Yefita ndi mwana wake anapililila mavuto pa umoyo wao. N’ciani cinawathandiza kukhalabe okhulupilika kwa Yehova?

KUKHALA OKHULUPILIKA M’DZIKO LOIPA

4, 5. (a) Kodi Yehova anapeleka lamulo lotani kwa Aisiraeli pamene analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Malinga ndi Masalimo 106, kodi mtundu wa Aisiraeli unakumana ndi mavuto otani cifukwa ca kusamvela?

4 Tsiku lililonse, Yefita ndi mwana wake ayenela kuti anali kukumbukila mavuto amene Aisiraeli anakumana nao cifukwa cosamvela Yehova. Zaka 300 m’mbuyomo, Yehova anali atalamula Aisiraeli kupha anthu onse olambila mafano m’Dziko Lolonjezedwa, koma io sanamvele. (Deuteronomo 7:1-4) Aisiraeli ambili anayamba kutengela zocita za Akanani amene anali kulambila mafano ndi kucita zinthu zina zoipa.—Ŵelengani Salimo 106:34-39.

5 Cifukwa ca kusamvela kwa Aisiraeli, Yehova analeka kuwateteza kwa adani ao. (Oweruza 2:1-3, 11-15; Salimo 106:40-43) Mwacionekele, zinali zovuta kuti mabanja amene anali kukonda Yehova akhalebe okhulupilika kwa Iye m’zaka zovuta zimenezo. Komabe, Baibulo limakamba kuti kunali anthu okhulupilika monga Yefita ndi mwana wake, komanso Elikana, Hana, ndi Samueli. Iwo anali ofunitsitsa kukondweletsa Yehova.—1 Samueli 1:20-28; 2:26.

6. Ndi zinthu ziti zimene anthu m’dzikoli amakonda? Nanga ife tiyenela kucita ciani?

6 Masiku ano, maganizo a anthu m’dzikoli komanso zocita zao, n’zofanana ndi za Akanani. Amakonda kwambili ciwelewele, ciwawa, ndi ndalama. Koma Yehova amaticenjeza mosapita m’mbali. Amacita zimenezi cifukwa amafuna kutiteteza monga mmene anali kucitila kwa Aisiraeli. Kodi tidzatengelapo phunzilo pa zolakwa zao? (1 Akorinto 10:6-11) Tiyenela kucita zilizonse zimene tingathe kuti tipewe kutengela maganizo a dzikoli. (Aroma 12:2) Kodi timayesetsa kutelo?

YEFITA ANAKHALABE WOKHULUPILIKA NGAKHALE KUTI ENA ANAM’KHUMUDWITSA

7. (a) Ndi zinthu ziti zimene anthu a mtundu wa Yefita anam’citila? (b) Nanga iye anacita ciani?

7 M’nthawi ya Yefita, Aisiraeli anali kuvutitsidwa ndi Afilisiti komanso Aamoni cifukwa cakuti sanamvele Yehova. (Oweruza 10:7, 8) Kuonjezela pa adani a Aisiraeli, Yefita anali kukumananso ndi mavuto ocokela kwa abale ake enieni komanso kwa atsogoleli a Aisiraeli. Cifukwa abale ake anali kumuzonda ndi kum’citila nsanje, anam’thamangitsa m’dzikolo kuti asalandile colowa cake monga mwana woyamba kubadwa. (Oweruza 11:1-3) Yefita sanalole kuti zocita zao zankhanza zim’pangitse kukhala munthu woipa. Tidziŵa bwanji zimenezi? Cifukwa cakuti pamene atsogoleli a mtundu wao anam’pempha kuti awathandize, anawathandiza mwamsanga. (Oweruza 11:4-11) N’ciani cinathandiza Yefita kucita zinthu mwa njila imeneyi?

8, 9. (a) Ndi mfundo ziti za m’Cilamulo ca Mose zimene zinathandiza Yefita? (b) N’ciani cimene cinali cofunika kwambili kwa Yefita?

8 Yefita anali mwamuna wamphamvu komanso wolimba mtima, ndipo mbili ya Aisiraeli anali kuidziŵa bwino kuphatikizapo Cilamulo ca Mose. Kuona mmene Yehova anali kucitila zinthu ndi anthu Ake kunam’thandiza kudziŵa zinthu zimene Yehova amakonda ndi zimene amadana nazo. (Oweruza 11:12-27) Iye anali kukumbukila zimenezi nthawi zonse popanga zosankha pa umoyo wake. Anadziŵa kuti Yehova sakonda anthu amene amasungila anzao cakukhosi ndiponso amene amabwezela. Anadziŵanso kuti Mulungu amafuna kuti anthu Ake azikondana. Kuonjezela apo, kudzela m’Cilamulo iye anaphunzila mmene ayenela kucitila zinthu ndi anthu ena, ngakhale amene anali kumuzonda.—Ŵelengani Ekisodo 23:5; Levitiko 19:17, 18.

9 Citsanzo ca Yosefe ciyenela kuti cinam’thandiza kwambili Yefita. Zioneka kuti iye anali kudziŵa mmene Yosefe anasonyezela cifundo kwa abale ake ngakhale kuti anali kumuzonda. (Genesis 37:4; 45:4, 5) Kuganizila citsanzo cimeneci kuyenela kuti kunamuthandiza kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Zimene abale ake anam’citila zinamuŵaŵa kwambili. Koma kuteteza dzina la Yehova ndi anthu ake ndiye cinali cinthu cofunika kwambili kuposa mavuto amene anali kukumana nao. (Oweruza 11:9) Iye anayesetsa kukhala wokhulupilika kwa Yehova. Yehova anadalitsa Yefita ndi Aisiraeli cifukwa ca mmene Yefita anacitila zinthu.—Aheberi 11:32, 33.

Musaleke kutumikila Yehova cifukwa cakuti wina anakukhumudwitsani

10. Kodi tingacite ciani kuti mfundo za m’Baibulo zitithandize kucita zinthu monga Mkristu?

10 Kodi mudzayesetsa kutengela citsanzo ca Yefita? Kodi mudzacita ciani ngati Akristu anzanu akukhumudwitsani kapena ngati muona kuti akucitilani zinthu mopanda cilungamo? Musaleke kutumikila Yehova cifukwa cakuti wina anakukhumudwitsani. Musaleke kupita kumisonkhano kapena kuyanjana ndi mpingo. Tiyeni titengele Yefita ndi kumvela Yehova. Kucita zimenezi kudzatithandiza kupilila zinthu zofooketsa ndi kukhala citsanzo cabwino.—Aroma 12:20, 21; Akolose 3:13.

KUDZIPELEKA KUMAONETSA KUTI TILI NDI CIKHULUPILILO

11, 12. Kodi Yefita analonjeza ciani? Nanga lonjezolo linali kutanthauza ciani?

11 Yefita anadziŵa kuti afunikila thandizo la Yehova kuti akwanitse kulanditsa Aisiraeli kwa Aamoni. Iye analonjeza Yehova kuti ngati adzamuthandiza kupambana nkhondo, adzapeleka “nsembe yopseleza” munthu woyambilila kutuluka m’nyumba yake kudzamulandila pobwela kucoka ku nkhondo. (Oweruza 11:30, 31) Kodi zimenezi zinali kutanthauza ciani?

12 Yehova amanyansidwa ndi kupeleka anthu nsembe. Conco, Yefita sanali kutanthauza kuti adzapeleka munthu monga nsembe yeniyeni. (Deuteronomo 18:9, 10) Malinga ndi Cilamulo ca Mose, nsembe yopseleza inali kupelekedwa kwa Yehova yekha. Conco, Yefita anali kutanthauza kuti munthu amene adzam’peleka kwa Mulungu, adzatumikila Yehova pa cihema kwa moyo wake wonse. Yehova anamva pemphelo lake ndipo anam’thandiza kuti apambane nkhondo. (Oweruza 11:32, 33) Koma kodi Yefita anapeleka ndani kwa Yehova?

13, 14. Kodi mau a Yefita a pa Oweruza 11:35 amaonetsa bwanji cikhulupililo cake?

13 Kumbukilani cocitika cimene takambilana kuciyambi kwa nkhani ino. Pamene Yefita anafika kucoka ku nkhondo, munthu woyamba amene anamulandila anali mwana wake wamkazi wokondedwa. Yefita analibenso mwana wina. Kodi iye anasunga lonjezo lake? Kodi iye anapeleka mwana wake ku cihema kuti akatumikile Yehova kwa moyo wake wonse?

14 Apanso, Yefita anatsatila mfundo za m’Cilamulo ca Mulungu kuti asankhe mwanzelu. Mwina anakumbukila mau amene ali pa Ekisodo 23:19, pamene pamakamba kuti anthu a Yehova ayenela kupeleka kwa Iye zinthu zao zabwino koposa. Cilamulo cinakambanso kuti munthu akalonjeza kwa Yehova, “asalephele kukwanilitsa mau ake. Acite malinga ndi mau onse otuluka pakamwa pake.” (Numeri 30:2) Monga munthu wokhulupilika Hana, amene ayenela kuti analiko panthawiyo, Yefita anasunga lonjezo lake, ngakhale anadziŵa kuti zidzakhala zovuta kwa iye ndi mwana wake. Cifukwa cakuti mtsikanayo anafunika kukatumikila pa cihema, sakanakhala ndi ana. Conco, panalibe munthu amene akanatenga dzina la Yefita kapena kulandila colowa cake. (Oweruza 11:34) Ngakhale n’conco, Yefita anakhalabe wokhulupilika. Iye anati: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mau anga.” (Oweruza 11:35) Yehova analandila nsembe yamtengo wapatali ya Yefita ndipo anam’dalitsa. Inu mukanakhala Yefita, kodi mukanacita ciani?

15. Kodi ndi lonjezo lotani limene ambili a ife tinapanga? Nanga tingaonetse bwanji kuti tikusunga lonjezo lathu?

15 Pamene tinadzipeleka kwa Yehova, tinalonjeza kuti tidzacita cifunilo cake zivute zitani. Tinadziŵa kuti nthawi zina zidzakhala zovuta kusunga lonjezo limeneli. Koma kodi timacita ciani tikapemphedwa kucita zinthu zina zimene ifeyo sitikufuna? Ngati tikhala olimba mtima ndi kumvela Mulungu ndi mtima wonse, ndiye kuti tikusunga lonjezo lathu. Nthawi zina, tingakumane ndi mavuto cifukwa ca kudzipeleka kwathu, koma tikamvela Yehova, iye amatidalitsa kwambili. (Malaki 3:10) Nanga bwanji za mwana wa Yefita? Kodi anacita ciani ndi lonjezo la atate wake?

Tingaonetse bwanji kuti tili ndi cikhulupililo monga ca Yefita ndi mwana wake? (Onani ndime 16 ndi 17)

16. Kodi mwana wa Yefita anacita ciani atamva za lonjezo la atate ake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

16 Lonjezo la Yefita linali losiyana ndi la Hana. Hana analonjeza kuti adzapeleka mwana wake Samueli ku cihema kuti azikatumikila monga Mnazili. (1 Samueli 1:11) Mnazili anali kuloledwa kukwatila komanso kukhala ndi ana. Koma mwana wa Yefita anapelekedwa monga “nsembe yopseleza.” Motelo sanakanakhala ndi mwai wokwatiwa ndi kukhala ndi ana. (Oweruza 11:37-40) Tangoganizilani, iye akanakwatiwa ndi mwamuna wapamwamba m’dzikolo cifukwa atate ake anali mtsogoleli wa Aisiraeli. Koma tsopano Iye anali kudzakhala mtumiki wamba wa pa cihema. Kodi mtsikanayo anacita ciani? Iye anasonyeza kuti anali kuona kutumikila Yehova kukhala cinthu cofunika kuposa ciliconse. Anauza atate ake kuti: “Ndicitileni mogwilizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Oweruza 11:36) Analola kukhala wosakwatiwa ndiponso kusakhala ndi ana kuti atumikile Yehova. Kodi tingatsanzile bwanji mtima wake wodzipeleka?

Mwana wa Yefita analola kukhala wosakwatiwa ndiponso kusakhala ndi ana kuti atumikile Yehova

17. (a) Kodi tingatsanzile bwanji cikhulupililo ca Yefita ndi mwana wake? (b) Kodi mau a pa Aheberi 6:10-12 amakulimbikitsani bwanji kukhala odzipeleka?

17 Abale ndi alongo ambili acinyamata asankha kusaloŵa m’banja kapena kusakhala ndi ana kwa kanthawi. Acita zimenezi cifukwa cakuti afuna kucita zambili potumikila Yehova. Komanso acikulile ambili akugwilitsila nchito nthawi yao ndi mphamvu zao potumikila Yehova. Iwo akanafuna akanagwilitsila nchito nthawi imeneyo kuceza ndi ana komanso adzukulu ao. Ena a io akugwila nchito m’cimango kapena analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, ndipo ena akutumikila kumalo osoŵa. Ena amapanga makonzedwe kuti aonjezele utumiki wao pa nyengo ya Cikumbutso. Yehova sadzaiŵala kudzipeleka kwa anthu okhulupilika amenewa. (Ŵelengani Aheberi 6:10-12.) Nanga bwanji inuyo? Kodi mungadzipeleke kuti mutumikile Yehova mu utumiki wa nthawi zonse?

KODI TAPHUNZILA CIANI?

18, 19. Kodi taphunzila ciani pa nkhani ya Yefita ndi mwana wake? Nanga tingawatsanzile bwanji?

18 N’ciani cinathandiza Yefita kukhala wolimba pamene anali kukumana ndi mavuto ambili? Iye analola kutsogoleledwa ndi Yehova popanga zosankha pa umoyo wake. Sanalole kuti zocita za ena zimufooketse. Anakhalabe wokhulupilika ngakhale pamene ena anam’citila zinthu zoipa. Yehova anadalitsa Yefita ndi mwana wake cifukwa ca kudzipeleka kwao, ndipo anawagwilitsila nchito popititsa patsogolo kulambila koona. Ngakhale pamene ena anayamba kucita zinthu zoipa, Yefita ndi mwana wake anakhalabe okhulupilika kwa Yehova.

19 Baibulo limati: “Mukhale otsanzila anthu amene, mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cao.” (Aheberi 6:12) Tiyeni titsanzile Yefita ndi mwana wake mwa kukhalabe okhulupilika. Tikatelo, Yehova adzatidalitsa.