Kodi Timafunilanji Ciyembekezo?
Kodi Timafunilanji Ciyembekezo?
KODI Daniel, yemwe ankadwala matenda a kansa, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo uja, akanati asatayebe mtima zinthu zikanamuyendela bwanji? Kodi akanachila matenda a kansawo? Kodi bwenzi ali moyobe panopo? Ngakhale anthu ogogomezela kwambili ubwino wa ciyembekezo sanganene kuti akanatelo. Ndipotu pamenepa pagona mfundo yofunika kwambili; mfundo yakuti sitiyenela kukokomeza ubwino wa ciyembekezo. Ciyembekezo si mankhwala ocilitsa vuto lililonse.
Poyankha mafunso omwe a bungwe lofalitsa nkhani la Columbia Broadcasting System anali kumufunsa, Dr. Nathan Cherney anacenjeza kuti kukokomeza ubwino wa ciyembekezo kungathe kupweteketsa odwala amene matenda awapezeketsa kwambili. Iye anati: “Taonapo amuna akunena akazi awo kuti akufulumila kutaya mtima.” Dr. Cherney anapitiliza kuti: “Maganizo ameneŵa acititsa anthu kumaona kuti matenda awo angathe kucepa ngati sakutaya mtima, ndiyeno matendawo akamaipilaipila ena amaganiza kuti ndiye kuti odwalawo akufulumila kutaya mtima, komatu uku n’kulakwa.”
Zoona zake n’zakuti anthu amene akudwala matenda akayakaya amasauka nawo kwambili matendawo. Motelo si bwino kuti pamwamba pa zimenezi, ife owakondafe tiwacititse kuti azidziimba mlandu. Komanso, kodi tingati ciyembekezo cilibe kanthu?
Ayi sitingatelo. Mwacitsanzo, dokotala tam’chula uja, ndi katswili wa cithandizo cosalimbana na nthenda kapena kutalikitsa moyo wa wodwala, koma congothandiza kuti moyo wake ukhale wofeŵelapo panthaŵi yonse yomwe akudwalayo. Madokotala oteleŵa amaona kuti cithandizo cokhazikitsa pansi maganizo a wodwala, ngakhale amene matenda awapezeketsa kwambili, n’cothandiza kwabasi. Pali umboni woculuka wosonyeza kuti ciyembekezo n’cothandiza m’njila imeneyi komanso m’njila zina zambili.
Kuthandiza Kwake kwa Ciyembekezo
Mtolankhani wina amene amalemba nkhani za matenda, dzina lake Dr. W. Gifford-Jones anati: “Ciyembekezo ndi mankhwala amphamvu kwambili.” Iyeyu anaŵelenga akafukufuku osiyanasiyana omwe anacitidwa pofuna kudziŵa ubwino wolimbikitsa anthu amene akudwala mwakayakaya. Akuti zimenezi zimawathandiza kuti asamataye mtima. Atafufuza m’caka ca 1989 anapeza kuti odwala amene anathandizidwa m’njila imeneyi ankakhala na moyo wautaliko, komanso atafufuza posacedwapa sanapeze mfundo iliyonse yotsimikizila zimenezi. Komabe zina zimene akhala akufufuza zatsimikizila kuti odwala amene amalimbikitsidwa savutika maganizo ndiponso samva kuwawa monga odwala ena.
Taganizilaninso za kafukufuku wina wofuna kudziŵa kuti kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzana bwanji ndi matenda a mitsempha ya kumtima. Amuna okwana 1,300 anawaonetsetsa kwa nyengo yaitali kuti adziŵe ngati anali okonda kutaya mtima msanga kapena ayi. Patatha zaka 10 anadzapeza kuti amuna opitilila 12 pa 100 aliwonse pa gululi anadzadwala matenda a mitsempha ya kumtima. Ndipo pa gulu la odwalawo, amuna amene ankataya mtima msanga anali oculuka moŵilikiza poyelekezela na amene sankataya mtima msanga. Laura Kubzansky, yemwe ndi pulofesa wothandizila wa zaumoyo na makhalidwe a anthu ku Harvard School of Public Health anati: “Umboni wambili wotsimikizila kuti ‘kusataya mtima’ kumathandiza pa thanzi la munthu n’ngosatsimikizilika na sayansi. Komano pa kafukufuku amene tacitayu, kwa nthaŵi yoyamba, tapeza umboni weniweni wa sayansi wotsimikizila kuti kusataya mtima n’kothandiza munthu akamadwala matenda a mitsempha ya kumtima.”
Ofufuza ena anapeza kuti anthu amene amadziona kuti alibe thanzi labwino sachila mwamsanga pambuyo powacita opaleshoni kusiyana ndi anthu amene amadziona kuti ali ndi thanzi labwino. Akuti zikuoneka kuti kusataya mtima msanga kumathandizanso kuti munthu akhale ndi moyo wautali. Pa kafukufuku wina anafuna kudziŵa mmene kuona ukalamba ngati cinthu cabwino kapena coipa kumakhudzila anthu acikulile. Anthu ena acikulile atawacititsa kuti aziona mawu ongoonekela kwa kanthaŵi kocepa osonyeza kuti kukalamba kumasonyeza nzelu ndi kukhwima maganizo, acikulilewo anapezeka kuti ayamba kuyenda mwamphamvu. Mphamvu anapezazo n’zofanana ndi zimene akanapeza akanati azicita maseŵela olimbitsa thupi kwa milungu 12!
Kodi n’cifukwa ciani zinthu ngati ciyembekezo, kusataya mtima, ndiponso maganizo abwino zimaoneka kuti zimatipatsa thanzi labwino? N’kutheka kuti asayansi ndiponso madokotala sangatiuze yankho lotsimikizika la funsoli cifukwa samvetsa bwinobwino mmene maganizo ndiponso thupi la munthu limayendela. Komabe akatswili otele, amene amafufuza nkhaniyi angathe kunenapo malingalilo awo monga anthu oti akuidziŵa bwino nkhaniyi. Mwacitsanzo, pulofesa wina wa zaubongo anati n’kutheka kuti n’cifukwa cake: “Timamva bwino m’thupimu tikakhala osangalala ndiponso osataya mtima. Tikamamva conco sitikhala ndi nkhaŵa iliyonse ndipo thupi lathu limasangalala. Cimodzi mwa zinthu zina zimene anthu angacite kuti akhale athanzi n’cimeneci.”
Madokotala, akatswili a maganizo a anthu, ndiponso asayansi ena zimenezi angazione ngati nzelu zatsopano, komatu izi si zatsopano kwa anthu ophunzila Baibo. Kwa zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mfumu yanzelu Solomo inauzilidwa kulemba mawu aŵa: “Mtima wosekelela ucilitsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Onani kuti lembali silikukokomeza nkhaniyi. Silikunena kuti mtima wosekelela ungathe kucilitsa nthenda ina iliyonse koma langoti “ucilitsa bwino.”
Ndipotu, sikungakhale kulakwa kufunsa kuti kodi ciyembekezo cikanakhala kuti ndi mankhwala, alipo dokotala amene akanapanda kulembela odwala ake mankhwalaŵa? Komanso ciyembekezo cimathandiza m’njila ina yofunika kwambili kuposa thanzi cabe.
Mmene Kusataya Mtima Ndiponso Kutaya Mtima Kumakhudzila Moyo Wanu
Ofufuza anapeza kuti anthu osakonda kutaya mtima amapindula kwambili cifukwa ca maganizo otele. Nthaŵi zambili amacita bwino kusukulu, ku nchito ngakhalenso pa zamaseŵela. Mwacitsanzo, anacita kafukufuku pa timu ina ya atsikana yocita maseŵela osiyanasiyana. Makochi a timuyo anafotokoza zonse zokhudza maluso a atsikanawo pa maseŵelawo. Komanso, mtsikana aliyense anam’funsa bwinobwino payekha n’kudziŵa kuti ali ndi ciyembekezo cacikulu motani. Kunapezeka kuti cinthu cothandiza kwambili kuti atsikanawo aziseŵela bwino cinali ciyembekezo cawo osati maluso ena onse amene makochi awo anachula. Kodi n’cifukwa ciani ciyembekezo cimathandiza kwambili conco?
Pali zambili zimene zadziŵika pofufuza zimene zimacitika tikataya mtima. Atafufuza nkhaniyi ca m’ma 1960, anatulukila zodabwitsa pa khalidwe la nyama, zomwe zinacititsa kuti pabwele mawu akuti “kutaya mtima kocita kuphunzila.” Kenaka anapeza kuti anthu angathenso kukhala ndi vutoli. Mwacitsanzo, pofuna kutsimikiza zimenezi anatenga anthu n’kuwaika pa malo aphokoso loboola mkutu atawauza kuti angathe kuzimitsa phokosolo podina mabatani enaake. Anthuwo anakwanitsa kuzimitsa phokosolo.
Gulu lina la anthu linauzidwa kucita cimodzimodzi, komano anthuwo akadina mabataniwo palibe cimene cinkacitika. N’zosadabwitsa kuti ambili pa gululi anafika pongotaya mtima kuti phokosolo silisiya. Kenaka atawayesanso anthuwo anacita mphwayi moti sanayese n’komwe kuzimitsa phokosolo. Iwowo anali ataona kuti palibe ciliconse cimene angacitepo kuti phokosolo lileke. Koma ngakhale m’gulu laciŵilili, anthu osataya mtima sanalefuke maganizo n’kusiya kuyesayesa.
Dr. Martin Seligman, amene anathandiza kukonza njila zofufuzila pa akafukufuku ena oyamba aja anakhudzidwa mtima kwambili ndi zimene anapeza pa nchito yofufuza mmene kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzila anthu moti anaisandutsa nchito yake yeniyeni. Iyeyu anafufuza mosamala za mmene anthu amene ankakonda kudziona ngati olephela amaganizila. Iye anapeza kuti kutaya mtima motele kumasokoneza anthu kucita zinthu zambili m’moyo mwinanso kuwalepheletselatu kucita zinthu bwino-bwino. Ponenapo mwacidule za kutaya mtimaku Seligman anati: “Nditafufuza nkhaniyi kwa zaka 25 ndatsimikiza kuti ngati nthaŵi zambili maganizo athu ali ofanana ndi maganizo a anthu osacedwa kutaya mtima, pomaganiza kuti zinthu zikangolakwika ndiye kuti olakwa ndi ifeyo, komanso kuti zipitililabe kutelo, ndipo kuti zingathe kusokoneza zochita zathu zonse, cimacitika n’cakuti timakumanadi ndi zovuta zambili kusiyana na zimene tikanakumana nazo.”
Kwa ena, izinso zingaoneke ngati zatsopano, komatu si zacilendo kwenikweni kwa anthu ophunzila Baibo. Taonani mwambi uwu: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako icepa.” (Miyambo 24:10) Inde, Baibo limalongosola momveka bwino kuti mukafooka cifukwa ca maganizo, mumalefuka. Ndiyeno kodi mungatani kuti musamataye mtima msanga koma muzikhala ndi ciyembekezo cacikulu?
Ciyembekezo cingakuthandizeni kwambili