ZIMENE BAIBO IMANENA
Kuchova Juga
Anthu ena amaona kuti kuchova juga kulibe vuto lililonse, pomwe ena amaona kuti ni khalidwe loipa.
Kodi kuchova juga kuli na vuto lililonse?
ZIMENE ANTHU AMANENA
Anthu ambili amaona kuti kuchova juga n’kosangalatsa komanso kulibe vuto lililonse ngati malamulo a dzikolo saletsa. Amati kuchova juga kwina, monga malotale, kumathandiza kuti anthu apeze ndalama.
ZIMENE BAIBO IMANENA
M’Baibo mulibe mawu akuti kuchova juga. Komabe mfundo zina za m’Baibo zingatithandize kudziŵa mmene Mulungu amaonela nkhaniyi.
Anthu akamachova juga, amapeza ndalama cifukwa coti anzawo aluza. Zimenezi n’zosemphana na cenjezo la m’Baibo lakuti: “Khalani maso ndipo cenjelani ndi kusilila kwa nsanje kwa mtundu uliwonse.” (Luka 12:15) Munthu wochova juga amafunitsitsa kuti ena aluze, iyeyo apeze phindu. Makampani a malotale akamalengeza za mpikisano, amangochula ndalama zambili zimene munthu angawine cifukwa amadziŵa kuti anthu amafuna kulemela mwamsanga. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu azibecha ndalama zambili m’malo ochovela juga. Komatu makampaniwa satsindika mfundo yoti ngakhale munthu yemwe walowetsa ndalama zambili akhoza kuluza. Conco, m’malo molimbikitsa anthu kupewa mtima wadyela, kuchova juga kumapangitsa anthu kuti azilakalaka atapeza ndalama zambili m’kanthawi kocepa.
Anthu ochova juga amangoganizila phindu limene angapeze. Komatu Baibo imanena kuti munthu “asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Komanso pa Malamulo Khumi aja, lina limanena kuti: “Usalakelake . . . ciliconse ca mnzako.” (Ekisodo 20:17) Munthu wochova juga amaganiza kuti iyeyo ni amene awine n’kutenga ndalama za enawo.
Baibo imaticenjezanso kuti tisamaganize kuti pali mphamvu inayake imene imapangitsa munthu kucita mwayi. Mwacitsanzo, ku Isiraeli wakale, kunali anthu ena omwe anasiya kukhulupilila Yehova ndipo anayamba ‘kuyalila tebulo mulungu wa Mwayi.’ Koma Mulungu sanasangalale na zimenezi ndipo anawauza kuti: “Munapitiliza kucita zinthu zoipa pamaso panga ndipo munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”—Yesaya 65:11, 12.
N’zoona kuti m’mayiko ena, ndalama zomwe makampani amapeza akapangitsa mipikisano ya malotale amazigwilitsa nchito kulipilila anthu sukulu, kukweza cuma ca dziko komanso pa nchito zina zothandiza anthu. Koma zimenezi sizipangitsa kuti kuchova juga kukhale khalidwe labwino cifukwa monga taonela, khalidweli limalimbikitsa mtima wadyela komanso wodzikonda. Ndipo wochova juga amafunitsitsa kuti anzake aluze n’colinga coti iyeyo awine.
“Usalakelake . . . ciliconse ca mnzako.”—Ekisodo 20:17.
Kodi munthu wochova juga amakumana na mavuto otani?
ZIMENE BAIBO IMANENA
Baibo imacenjeza kuti “anthu ofunitsitsa kulemela, amagwela m’mayeselo na mumsampha. Iwo amakodwa na zilakolako zambili zowapweteketsa ndiponso amacita zinthu mopanda nzelu. Zinthu zimenezi zimawawononga na kuwabweletsela mavuto.” (1 Timoteyo 6:9) Dyela kapena umbombo ni zimene zimapangitsa kuti anthu azichova juga. Komatu makhalidwe amenewa ni oipa kwambili moti Baibo imati tiyenela kuwapewa.—Aefeso 5:3.
Popeza anthu ochova juga amapeza ndalama zambili osakhetsa thukuta, khalidweli limalimbikitsa kukonda ndalama. Komatu Baibo imati “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” Kungapangitse munthu kuti azikhala na nkhawa komanso kuti asamakhulupilile Mulungu. Baibo imati anthu okonda ndalama ‘amadzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.’—1 Timoteyo 6:10.
Mtima wadyela umapangitsa kuti munthu asamakhutile na zomwe ali nazo ndipo zimenezi zimacititsa kuti azikhala wosasangalala. Baibo imati: “Munthu wokonda siliva sakhutila ndi siliva, ndipo wokonda cuma sakhutila ndi phindu limene amapeza.”—Mlaliki 5:10.
Anthu ambili akayamba kuchova juga, amazolowela kwambili khalidweli ndipo amalephela kulisiya. Kuchova juga ni vuto lalikulu padziko lonse, ndipo kafukufuku amasonyeza kuti ku United States kokha kuli anthu mamiliyoni ambili omwe amachova juga.
Mwambi wina wa m’Baibo umati: “Colowa copezedwa mwadyela poyamba, tsogolo lake silidzadalitsidwa.” (Miyambo 20:21) Anthu amene anazolowela kwambili kuchova juga moti amalephela kusiya, amakhala na ngongole ndiponso mavuto azacuma. Khalidweli lingacititsenso kuti banja la munthu lithe, acotsedwe nchito komanso kuti adane na anzake. Munthu akamatsatila mfundo za m’Baibo amakhala wosangalala komanso amapewa mavuto amene amabwela cifukwa ca kuchova juga.
“Anthu ofunitsitsa kulemela, amagwela m’mayeselo ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambili zowapweteketsa ndiponso amacita zinthu mopanda nzelu. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweletsela mavuto.”—1 Timoteyo 6:9.