GALAMUKA! Na. 1 2018 | Njila Yopezela Cimwemwe
KODI TINGAPEZE KUTI MALANGIZO OTITHANDIZA KUKHALA NA UMOYO WACIMWEMWE?
Baibo imakamba kuti: “Wodala ndi munthu amene . . . amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku.”—Salimo 1:1, 2.
Nkhani 7 zimenezi, zifotokoza mfundo zimene kwa nthawi yaitali zakhala zothandiza maningi kuti munthu akhale wacimwemwe.
Mmene Mungaipezele
Kodi mumaona kuti ndimwe munthu wacimwemwe? N’ciani cimapangitsa munthu kukhala wacimwemwe?
Kukhutila Komanso Kupatsa
Ambili amaganiza kuti munthu amakhala wacimwemwe akapeza cuma cambili. Kodi kukhala na ndalama komanso katundu wambili kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa? Kodi zocitika zimaonetsa ciani?
Thanzi Labwino na Kupilila
Kodi matenda angapangitse munthu kusoŵa cimwemwe?
Cikondi
Kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili kuti munthu akhale wacimwemwe.
Kukhululuka
Umoyo wokhala wokhumudwa na kusunga cakukhosi, si umoyo wacimwemwe ndipo umaononga thanzi.
Colinga ca Moyo
Kupeza mayankho okhutilitsa pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo kungatithandize kukhala acimwemwe.
Ciyembekezo
Anthu ambili amakhala alibe cimwemwe cifukwa alibe ciyembekezo cotsimikizika cokhudza tsogolo lawo ndi la okondedwa awo.
Dziŵani Zambili Zokhudza Njila Yopezela Cimwemwe
Pali zinthu zambili zimene zingapangitse munthu kukhala wacimwemwe kapena iyayi. Dziŵani zambili zokhudza webusaiti yamahala imene ingakuthandizeni pa mavuto osiyana-siyana amene mumakumana nawo mu umoyo wanu.