Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Colinga ca Moyo

Colinga ca Moyo

ANTHU TINALENGEWA MWAPADELA MANINGI, TIMAKWANITSA KULEMBA, KUPENTA, KUPANGA ZINTHU, NA KUGANIZILA MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO MONGA AKUTI: N’cifukwa ciani zinthu zinalengewa? Zinatheka bwanji kuti tikhaleko? Kodi colinga ca moyo n’ciani? Kodi pali ciyembekezo canji cokhudza tsogolo lathu?

Anthu ena amacita manyazi kufunsa mafunso amenewa. Iwo amaganiza kuti mayankho ake ni ovuta kuŵamvetsa. Ena amakamba kuti mafunso amenewo alibe phindu cifukwa zamoyo zinacita kusandulika kucokela ku zinthu zina. “Kulibe milungu, kulibenso colinga ca moyo. Palibe maziko enieni a makhalidwe abwino, ndiponso moyo ulibe phindu kweni-kweni.” Anakamba conco pulofesa wina wa mbili yakale na zinthu za moyo, dzina lake William Provine.

Koma anthu ena amaona kuti maganizo amenewo ni olakwika. Iwo amaona kuti cilengedwe cimayendela malamulo odalilika, okonzedwa bwino ndi apamwamba. Anthu amenewa amacita cidwi na mmene zinthu za m’cilengedwe zinapangidwila, cakuti ena amapanga zinthu motengela ku cilengedwe. Tsiku na tsiku iwo amaona kapangidwe ka luso ndi kodabwitsa ka zinthu, ndipo zimenezi zimaŵapatsa umboni wakuti amene anapanga zinthu zimenezo ni wanzelu kwambili, osati zakuti zinakhalako zokha.

Kuganizilapo mozama kumeneku kwapangitsa ena amene anali kukhulupilila cisanduliko kusintha maganizo awo. Onani zitsanzo ziŵili zotsatila:

DOKOTA WA ZAMISEMPHA DZINA LAKE, ALEXEI MARNOV ANATI: “Ku masukulu amene n’naphunzila, anali kuphunzitsa kuti kulibe Mulungu ndiponso kuti zinthu zinacita kusandulika kucokela ku zinthu zina. Aliyense wokhulupilila Mulungu anali kumuona kuti ni mbuli.” Koma mu 1990 anayamba kusintha maganizo ake.

Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zonse nimafuna kumvetsetsa kuti zinthu zinakhalako bwanji, kuphatikizapo ubongo wa munthu. Ciwalo cimeneci n’copangiwa mocoloŵana kwambili kuposa cinthu cina ciliconse m’cilengedwe codziŵika kwa anthu. Koma kodi ubongo umenewu unapangiwa kuti uziphunzila zinthu na kudziŵa maluso basi pambuyo pake n’kufa? Kwa ine, izi zinali zosamveka. Conco, n’nayamba kudzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani tili na moyo? Nanga colinga ca moyo n’ciani?’ Pambuyo poganizilapo mozama, n’naona kuti Mlengi aliko.”

Kufuna kudziŵa colinga ca moyo kunacititsa Alexei kuphunzila Baibo. Mkazi wake amene ni dokota, nayenso anali kukhulupilila kuti kulibe Mulungu. Koma pambuyo pake anayamba kuphunzila Baibo. Poyamba anacita izi kuti atsimikize mwamuna wake kuti zimene anayamba kukhulupilila n’zabodza! Lomba onse aŵili amakhulupilila Mulungu maningi, na kumvetsetsa colinga cake cokhudza anthu cofotokozedwa m’Baibo.

WASAYANSI, DR. HUABI YIN, anaphunzila sayansi yokhudza zinthu zosiyana-siyana. Ndipo kwa zaka zambili anali kuphunzila zokhudza dzuŵa. Iye anati: “Pamene ise a sayansi tiphunzila zinthu zodabwitsa za m’cilengedwe, nthawi zonse timaona kuti n’zadongosolo lapamwamba kwambili, cifukwa ca malamulo ake odalilika. N’nadzifunsa kuti, ‘Kodi malamulo amenewa anakhalako bwanji? Ngati moto wophikila cakudya uyenela kuyang’anilidwa bwino kuti usabweletse ngozi, kodi n’ndani amayang’anila kutentha kwa dzuŵa?’ M’kupita kwa nthawi n’naona kuti mau oyamba a m’Baibo, amapeleka yankho lomveka bwino kwambili kuti: ‘Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.’”—Genesis 1:1.

Kukamba zoona, sayansi yayankha mafunso akuti “bwanji,” monga akuti: Kodi maselo a ubongo amaseŵenza bwanji? Kodi dzuŵa limakwanitsa bwanji kutulutsa mphamvu ya kutentha na kuwala? Koma malinga n’zimene Alexei na Huabi anapeza, Baibo imayankha mafunso ofunika kwambili akuti “n’cifukwa ciani,” monga akuti: N’cifukwa ciani zinthu zinalengewa? N’cifukwa ciani zili na malamulo amene amazitsogolela? Nanga n’cifukwa ciani tili na moyo?

Ponena za dziko lapansi, Baibo imakamba kuti: “[Mulungu] sanalilenge popanda colinga, . . . analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Kukamba zoona, Mulungu ali nalo colinga dziko lapansi, ndipo monga mmene nkhani yotsatila idzafotokozela, colinga cimeneco cimagwilizana ndi ciyembekezo cokhudza tsogolo lathu.