Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo

Ziphunzitso Zimene Zimatipatsa Ciyembekezo

Mulungu analonjeza kuti posacedwa adzakonza zinthu padziko lapansi. Iye adzathetsa mavuto onse na kupangitsa kuti anthu adzakhale na umoyo wacimwemwe padzikoli. (Salimo 37:11) N’cifukwa ciani tingalikhulupilile lonjezo limeneli? Cifukwa “Mulungu si munthu woti anganene mabodza.” (Numeri 23:19) Onani zina mwa zinthu zabwino zimene Mlengi wathu adzacita.

Mulungu Adzawononga Anthu Oipa

“Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ocita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatelo kuti awonongeke kwamuyaya.”—SALIMO 92:7.

Monga taonela m’nkhani yapita, zinthu zoipa zikuwonjezeka. Izi sitiyenela kudabwa nazo. Baibo inakambilatu pa 2 Timoteyo 3:1-5 kuti mu “masiku otsiliza” anthu adzaipilatu. Kodi titanthauza ciani tikati masiku otsiliza? Titanthauza masiku otsiliza a anthu oipa amene samvela Mulungu. Posacedwa, Mulungu adzawononga anthu amene amakana kusintha makhalidwe awo oipa. Akadzatelo, anthu abwino okha, amene amamvela Mulungu ndiwo adzakhale padziko lapansi. Malemba amati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Mulungu Adzawononga Satana

“Mulungu amene amapatsa mtendele [adzaphwanya] Satana.”—AROMA 16:20.

Satana, ziŵanda, na anthu oipa akadzacotsedwa, padziko lapansi padzakhala mtendele. Mlengi wathu analonjeza kuti: “Sipadzakhala [wokuwopsani.]”—Mika 4:4.

Mulungu Adzathetsa Matenda na Imfa

“Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.

Kuvutika komanso matenda zidzatha cifukwa Mulungu adzakonza zonse zimene zinawonongeka cifukwa ca Satana, Adamu, Hava, na kupanda ungwilo kwathu. Zotulukapo zake, “imfa sidzakhalaponso.” Anthu amene amakonda Mlengi na kumumvela adzakhala na moyo kwamuyaya. Koma kodi adzakhala kuti?

Mlengi Wathu Adzapanga Dziko Lapansi Kukhala Paradaiso

“Cipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—YESAYA 35:1.

Mulungu akadzawononga anthu oipa, dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Mudzakhala malo ambili okongola, minda yabwino, na cakudya coculuka. (Salimo 72:16) M’nyanja zamcele, m’nyanja zing’ono-zing’ono komanso m’mitsinje mudzakhala madzi aukhondo na zamoyo zambili. Anthu sadzakumbukanso kuti dziko lapansi linali loipa. Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo, ndipo palibe munthu amene adzakhala wosauka, wanjala, kapena wosoŵa pokhala.—Yesaya 65:21, 22.

Mulungu Adzaukitsa Akufa

“Kudzakhala kuuka.”—MACHITIDWE 24:15.

Kodi mumalakalaka kuonananso na okondedwa anu amene anamwalila? Mulungu Wamphamvuzonse adzawaukitsa kuti akhalenso na moyo m’Paradaiso pano padziko lapansi. Akadzaukitsidwa mudzawadziŵa, ndipo nawonso adzakudziŵani. Tangoganizilani cimwemwe cimene imwe na iwo mudzakhala naco! N’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti zimenezi zidzacitika? Cifukwa m’Baibo muli zitsanzo za anthu akulu-akulu komanso ana amene anaukitsidwa, ndipo anakhalanso pamodzi na mabanja awo. Cina, nthawi zambili Yesu anali kuukitsa akufa pamaso pa anthu ambili.—Luka 8:49-56; Yohane 11:11-14, 38-44.