GALAMUKA! Na. 2 2018 | Zinsinsi 12 za Banja Lacimwemwe
Zinsinsi 12 za Mabanja Acimwemwe
Timamva zifukwa zosiyana-siyana zimene zimapangitsa mabanja kupasuka.
M’zaka za pakati pa 1990 ndi 2015, ciŵelengelo ca osudzulana ku America cinawonjezeka kuwilikiza kaŵili kwa anthu a zaka zopitilila 50. Ndipo a zaka zopitilila 65 ciŵelengelo cawo cinawilikiza katatu.
Akatswili ena amalimbikitsa makolo kuti nthawi zonse aziyamikila ana awo. Enanso amakamba kuti azilanga ana awo mwamphamvu na colinga cofuna kuwathandiza. Conco, makolo sadziŵa zimene angacite.
Acicepele amakula, koma osadziŵa maluso ofunikila kuti akhale na umoyo wabwino.
Nanga cimathandiza mabanja ena kukhala acimwemwe n’ciani? Zoona n’zakuti . . .
Ukwati ungakhale wokondweletsa komanso mgwilizano wa moyo wonse.
Makolo angaphunzile kupeleka cilango mwacikondi kwa ana awo.
Acicepele angaphunzile maluso amene angafunikile akadzakula.
Motani? Magazini ino ya Galamuka! idzafotokoza zinsinsi 12 za mabanja acimwemwe.
1: Kukhulupilika
Zinthu zitatu zimene zingathandize okwatilana kukhalabe ogwilizana.
2: Kugwilizana
Kodi mnzanu wa m’cikwati mumamuona monga munthu wokhala naye nyumba imodzi cabe?
3: Kulemekezana
Dziŵani zofunika kukamba komanso kucita kuti mnzanu wa m’cikwati azidzimva wolemekezedwa.
4: Kukhululukilana
Kodi mungacite ciani kuti musamasumike kwambili maganizo anu pa zimene mnzanu wa m’cikwati amalakwitsa?
5: Kukambilana
Masitepu atatu amene angakuthandizeni kukhala pa ubwenzi wolimba ndi ana anu.
6: Cilango
Kodi kupeleka cilango kwa mwana kumam’pangitsa kudziona wosafunika?
7: Makhalidwe
Kodi muyenela kuphunzitsa ana anu mfundo zabwanji?
8: Citsanzo
Ngati mufuna kuti mau anu aziwafika pamtima ana anu, mufunika kucita zinthu mogwilizana na zimene mumakamba.
9: Umunthu Wanu
Kodi acicepele angakhalile bwanji kumbuyo zimene amakhulupilila?
10: Kudalilika
Kudalilidwa na makolo ni sitepu yofunika kuti mukhale wokhwima m’maganizo.
11: Kukhala Wolimbika
Kuphunzila kugwila nchito molimbika muli wacicepele kungakuthandizeni pa zilizonse zimene mucita mu umoyo.
12: Zolinga
Kukwanilitsa zolinga kungakuthandizeni kukhala na cidalilo, kulimbitsa maubwenzi anu, ndiponso kuonjezela cimwemwe canu.
12: Zolinga
Kukwanilitsa zolinga kungakuthandizeni kukhala na cidalilo, kulimbitsa maubwenzi anu, ndiponso kuonjezela cimwemwe canu.