Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumvela makolo anu kuli monga kubweza loni imene munatenga ku banki. Nthawi zonse pamene mubweza loni yanu, m’pamenenso amakudalilani kwambili

KWA ACICEPELE

10: Kudalilika

10: Kudalilika

ZIMENE KUMATANTHAUZA

Anthu odalilika amadalilidwa na makolo awo, anzawo, komanso mabwana awo ku nchito. Iwo amatsatila malamulo, kukwanilitsa malonjezo awo, ndipo nthawi zonse amakamba zoona.

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA

Nthawi zambili, munthu amapatsidwa ufulu woculuka ngati waonetsa kukhulupilika kwa nthawi yokwanila.

“Kuti makolo anu azikudalilani, njila yabwino ni kucita zinthu zoonetsa kuti ndimwe munthu wokhwima m’maganizo komanso wodalilika. Mungacite zimenezi osati cabe pamene makolo anu alipo koma olo pamene iwo palibe.”—Sarahi.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Pitilizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.

ZIMENE MUNGACITE

Ngati mufuna kuti anthu azikudalilani kwambili kapena ngati mufuna kuti anthu amene amakukayikilani ayambenso kukudalilani, mungacite zotsatilazi.

Khalani oona mtima. Ngati simukamba zoona, mwamsanga anthu adzaleka kukudalilani. Koma ngati ndimwe oona mtima ndipo simubisa zimene mwalakwitsa, anthu adzakudalilani.

“N’zosavuta kukhala oona mtima ngati zonse ziyenda bwino. Koma kukhala oona mtima pa zinthu zimene zingakuonetseni monga kuti ndimwe wolakwa, ndiye kumapangitsa kuti anthu akudalileni kwambili.”—Caiman.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

Khalani wokhulupilika. Kafuku-fuku wina amene anacitika ku America, anaonetsa kuti 78 pelesenti ya akulu-akulu olemba anthu nchito m’makampani, anakamba kuti kukhulupilika ni “cimodzi mwa zinthu zitatu zofunika kwambili kuti munthu aloŵe nchito.” Kuphunzila kukhala wokhulupilika tsopano, kudzakupindulitsani mukadzakula.

“Makolo anga amaona kuti ndine wodalilika pamene nigwila nchito za pakhomo popanda kukumbutsidwa nthawi na nthawi. Nthawi zonse pamene nicita izi, m’pamenenso amanidalila kwambili.”—Sarah.

MFUNDO YA M’BAIBO: ‘Nikhulupilila kuti ucita zimenezi. Ndikudziwa kuti ucita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.’—Filimoni 21.

Khalani oleza mtima. Kukula mwakuthupi monga kutalika kapena kuina, kumaonekela mosavuta kwa ena. Koma n’kosiyana na kukhwima m’maganizo cifukwa kumatenga nthawi yaitali kuti kuonekele kwa ena.

“Kuti makolo anu na anthu ena azikudalilani, zimatenga nthawi komanso zimafuna khama. Koma ngati nthawi zonse mumacita zinthu mokhulupilika, pang’ono-pang’ono iwo adzayamba kukudalilani.”—Brandon.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Valani . . . kuleza mtima.”—Akolose 3:12.