Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukambilana kuli monga biliji, kumakugwilizanitsani ndi ana anu

KWA MAKOLO

5: Kukambilana

5: Kukambilana

ZIMENE KUMATANTHAUZA

Kukambilana moona mtima kumakhala kotheka ngati imwe makolo na ana anu, mukambilana momasuka malingalilo anu na mmene mumvelela.

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA

Kukambilana ndi acicepele kumakhala kovuta, maka-maka azaka pakati pa 13 ndi 19. “Ana akakhala aang’ono amamasuka kuuza makolo awo zonse za kumtima. Koma akasinkhuka, samakamba zambili na makolo awo. Conco, makolo amalephela kudziŵa maganizo a ana awo ndi mmene amvelela.” Limakamba zimenezi buku lakuti, Breaking the Code. Ngakhale pamene ana anu aoneka monga safuna kukamba, imeneyo ndiye nthawi imene amafuna kwambili kukambilana!

ZIMENE MUNGACITE

Khalani wokonzeka kukambilana na mwana wanu nthawi iliyonse imene wafuna. Citani zimenezo olo kuti izi zingaphatikizepo makambilano a usiku kwambili.

“Mwina mungaganize zokamba kuti, ‘Lomba ndiye pamene ufuna kukamba na ine, koma mzuŵa monse tinali tonse!’ Kodi tifunika kudandaula ngati ana athu afuna kukamba na ise? Kodi izi si zimene kholo lililonse limafuna?”—Lisa.

“Nimakonda kugona mwamsanga, koma makambilano ena abwino amene nakhalapo nawo ndi ana anga acicepele, anacitika capakati pausiku.”—Herbert.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.

Pewani zotangwanitsa. Mwamuna wina amene ni kholo anavomeleza kuti: “Nthawi zina nimapezeka kuti niganizila zinthu zina pamene ana anga akamba na ine. Ndipo iwo amazindikila zimenezo!”

Ngati mumatangwanika na zinthu monga TV kapena foni, mungacite bwino kuzimya TV na kuika foni pambali. Ndiyeno, ikani maganizo anu pa zimene mwana wanu akamba, pofuna kuonetsa kuti mukuziona kukhala zofunika, olo kuti zioneke monga n’zosafunika.

“Ana athu afunika kuona kuti zimene amatiuza timaziona kukhala zofunika. Koma ngati amaona kuti timawanyalanyalaza, angaleke kutiuza zinthu ndipo angapeze wina womuululila zakukhosi.”—Maranda.

“Musakalipe, olo kuti zimene mwana wanu aganiza n’zolakwika.”—Anthony.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Muzimvetsela mwachelu kwambili.”—Luka 8:18.

Seŵenzetsani mpata ulionse. Nthawi zina ana amamasuka kufotokoza za kukhosi pamene acitila zinthu pamodzi na makolo awo, osati kucita kukonza nthawi yokambilana nawo.

“Timapezelapo mwayi woceza ndi ana athu tikhala paulendo m’motoka. Kukambilana nawo pa nthawi ngati imeneyi, kwatithandiza kuti tizikambilana momasuka.”—Nicole.

Nthawi ya cakudya imapelekanso mpata wabwino wokambilana momasuka.

“Panthawi ya cakudya ca m’madzulo, aliyense wa ise amafotokoza cinthu cimodzi cokondweletsa ndi cina cosakondweletsa cimene cacitika pa tsikulo. Cizoloŵezi cimeneci cimatigwilizanitsa na kutikumbutsa kuti ena adzatithandiza tikakumana na mavuto.”—Robin.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Aliyense akhale wofulumila kumva [ndi] wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.