KWA OKWATILANA
1: Kukhulupilika
ZIMENE KUMATANTHAUZA
Amuna na akazi amene ni okhulupilika m’banja mwawo amaona kuti cikwati ni mgwilizano wa moyo wawo wonse. Izi zimapangitsa kuti azidalilana. Aliyense amakhala na cidalilo cakuti olo pakhale mavuto, mnzawo wa m’cikwati sadzawasiya.
Anthu ena amakhala m’cikwati cabe cifukwa cokakamizidwa na acibululu awo kapena anzawo. Koma cifukwa cabwino kwambili cokwalila m’cikwati ciyenela kukhala cakuti aŵiliwo amakondana na kulemekezana.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Mwamunanso asasiye mkazi wake.”—1 Akorinto 7:11.
“Ngati ndiwe wokhulupilika m’cikwati, umalolela kulakwilidwa. Umakhala wokonzeka kukhululuka komanso kupepesa ukalakwitsa. Suona mavuto monga mwayi wothetsela cikwati.”—Micah.
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA
Ngati mwamuna na mkazi ni osakhulupilika m’banja, akakumana na mavuto, amathamangila kukamba mau monga akuti, ‘Sindise oyenelelana’ ndipo amafuna-funa njila zothetsela cikwati.
“Ambili amaloŵa m’cikwati ali na ‘maganizo’ akuti zinthu zikadzavuta, adzasudzulana cabe. Ngati anthu aloŵa m’cikwati na maganizo aconco, ndiye kuti kungoyambila pa ciyambi, cikwati cawo cimakhala cosalimba.”—Jean.
ZIMENE MUNGACITE
DZIFUFUZENI
Muli mkati mokangana . . .
-
Kodi mumayamba kuganiza kuti munasankha mwamuna kapena mkazi wosayenelela?
-
Kodi mumaganizila zokwatilana na munthu wina?
-
Kodi mumakamba mau monga akuti, “Nidzakusiya ine” kapena “Nidzapeza wina amene anganikonde”?
Ngati mwayankha kuti inde pa imodzi mwa mafunso aya kapena kuposapo, lomba ni nthawi yakuti mulimbitse cikwati canu.
KAMBILANANI NA MNZANU WA M’CIKWATI
-
Kodi kukhulupililana ndi kudalilana m’cikwati canu zayamba kucepekela? Ngati n’conco, n’cifukwa ciani?
-
Kodi mungacite zinthu ziti kuti mulimbitse mgwilizano m’cikwati canu?
MUNGACITENSO IZI
-
Muzimulembelako ka uthenga ka cikondi mnzanu wa m’cikwati
-
Onetsani kukhulupilika kwanu mwa kuika masinapu ya mnzanu wa m’cikwati pa malo oonekela ku nchito
-
Muzitumilako foni mnzanu wa m’cikwati nthawi zonse mukakhala kunchito kapena pamene muli kwina
MFUNDO YA M’BAIBO: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse”—Mateyu 19:6.