Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza

Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza

Masiku ano, zimaoneka monga kuti asayansi anaphunzila za ciliconse m’cilengedwe. Komabe, pali mafunso ambili ofunika amene iwo sangakwanitse kuyankha.

Kodi asayansi amadziŵa mmene cilengedwe kuphatikizapo moyo zinayambila? Yankho lacidule n’lakuti ayi. Anthu ena amakamba kuti akatswili a sayansi ya zacilengedwe, angathe kufotokoza mmene cilengedwe cinayambila. Komabe, pulofesa wa maphunzilo a zakuthambo, dzina lake Marcelo Gleiser, wa pa Koleji ya Dartmouth, amenenso amakayikila za kukhalapo kwa Mulungu anati: “Sitinakwanitse kufotokoza mmene cilengedwe cinayambila.”

Mofananamo, pofotokoza za ciyambi ca moyo, nkhani ina m’magazini yochedwa Science News inati: “N’zovuta kudziŵa mmene moyo unayambila padziko lapansi. Zili conco cifukwa mathanthwe na zinthu zina zakale zimene zikanatithandiza kudziŵa zomwe zinacitika dziko litangokhalako kumene, zinatha kale-kale.” Mawu amenewa aonetsa kuti asayansi sanapeze yankho pa funso lakuti, Kodi cilengedwe conse kuphatikizapo moyo zinayamba bwanji?

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Ngati zamoyo pano padziko lapansi zinacita kupangidwa, ndani anazipanga?’ Mwinanso munaganizilapo mafunso monga awa: ‘Ngati kulidi Mlengi wanzelu komanso wacikondi, n’cifukwa ciani amalola kuti anthufe tizivutika? N’cifukwa ciani amalola kuti pakhale zipembedzo zambili zosiyanasiyana? Nanga n’cifukwa ciani amalola anthu amene amati amamulambila kucita zinthu zambili zoipa?’

Sayansi singakwanitse kuyankha mafunso amenewa. Koma izi sizitanthauza kuti simungapeze mayankho okhutilitsa. Anthu ambili apeza mayankho okhutilitsa m’Baibo.

Ngati mufuna kudziŵa cifukwa cake asayansi ena amene anaphunzila Baibo amakhulupilila kuti kuli Mlengi, pitani pa jw.org. Pamenepo, fufuzani mawu akuti “ndemanga zokhudza ciyambi ca moyo.