Cifukwa Cake Kudziŵa Ngati Mlengi Aliko N’kofunika
N’cifukwa ciani kudziŵa ngati Mlengi aliko n’kofunika? Cifukwa ngati mwakhutila na umboni wakuti kuli Mulungu wamphamvuzonse, mungafune kupenda umboni wakuti Baibo ni youzilidwa na iye. Ndipo mukakhulupilila zimene Baibo imakamba, mudzapindula m’njila izi:
Mudzakhala na umoyo wacimwemwe
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “[Mulungu] anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzaza mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.”—Machitidwe 14:17.
TANTHAUZO LAKE: Ciliconse ca m’cilengedwe cimene mumasangalala naco ni mphatso yocokela kwa Mlengi. Mudzayamikila kwambili mphatso zimenezi mukadziŵa kuti amene anakupatsani amakukondani kwambili.
Mudzapeza malangizo othandiza pa umoyo
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “Ukacita zimenezi udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njila yonse ya zinthu zabwino.”—Miyambo 2:9.
TANTHAUZO LAKE: Popeza Mulungu ni Mlengi wathu, amadziŵa zimene timafunikila kuti tikhale acimwemwe. Mukamaŵelenga Baibo, mudzapeza mfundo zambili zimene zingakuthandizeni pa umoyo wanu.
Mudzapeza mayankho pa mafunso anu
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “Udzamudziwadi Mulungu.”—Miyambo 2:5.
TANTHAUZO LAKE: Mukadziŵa kuti Mlengi alipo, mudzapeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili monga akuti: Kodi colinga ca moyo n’ciani? N’cifukwa ciani padzikoli pali mavuto ambili? Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila? Mungapeze mayankho okhutilitsa pa mafunso amenewa m’Baibo.
Mudzakhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova.’”—Yeremiya 29:11.
TANTHAUZO LAKE: Mulungu analonjeza kuti m’tsogolo adzathetsa zoipa, mavuto, ngakhale imfa. Mukakhulupilila malonjezo a Mulungu, mudzakhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino cimene cidzakuthandizani kukhalabe wolimba mtima pamene mwakumana na mavuto.