Zimene Cilengedwe Cimatiuza
Mpaka pano, akatswili oona za kuthambo amagoma naco cilengedwe. Ndipo akupitiliza kupanga zida zapamwamba zowathandiza kupenda zam’cilengedwe. Kodi atulukilako zotani?
Zam’cilengedwe zinalinganizidwa mwadongosolo. Nkhani yopezeka m’magazini yochedwa Astronomy inati:“Milalang’amba siyomwazikana mwacisawawa mu mlengalenga, koma ni yolinganizika mwadongosolo.” Kodi izi zimatheka bwanji? Asayansi amakhulupilila kuti cisinsi cake cagona pa zinthu zinazake zosaoneka zam’cilengedwe. Zinthu zosaoneka zimenezi n’zimene zimagwila komanso kucilikiza magulu osiyanasiyana a milalang’amba kuthambo.
Kodi zinatheka bwanji kuti zam’cilengedwe zikhale zolinganizika bwino conco? Kodi zingakhale zoona kuti dongosolo limeneli linangokhalako lokha? Onani zimene anakamba malemu Allan Sandage. Iye amadziŵika kuti anali “mmodzi wa akatswili a sayansi ya zakuthambo otsogola kwambili a m’zaka za m’ma 1900,” ndipo anali kukhulupilila kuti kuli Mulungu.
Iye anati: “Niona kuti sizingatheke kuti zinthu zolinganizika mwadongosolo zimenezi zikhaleko zokha. Payenela kukhala cinacake cimene cinazilinganiza.”
Cilengedwe cinalinganizidwa bwino kuti cizicilikiza moyo. Ganizilani mphamvu imene asayansi amaicha mphamvu yocepa. Mphamvu imeneyi imapangitsa kuti dzuŵa liziyaka pa mlingo woyenela. Mphamvuyi ikanacepako pang’ono, sembe dzuŵa silinapangike. Ngati mphamvuyi ikanaculukilapo pang’ono, dzuŵa likanayaka kwambili, ndipo likananyeka kale-kale.
Mphamvu yocepa ni cimodzi mwa zinthu zolinganizidwa bwino kwambili zimene zimapangitsa kuti moyo ukhalepo. Mlembi wa zasayansi, dzina lake Anil Ananthaswamy anati ngakhale cimodzi cabe mwa zinthuzo cikanakhala cosalinganizika bwino, “nyenyezi, mapulaneti, komanso milalang’amba sizikanakhalako. Moyo nawonso sukanakhalapo.”
M’cilengedwe muli malo abwino okhalapo anthu. Dziko lapansi lili na cifungadziko cabwino, madzi okwanila, komanso mwezi wa saizi yabwino, umene umapangitsa kuti dziko lizikhazikika pa malo ake. Magazini yakuti National Geographic inati: “Pa mwala wodabwitsa umenewu [dziko lapansi] pali zinthu zamoyo na zopanda moyo zimene n’zogwilizana bwino ndipo zimadalilana, moti pulaneti imeneyi ndiyo malo okha oyenelela amene tidziŵa oti anthu n’kukhalapo.” a
Malinga na zimene mlembi wina analemba, “dzuŵa na mapulaneti amene amalizungulila zili kutali na nyenyezi zina” mu mlalang’amba wathu. Koma kutalikilana kumeneko n’kumene kumapangitsa kuti zikhale zotheka moyo kukhalapo padziko. Tikanakhala kufupi na nyenyezi zina, kaya pakatikati pa mlalang’amba wathuwu kapena m’mbali mwake, padzikoli sipakanakhala camoyo cifukwa ca kutentha kosaneneka. M’malomwake, dziko lili pa malo amene asayansi amati ni “malo okhawo mu mlalang’amba pamene pangakhale zamoyo.”
Malinga na zimene anaphunzila zokhudza cilengedwe komanso malamulo ake, katswili wa sayansi Paul Davies anati: “Sinikhulupilila kuti kukhalapo kwathu m’cilengedweci kunangocitika mwangozi kapena mosayembekezeleka. . . . Niona kuti tinapangidwa na colinga.” Davies saphunzitsa kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zam’cilengedwe, kuphatikizapo anthufe. Koma kodi muganiza bwanji? Zinthu zonse zam’cilengedwe, kuphatikizapo dziko lapansi zimaoneka kuti zinapangidwa m’njila yakuti moyo ukhalepo. Kodi n’kutheka kuti zimaoneka conco cifukwa zinapangidwa na winawake?
a Nkhani imeneyi ya m’magazini ya National Geographic sinanene izi pofuna kuonetsa kuti Mulungu ndiye analenga dziko na anthu. M’malomwake, inali kungothilila ndemanga mfundo yakuti dziko lapansi ni malo abwino okhalapo anthu.