Zimene Zamoyo Zimatiuza
Kulikonse padzikoli, timaona zamoyo zikukula, kuyenda, na kubelekana. Zamoyo zimenezi zimapangitsa pulaneti lathuli kukhala lokongola kwambili. Kuposa kale lonse, anthu masiku ano amadziŵa zambili zokhudza zamoyo. Kodi zamoyo zimatiuza ciani ponena za mmene moyo unayambila? Ganizilani izi.
Zamoyo zimaoneka kuti zinacita kupangidwa. Zamoyo ni zopangidwa na tunthu tung’ono-tung’ono tochedwa maselo. Maselo ali ngati tumafakitale tung’ono-tung’ono. Amacita zinthu zambili zogometsa zimene zimathandiza kuti zamoyo zipitilize kukhala na moyo, komanso kuti zizibelekana. Umu ni mmene zamoyo zonse zilili. Mwacitsanzo, ganizilani za yisiti, imene ni twamoyo twa selo limodzi. Poyelekeza na selo la munthu, selo la yisiti limaoneka ngati losacoloŵana kweni-kweni. Koma limacita zinthu zogometsa kwambili. Pakati pake pamakhala DNA, imene imapeleka malangizo a zimene selo liyenela kucita. Mu selo lililonse mumakhala tunthu tung’ono-tung’ono tumene tumasankha, kutumiza, na kusintha makemiko kukhala cakudya, cimene n’cofunika kuti selo likhalebe na moyo. Selo la yisiti likasoŵa cakudya, limaleka kugwila nchito n’kukhala ngati lagona. Ici n’cifukwa cake yisiti imatha kukhala nthawi yaitali m’khichini monga yopanda moyo, koma munthu akaiseŵenzetsa kuti aphikile zinthu, imayamba kugwila nchito.
Kwa zaka zambili, asayansi akhala akuphunzila za maselo a yisiti kuti amvetsetse mmene maselo a munthu amagwilila nchito. Koma pakali zambili zimene samvetsetsa. Pulofesa Ross King, wa pa Chalmers University of Technology ku Sweden anati: “Palibe asayansi okwanila amene angapime zonse zimene tifuna kuti timvetsetse ngakhale mmene selo la yisiti limagwilila nchito.”
Kodi muganiza bwanji? Kodi zinthu zogometsa zimene zimacitika m’selo la yisiti ni umboni wakuti linacita
kupangidwa? Kapena zimenezi zinangocitika zokha popanda winawake wozipanga?Moyo umacokela ku zinthu zamoyo kale. DNA ni yopangidwa na msakanizo wa makemiko ochedwa ma nucleotide. Selo lililonse la munthu limakhala na ma nucleotide 3.2 biliyoni. Makemiko amenewa amakhala olumikizidwa mwadongosolo, kuti azipatsa maselo malangizo a mopangila ma enzaimu na mapuloteni.
Asayansi amakamba kuti, kuti DNA ipangike payokha ngakhale imodzi cabe, ma nucleotide angafunike kulumikizana maulendo mathililiyoni ambili-mbili. Zimenezi n’zokayikitsa kwambili kuti zingacitike, moti zioneka kuti n’zosatheka.
Mfundo ni yakuti asayansi sanapangeko camoyo ciliconse kucokela ku zinthu zopanda moyo.
Anthu anapangidwa mwapadela. Anthufe tinapangidwa m’njila yakuti tizikondwela mokwanila na umoyo kuposa zamoyo zina zonse. Tili na maluso apadela opanga zinthu, kugwilizana na anthu ena, komanso kuonetsa mmene timvelela. Ife anthu timatha kudziŵa na kusiyanitsa makomedwe a zinthu, fungo, mamvekedwe, mitundu, na maonekedwe ake. Timakonzekela zakutsogolo ndiponso timafuna kudziŵa colinga ca moyo.
Muganiza bwanji? Kodi maluso amenewa anangobwela okha mwa ife cifukwa anali ofunikila kuti tikhalebe na moyo komanso kuti tizibelekana? Kapena amaonetsa kuti moyo ni mphatso yocokela kwa Mlengi wacikondi?